1 Mbiri 15:1-29
15 Davide anapitiriza kumanga nyumba zake mu Mzinda wa Davide ndipo anakonza malo oikapo Likasa la Mulungu woona, nʼkulimangira tenti.+
2 Pa nthawi imeneyi mʼpamene Davide ananena kuti: “Alevi okha ndi amene ayenera kunyamula Likasa la Mulungu woona, chifukwa Yehova anasankha iwowa kuti azinyamula Likasa la Yehova ndiponso azimutumikira nthawi zonse.”+
3 Ndiyeno Davide anasonkhanitsa Aisiraeli onse ku Yerusalemu kuti akanyamule Likasa la Yehova, kupita nalo kumalo amene iye anakonza kuti akaliike.+
4 Kenako Davide anasonkhanitsa mbadwa za Aroni+ ndi Alevi.+
5 Kuchokera ku banja la Kohati, panali Uriyeli mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 120.
6 Kuchokera ku banja la Merari, panali Asaya+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 220.
7 Kuchokera ku banja la Gerisomu, panali Yoweli+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 130.
8 Kuchokera pa mbadwa za Elizafana,+ panali Semaya mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 200.
9 Kuchokera pa mbadwa za Heburoni, panali Elieli mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 80.
10 Kuchokera pa mbadwa za Uziyeli,+ panali Aminadabu mtsogoleri wawo ndi abale ake okwana 112.
11 Komanso Davide anaitanitsa Zadoki+ ndi Abiyatara,+ omwe anali ansembe. Anaitanitsanso Alevi awa: Uriyeli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu.
12 Ndiyeno anawauza kuti: “Inuyo ndinu atsogoleri a nyumba za makolo a Alevi. Choncho inu ndi abale anu mudziyeretse ndipo mukatenge Likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli nʼkukaliika kumalo amene ndakonza kuti lizikhalako.
13 Chifukwa chakuti ulendo woyamba uja si inuyo amene munalinyamula,+ Yehova Mulungu wathu anatikwiyira koopsa,+ popeza sitinatsatire malangizo ake.”+
14 Choncho ansembe ndi Alevi anadziyeretsa kuti akatenge Likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli.
15 Ndiyeno Alevi anakanyamula Likasa la Mulungu woona pamapewa awo pogwiritsa ntchito ndodo,+ mogwirizana ndi zimene Mose anawalamula potsatira mawu a Yehova.
16 Kenako Davide anauza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo oimba kuti aimbe mosangalala komanso agwiritse ntchito zipangizo zoimbira. Zipangizozo zinali zoimbira za zingwe, azeze+ ndi zinganga.+
17 Choncho Aleviwo anasankha Hemani+ mwana wa Yoweli. Pa abale ake, anasankhapo Asafu+ mwana wa Berekiya ndipo pa abale awo a kubanja la Merari, anasankhapo Etani+ mwana wa Kusaya.
18 Anasankhanso abale awo a gulu lachiwiri.+ Abale awowo anali Zekariya, Beni, Yaazieli, Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya ndiponso Obedi-edomu ndi Yeyeli, alonda apageti.
19 Hemani,+ Asafu+ ndi Etani anawasankha kuti aziimba ndi zinganga zakopa.*+
20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Maaseya ndi Benaya ankaimba ndi zoimbira za zingwe zochunidwa kuti ziziimba Alamoti.*+
21 Matitiya,+ Elifelehu, Mikineya, Obedi-edomu, Yeyeli ndi Azaziya ankaimba azeze ochunidwa kuti aziimba Seminiti*+ ndipo ndi amene ankatsogolera.
22 Kenaniya,+ mtsogoleri wa Alevi, ndi amene ankayangʼanira ntchito yonyamula katundu chifukwa anali katswiri pa ntchitoyi.
23 Berekiya ndi Elikana anali alonda apageti panyumba yomwe munkakhala Likasa.
24 Sebaniya, Yosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezere, omwe anali ansembe, ankaimba malipenga mokweza patsogolo pa Likasa la Mulungu woona.+ Obedi-edomu ndi Yehiya nawonso anali alonda apageti panyumba yomwe munkakhala Likasa.
25 Davide ndi akulu a Isiraeli ndiponso atsogoleri a anthu 1,000 ankayenda mosangalala+ limodzi ndi likasa la pangano la Yehova kuchokera kunyumba kwa Obedi-edomu.+
26 Mulungu woona atathandiza Alevi omwe ananyamula likasa la pangano la Yehova, iwo anapereka nsembe ngʼombe zazingʼono zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.+
27 Davide, Alevi onse onyamula Likasa, oimba ndiponso Kenaniya amene ankayangʼanira oimba komanso ntchito yonyamula Likasa, anavala mikanjo yodula manja, yansalu yabwino kwambiri. Koma Davide anavalanso efodi wansalu.+
28 Aisiraeli onse ankapita limodzi ndi likasa la pangano la Yehova akufuula mokondwera+ ndiponso akuliza nyanga za nkhosa ndi malipenga.+ Iwo ankaimbanso mokweza zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze.+
29 Koma likasa la pangano la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide,+ Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kusangalala. Ndiyeno Mikala anayamba kumunyoza mumtima mwake.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “zamkuwa.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.