Ekisodo 25:1-40
25 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:
2 “Uza Aisiraeli kuti apereke zopereka kwa ine. Ulandire zopereka zanga kwa munthu aliyense amene akufunitsitsa kupereka.+
3 Zopereka zimene ukuyenera kulandira kwa iwo ndi izi: golide,+ siliva,+ kopa,*+
4 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo,* ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi ubweya wa mbuzi.
5 Ulandirenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,+
6 mafuta a nyale,+ basamu wopangira mafuta odzozera+ ndi zofukiza zonunkhira.+
7 Komanso ulandire miyala ya onekisi ndi miyala ina yoika pa efodi+ ndiponso pachovala pachifuwa.+
8 Mundipangire malo opatulika, ndipo ndidzakhala pakati panu.+
9 Mukapange chihema chopatulika ndi ziwiya zake zonse mogwirizana ndendende ndi zimene ndikukusonyeza.+
10 Mupange likasa* la mtengo wa mthethe, masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+
11 Kenako mulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe mulikute ndi golide, ndipo mupange mkombero wagolide kuzungulira likasalo.+
12 Mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo.
13 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide.+
14 Mulowetse ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.
15 Ndodo zonyamulirazo zizidzakhala mumphete za Likasalo. Sizikuyenera kuchotsedwamo.+
16 Mkati mwa Likasamo udzaikemo Umboni umene ndidzakupatse.+
17 Mudzapange chivundikiro chagolide woyenga bwino, masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+
18 Mupangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo muwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+
19 Kerubi mmodzi akhale kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina akhale kumbali inayo.
20 Akerubiwo atambasule mapiko awo nʼkuwakweza mʼmwamba ndipo aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Iwo akhale moyangʼanizana, koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro.
21 Chivundikirocho+ udzachiike pa Likasalo, ndipo mu Likasamo udzaikemo Umboni umene ndidzakupatse.
22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho.+ Ndidzakuuza malamulo onse oti ukauze Aisiraeli kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni.
23 Mupangenso tebulo+ la mtengo wa mthethe, masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+
24 Mudzalikute ndi golide woyenga bwino, ndipo mudzapange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.
25 Mupange felemu kuzungulira tebulo lonse, muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo mupangenso mkombero wagolide pafelemulo.
26 Tebulolo mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika mʼmakona ake 4 mmene muli miyendo yake 4.
27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo.
28 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo muzikute ndi golide. Ndodo zimenezi azinyamulira tebulolo.
29 Mupangenso mbale zake, makapu, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Muzipange ndi golide woyenga bwino.+
30 Ndipo patebulopo muziikapo mkate wachionetsero pamaso panga nthawi zonse.+
31 Kenako mupange choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Choikapo nyalecho chikhale chinthu chimodzi chosula ndipo chikhale ndi tsinde, thunthu, nthambi, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+
32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6. Kumbali ina kukhale nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kukhalenso nthambi zitatu.
33 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse ikhale ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse ikhalenso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho zikhale zotero.
34 Pathunthu la choikapo nyalecho pakhale timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa.
35 Mphindi imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale.
36 Choikapo nyale chonsecho, kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake, chikhale chimodzi ndipo chisulidwe ndi golide woyenga bwino.+
37 Muchipangire nyale 7 ndipo nyalezo zikayatsidwa ziziunikira malo amene ali patsogolo pake.+
38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+
39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.*
40 Uonetsetse kuti wazipanga motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Kapena kuti, “ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wapepo.”
^ Katumbu ndi nyama yaubweya yamʼmadzi, ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka mʼnyanja zikuluzikulu.
^ Kapena kuti, “bokosi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri ndi hafu.” Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.