Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?
Kodi mukuona kuti zinthu m’dzikoli . . .
-
zikhalabe mmene zililimu?
-
ziipa kuposa pamenepa?
-
kapena zikhala bwino?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Mulungu . . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4, Baibulo la Dziko Latsopano.
KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?
Mudzakhala ndi moyo wosangalatsa komanso ntchito yabwino.—Yesaya 65:21-23.
Simudzadwala kapena kuvutika m’njira iliyonse.—Yesaya 25:8; 33:24.
Mudzakhala wosangalala ndi banja lanu komanso mabwenzi anu mpaka kalekale.—Salimo 37:11, 29.
KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?
Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:
-
Mulungu ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezo limeneli. M’Baibulo ndi Yehova Mulungu yekha amene amatchedwa “Wamphamvuyonse” chifukwa ali ndi mphamvu zopanda malire. (Chivumbulutso 15:3) Choncho adzakwaniritsa lonjezo lake losintha dzikoli kuti likhale labwino. Ndipotu Baibulo limanena kuti “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”—Mateyu 19:26.
-
Mulungu akufunitsitsa kukwaniritsa lonjezo lake. Mwachitsanzo, Yehova ‘akulakalaka’ kuukitsa anthu amene anamwalira. —Yobu 14:14, 15.
Baibulo limasonyezanso kuti Mwana wa Mulungu, Yesu, ankachiritsa odwala. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Chifukwa ankafunitsitsa kuwathandiza. (Maliko 1:40, 41) Yesu anatsanzira ndendende Atate wake pa nkhani yofunitsitsa kuthandiza anthu ovutika.—Yohane 14:9.
Choncho sitingakayikire kuti Yehova ndi Yesu ndi ofunitsitsa kutithandiza kuti tidzakhale osangalala m’tsogolomu.—Salimo 72:12-14; 145:16; 2 Petulo 3:9.
GANIZIRANI MFUNDO IYI
Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti asinthe dzikoli kukhala labwino?
Baibulo limayankha funso limeneli pa MATEYU 6:9, 10 ndi pa DANIELI 2:44.