Levitiko 19:1-37

  • Malamulo osiyanasiyana okhudza kukhala oyera (1-37)

    • Kakololedwe koyenera (9, 10)

    • Kuchita zinthu moganizira anthu avuto losaona ndi losamva (14)

    • Miseche (16)

    • Musamasunge chakukhosi (18)

    • Analetsa kuchita zamatsenga ndi zamizimu (26,31)

    • Analetsa kudzichekacheka (28)

    • Kulemekeza achikulire (32)

    • Zoyenera kuchita ndi alendo (33, 34)

19  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2  “Uza gulu lonse la Aisiraeli kuti, ‘Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.+ 3  Aliyense wa inu azilemekeza* mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 4  Musatsatire milungu yopanda pake+ kapena kudzipangira milungu yachitsulo chosungunula.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5  Mukamapereka nsembe yamgwirizano kwa Yehova,+ muziipereka mʼnjira yakuti Mulungu asangalale nanu.+ 6  Muzidya nyama yoperekedwa nsembeyo pa tsiku limene mwaipereka ndiponso tsiku lotsatira, koma yotsala mpaka tsiku lachitatu muziiwotcha pamoto.+ 7  Ngati munthu wadya nyamayo pa tsiku lachitatu, wadya nyama yonyansa. Mulungu sadzalandira nsembe imeneyo. 8  Munthu amene wadya nyamayo aziyankha mlandu wa kulakwa kwakeko chifukwa waipitsa chinthu chopatulika cha Yehova. Munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 9  Mukamakolola zinthu zamʼmunda mwanu, musamachotseretu zonse mʼmphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha* mʼmunda mwanumo.+ 10  Komanso, musamakolole mphesa zotsala zamʼmunda mwanu kapena kutola mphesa zimene zamwazika mʼmunda mwanu. Zimenezo muzisiyira anthu osauka*+ ndi mlendo wokhala pakati panu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 11  Musamabe,+ musamapusitse anzanu+ ndiponso musamachitirane chinyengo. 12  Musamalumbire zabodza mʼdzina langa+ nʼkuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. 13  Musamabere anzanu mwachinyengo+ ndipo musamalande zinthu za aliyense.+ Malipiro a munthu waganyu asagone mʼnyumba mwanu mpaka mʼmawa.+ 14  Musamatemberere* munthu amene ali ndi vuto losamva ndipo munthu amene ali ndi vuto losaona musamamuikire chinthu chopunthwitsa.+ Muziopa Mulungu wanu.+ Ine ndine Yehova. 15  Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka kapena munthu wolemera.+ Ndipo muziweruza mwachilungamo. 16  Usamayendeyende pakati pa anthu a mtundu wako nʼkumafalitsa miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.*+ Ine ndine Yehova. 17  Usamadane ndi mʼbale wako mumtima mwako,+ koma uzimudzudzula+ kuti iwenso usakhale wochimwa ngati iyeyo. 18  Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu a mtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova. 19  Malamulo angawa muziwasunga: Musamachititse kuti ziweto zanu zamitundu yosiyana zikwerane. Podzala mbewu mʼmunda mwanu musamasakanize mitundu iwiri yosiyana.+ Ndipo musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.*+ 20  Mwamuna akagona ndi kapolo wamkazi amene mbuye wake anamulonjeza kuti adzamupereka kwa mwamuna wina, koma mkaziyo sanawomboledwe kapena kupatsidwa ufulu, pazikhala chilango. Koma iwo asaphedwe chifukwa mkaziyo anali asanakhale mfulu. 21  Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula pakhomo la chihema chokumanako.+ 22  Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Azichita zimenezi popereka kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula ija ndipo munthuyo adzakhululukidwa tchimo lakelo. 23  Mukafika mʼdziko limene mukupita nʼkudzala mtengo uliwonse wa zipatso, zipatso zake zizikhala zodetsedwa kwa inu ndipo mtengowo musamauyandikire. Musamayandikire mtengowo kwa zaka zitatu ndipo musamadye zipatso zake. 24  Koma mʼchaka cha 4, zipatso zake zonse zizikhala zoyera ndipo muzizipereka kwa Yehova mosangalala.+ 25  Ndiyeno mʼchaka cha 5, mungathe kukolola zipatso zake mofanana ndi mbewu zina zonse komanso kudya zipatso za mtengowo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 26  Musamadye chilichonse chimene chili ndi magazi.+ Musamaombeze kapena kuchita zamatsenga.+ 27  Musamamete ndevu zanu zotsikira mʼmasaya kapena kudula nsonga za ndevu zanu.*+ 28  Musamadzicheke chifukwa cha munthu wakufa,+ ndipo musamadzilembe zizindikiro pakhungu lanu. Ine ndine Yehova. 29  Musamanyoze mwana wanu wamkazi pomupangitsa kuti akhale hule,+ kuopera kuti dziko lingachite uhule nʼkudzaza ndi makhalidwe otayirira.+ 30  Muzisunga masabata anga+ ndipo muzilemekeza* malo anga opatulika. Ine ndine Yehova. 31  Musamapemphe anthu olankhula ndi mizimu+ kuti akuthandizeni ndipo musamafunse malangizo kwa anthu olosera zamʼtsogolo+ nʼkukuchititsani kukhala odetsedwa. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 32  Anthu aimvi uziwagwadira,+ munthu wachikulire uzimupatsa ulemu+ ndipo uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova. 33  Ngati munthu akukhala mʼdziko lanu monga mlendo, musamamuchitire zoipa.+ 34  Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa.+ Muzimukonda ngati mmene mumadzikondera nokha, chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 35  Musamachite chinyengo poyeza kutalika kwa chinthu, kulemera kwa chinthu kapena poyeza kuchuluka kwa zinthu.+ 36  Muzikhala ndi masikelo olondola, miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu ndi miyezo yolondola.*+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo. 37  Muzisunga malamulo anga onse ndi zigamulo zanga zonse, ndipo muzizitsatira.+ Ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “aziopa.”
Kapena kuti, “musamatenge zotsala.”
Kapena kuti, “ovutika.”
Kapena kuti, “Musamafunire zoipa.”
Mabaibulo ena amati, “Usamangoyangʼana pamene moyo wa mʼbale wako uli pangozi.”
Kutanthauza chovala chimene nsalu yake anaiwomba mophatikiza ulusi wathonje ndi ubweya wankhosa. Onani De 22:11.
Apa akuwaletsa kuchita zimene anthu akunja ankachita, koma sakutanthauza kuti asamayepule ndevu zawo ngakhale pangʼono.
Mʼchilankhulo choyambirira, “muziopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Muzikhala ndi muyezo wolondola wa efa komanso muyezo wolondola wa hini.” Muyezo wa efa ankaugwiritsa ntchito poyeza zinthu zouma ngati tirigu, koma muyezo wa hini ankaugwiritsa ntchito poyeza zinthu zamadzi. Onani Zakumapeto B14.