Wolembedwa ndi Luka 11:1-54
11 Tsopano Yesu ankapemphera pamalo enaake. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera ngati mmene Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
2 Ndiyeno iye anawauza kuti: “Mukamapemphera muzinena kuti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.*+ Ufumu wanu ubwere.+
3 Mutipatse chakudya chalero mogwirizana ndi chakudya chofunika pa tsikuli.+
4 Ndipo mutikhululukire machimo athu,+ chifukwa nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.*+ Komanso tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa.’”*+
5 Kenako anawauza kuti: “Tiyerekeze kuti mmodzi wa inu ali ndi mnzake ndipo wapita kwa mnzakeyo pakati pa usiku kukamupempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate,
6 chifukwa mnzanga winawake wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe choti ndimupatse.’
7 Koma mnzake ali mʼnyumbayo nʼkuyankha kuti: ‘Usandivutitse ine. Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingathe kudzuka kuti ndikupatse kanthu.’
8 Ndithu ndikukuuzani, adzadzuka nʼkumupatsa chilichonse chimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi mnzake, koma chifukwa chakuti wakakamira kwambiri.+
9 Choncho ndikukuuzani, pitirizani kupempha+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.+
10 Chifukwa aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.
11 Kodi pakati panu pali bambo amene mwana wake atamupempha nsomba, angamupatse njoka mʼmalo mwa nsomba?+
12 Kapenanso atamupempha dzira, kodi angamupatse chinkhanira?
13 Choncho ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.”+
14 Kenako anatulutsa chiwanda mwa munthu chimene chinkamulepheretsa kulankhula.+ Chiwandacho chitatuluka, munthu wosalankhulayo analankhula ndipo gulu la anthu linadabwa kwambiri.+
15 Koma ena mwa iwo ananena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+
16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumukakamiza kuti awasonyeze chizindikiro+ chochokera kumwamba.
17 Atadziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo nyumba yogawanika imagwa.
18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso wagawanika, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Chifukwa inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule.
19 Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa.
20 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu,+ ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+
21 Munthu wamphamvu amene ali ndi zida zokwanira, akamalondera nyumba yake, chuma chake chimatetezeka.
22 Koma wina wamphamvu kuposa iyeyu akabwera nʼkumugonjetsa, amamulanda zida zake zonse zimene amadalira ndipo katundu amene wamulanda, amamugawa kwa ena.
23 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine ndipo amene sagwira ntchito yosonkhanitsa anthu limodzi ndi ine amawabalalitsa.+
24 Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa mʼmalo opanda madzi kufunafuna malo okhala, koma akapanda kupezeka, umanena kuti, ‘Ndibwerera kunyumba yanga imene ndinatulukamo ija.’+
25 Ndiye ukafika umapeza kuti ndi mosesedwa bwino komanso mokongoletsedwa.
26 Ukatero umapita kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa umenewo ndipo ikalowa mkatimo imakhala mmenemo. Choncho zotsatira zake nʼzakuti zochita za munthuyo zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba.”
27 Ali mkati molankhula zimenezi, mayi wina mʼgulu la anthulo anafuula nʼkumuuza kuti: “Wosangalala ndi mayi amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!”+
28 Koma iye ananena kuti: “Ayi, mʼmalomwake, osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga!”+
29 Pamene gulu la anthulo linkachulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “Mʼbadwo uwu ndi mʼbadwo woipa, ukufuna chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+
30 Mofanana ndi Yona+ amene anakhala chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku mʼbadwo uwu.
31 Mfumukazi yakumʼmwera+ adzaiukitsa kwa akufa pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi anthu a mʼbadwo uwu ndipo idzawatsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+
32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.
33 Munthu akayatsa nyale saiika pamalo obisika kapena kuivindikira ndi dengu,* koma amaiika pachoikapo nyale,+ kuti amene akulowa aone kuwala.
34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Ngati diso lako likuyangʼana* pachinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhalanso lowala kwambiri. Koma ngati lili ladyera,* thupi lako lonse lidzachitanso mdima.+
35 Choncho khala tcheru kuti kuwala kumene kuli mwa iwe kusakhale mdima.
36 Ndiye ngati thupi lako lonse ndi lowala kwambiri, popanda mbali ina yamdima, thupi lonse lidzawala kwambiri ngati mmene nyale imachitira pokuunikira ndi kuwala kwake.”
37 Atalankhula zimenezi, Mfarisi wina anamupempha kuti akadye naye. Choncho iye anapita ndipo anakadya chakudya.
38 Koma Mfarisiyo anadabwa ataona kuti akudya chakudyacho asanasambe.*+
39 Choncho Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi muli ngati kapu ndi mbale zimene zatsukidwa kunja kokha koma mkati mwake muli mwakuda. Mkati mwa mitima yanu mwadzaza dyera ndi zinthu zoipa.+
40 Anthu opanda nzeru inu! Kodi amene anapanga kunja si amenenso anapanga mkati?
41 Koma inu mukamapereka mphatso zachifundo,* muzipereka zinthuzo kuchokera pansi pamtima, mukatero zina zonse zokhudza inuyo zidzakhala zoyera.
42 Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti ndi ta luwe komanso cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse.+ Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unali udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simumayenera kunyalanyaza zinthu zinazo.+
43 Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso kupatsidwa moni mʼmisika!+
44 Tsoka kwa inu, chifukwa muli ngati manda* amene sakuoneka bwinobwino*+ moti anthu amayenda pamwamba pake koma osadziwa!”
45 Poyankha mmodzi wa anthu odziwa Chilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, zimene mukunenazi mukunyoza ndi ife tomwe.”
46 Ndiyeno iye anati: “Tsoka kwa inunso odziwa Chilamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simukhudza katunduyo ngakhale ndi chala chanu!+
47 Tsoka kwa inu, chifukwa mumamanga manda* a aneneri, komatu makolo anu ndi amene anawapha!+
48 Mosakayikira, ndinu mboni pa zimene makolo anu anachita. Ndipo mukugwirizana ndi zimene anachitazo, chifukwa iwo anapha aneneri,+ pamene inu mukumanga manda awo.
49 Nʼchifukwa chake nzeru ya Mulungu inanenanso kuti: ‘Ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, koma iwo adzapha komanso kuzunza ena mwa iwo.
50 Choncho mʼbadwo uwu udzaimbidwa mlandu wa magazi a aneneri, amene anakhetsedwa kuyambira pamene dziko linakhazikika.+
51 Kuyambira magazi a Abele+ mpaka magazi a Zekariya, amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi nyumba yopatulika.’*+ Inde ndikukuuzani, mʼbadwo uwu udzayankha mlandu wa magazi amenewo.
52 Tsoka kwa inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu. Inuyo simunalowemo,* ndipo anthu amene akufuna kulowamo mukuwatsekereza!”+
53 Choncho atachoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumupanikiza koopsa nʼkumamufunsa mafunso ambiri,
54 ndipo ankayembekezera kuti anene mawu oti amupezerepo chifukwa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “lizionedwa kuti ndi lopatulika; lizionedwa kuti ndi loyera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ali nafe ngongole.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Musatilowetse mʼmayesero.”
^ Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda amadziwika nalo.
^ Kapena kuti, “dengu loyezera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “likulunjika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “loipa.”
^ Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
^ Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mipando yabwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda opanda chizindikiro chilichonse.”
^ Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
^ Kapena kuti, “kachisi.”