2 Samueli 7:1-29
7 Mfumu inkakhala mʼnyumba yake*+ ndipo Yehova anachititsa kuti izikhala mwamtendere komanso isamavutitsidwe ndi adani ake onse.
2 Ndiyeno mfumuyo inauza mneneri Natani+ kuti: “Ine ndikukhala mʼnyumba ya mitengo ya mkungudza,+ pamene Likasa la Mulungu woona likukhala mutenti.”+
3 Natani anauza mfumu kuti: “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukufuna, chifukwa Yehova ali nanu.”+
4 Usiku wa tsiku lomwelo, Yehova analankhula ndi Natani kuti:
5 “Pita ukauze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwe uyenera kundimangira nyumba yoti ine ndikhalemo?+
6 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Aisiraeli mu Iguputo mpaka lero,+ sindinakhalepo mʼnyumba koma nthawi zonse ndinkayendayenda ndili mutenti.+
7 Pa nthawi yonse imene ndinkayenda ndi Aisiraeli,* kodi ndinayamba ndafunsapo atsogoleri a mafuko a Isiraeli amene ndinawasankha kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’
8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+
9 Ine ndidzakhala nawe kulikonse kumene ungapite,+ ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzachititsa kuti dzina lako lidziwike+ ngati mmene zimakhalira ndi anthu otchuka mʼdzikoli.
10 Anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo nʼkuwakhazika pamalowo. Iwo adzakhala pamenepo ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu oipa sadzawaponderezanso ngati mmene ankachitira kale,+
11 pa nthawi imene ndinasankha oweruza+ kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli. Ndidzachititsa kuti uzikhala mwamtendere osavutitsidwa ndi adani ako.+
Komanso Yehova wakuuza kuti, Yehova adzakukhazikitsira nyumba.*+
12 Ukadzamwalira+ nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mwana wako weniweni, akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+
13 Iye ndi amene adzamangire dzina langa nyumba,+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+
14 Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Akalakwitsa zinthu zina, ine ndidzamudzudzula ndi ndodo ya anthu ndi zikoti za ana a anthu.*+
15 Ndipo chikondi changa chokhulupirika sichidzachoka pa iye ngati mmene ndinachichotsera pa Sauli,+ amene ndinamʼchotsa pamaso pako.
16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhalapobe mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+
17 Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+
18 Kenako Mfumu Davide anakhala pansi pamaso pa Yehova ndipo anati: “Ndine ndani ine, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? Ndipo banja lathu* nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano?+
19 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, kuwonjezeranso pamenepa, mwanena kuti nyumba ya mtumiki wanu idzakhazikika mpaka mʼtsogolo kwambiri. Amenewa ndi malangizo* amene mwapereka kwa anthu onse, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.
20 Ndiyeno ine mtumiki wanu Davide ndinganenenso chiyani kwa inu pomwe mukundidziwa bwino kwambiri,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa?
21 Inu mwachita zazikulu zonsezi chifukwa cha mawu anu komanso mogwirizana ndi zimene zili mumtima mwanu* ndipo mwandidziwitsa ine mtumiki wanu.+
22 Nʼchifukwa chake ndinudi wodabwitsa,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Palibe amene angafanane ndi inu+ komanso palibe Mulungu wina koma inu nokha.+ Zonse zimene tamva zikutsimikizira zimenezi.
23 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli?+ Inu Mulungu munapita kukawawombola anthu anu+ ndipo munadzipangira dzina+ pamene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha.+ Munathamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo chifukwa cha anthu anu amene munawawombola ku Iguputo.
24 Munachititsa Aisiraeli kuti akhale anthu anu mpaka kalekale.+ Ndipo inu Yehova mwakhala Mulungu wawo.+
25 Choncho inu Yehova Mulungu, chitani zimene mwalonjeza zokhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake ndipo muchite zimenezi mpaka kalekale. Muchite mogwirizana ndi zimene mwalonjeza.+
26 Dzina lanu likwezeke mpaka kalekale+ kuti anthu anene kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi Mulungu wa Isiraeli,’ ndipo nyumba ya ine mtumiki wanu Davide ikhazikike pamaso panu.+
27 Chifukwa inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, mwandiululira ine mtumiki wanu kuti, ‘Ndidzakumangira nyumba.’*+ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera kwa inu pempheroli.
28 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu Mulungu woona ndipo mawu anu ndi oona,+ komanso mwandilonjeza ine mtumiki wanu zinthu zabwinozi.
29 Choncho dalitsani nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa mwalonjeza ndipo madalitso anu akhale panyumba ya mtumiki wanu mpaka kalekale.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mʼnyumba yake yachifumu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
^ Kapena kuti, “mzere wa mafumu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mabaibulo ena amati “ana a Adamu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba yanga.”
^ Kapena kuti, “malamulo.”
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi cholinga chanu.”
^ Kapena kuti, “mzere wa mafumu.”