Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 16:1-24

  • Kutolera zopereka zopita kwa Akhristu a ku Yerusalemu (1-4)

  • Maulendo amene Paulo ankafuna kuyenda (5-9)

  • Ulendo wa Timoteyo ndiponso wa Apolo (10-12)

  • Malangizo ndiponso kupereka moni (13-24)

16  Pa nkhani ya zopereka zopita kwa oyerawo,+ mukhoza kutsatira malangizo amene ndinapereka ku mipingo ya ku Galatiya. 2  Tsiku loyamba la mlungu uliwonse, aliyense aziika kenakake pambali kunyumba kwake mogwirizana ndi zimene angakwanitse, kuti zopereka zisadzaperekedwe nditafika. 3  Koma ndikadzafika kumeneko, ndidzatuma amuna amene mungawavomereze mʼmakalata,+ kuti adzapititse mphatso yanu yachifundoyo ku Yerusalemu. 4  Komabe ngati pangafunike kuti inenso ndidzapite nawo, tidzapitira limodzi. 5  Ndidzabwera kumeneko pochokera ku Makedoniya, chifukwa ndidzadutsira ku Makedoniya.+ 6  Ndidzakhala nanu kumeneko, mwinanso nthawi yonse yozizira, kuti mudzandiperekeze kumene ndizidzapitako. 7  Sindikufuna kukuonani panopa mongodutsa chabe, koma ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kanthawi ndithu,+ Yehova* akalola. 8  Koma ndikhalabe kuno ku Efeso+ mpaka pa Chikondwerero cha Pentekosite, 9  chifukwa khomo* lalikulu la utumiki landitsegukira,+ koma pali otsutsa ambiri. 10  Timoteyo+ akadzafika mudzaonetsetse kuti asadzakhale ndi mantha pakati panu, chifukwa iye akugwira ntchito ya Yehova,*+ ngati mmene inenso ndikuchitira. 11  Choncho pasadzapezeke munthu womuderera. Mudzamuperekeze mwamtendere kuti adzabwere kunoko, chifukwa ineyo ndikumuyembekezera pamodzi ndi abale. 12  Ponena za mʼbale wathu Apolo,+ ndinamuchonderera kwambiri kuti abwere kwanuko pamodzi ndi abale. Sichinali cholinga chake kuti abwere panopa, koma adzabwera akadzapeza mpata. 13  Khalani maso,+ khalani ndi chikhulupiriro cholimba,+ khalani olimba mtima*+ ndipo khalani amphamvu.+ 14  Zonse zimene mukuchita, muzizichita mwachikondi.+ 15  Abale, mukudziwa kuti anthu a mʼbanja la Sitefana ndi amene anali oyamba kukhala okhulupirira* ku Akaya ndipo anadzipereka kutumikira oyera. Choncho ndikukulimbikitsani kuti, 16  inunso pitirizani kukhala ogonjera kwa anthu ngati amenewo, ndi kwa aliyense amene akugwira nawo ntchitoyi mwakhama.+ 17  Koma ndikusangalala kuti Sitefana,+ Fotunato ndi Akayiko ndili nawo kuno, chifukwa alowa mʼmalo mwanu. 18  Anthu amenewa andilimbikitsa kwambiri ineyo komanso alimbikitsa inuyo. Choncho anthu otere muziwalemekeza. 19  Mipingo ya ku Asia ikupereka moni. Akula ndi Purisika komanso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo,+ akupereka moni wochokera pansi pa mtima kwa nonsenu, mwa Ambuye. 20  Abale onse akukupatsani moni. Mupatsane moni mwachikondi. 21  Tsopano landirani moni wanga, wa ineyo Paulo, wolemba ndekha ndi dzanja langa. 22  Aliyense amene sakonda Ambuye, atembereredwe. Bwerani Ambuye wathu! 23  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu kukhale nanu. 24  Ndikukutsimikizirani inu nonse amene ndinu ophunzira a Khristu Yesu kuti ndimakukondani.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mwayi.”
Kapena kuti, “pitirizani kuchita chamuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zipatso zoyambirira.”