Wolembedwa ndi Luka 24:1-53

  • Yesu anaukitsidwa (1-12)

  • Pamsewu wopita ku Emau (13-35)

  • Yesu anaonekera kwa ophunzira (36-49)

  • Yesu anakwera kumwamba (50-53)

24  Koma pa tsiku loyamba la mlungu, azimayi aja analawirira mʼmawa kwambiri kupita kumandako,* atatenga zonunkhira zimene anakonza zija.+ 2  Koma anapeza kuti mwala wagubuduzidwa pamandawo,*+ 3  ndipo atalowa mʼmandamo, mtembo wa Ambuye Yesu sanaupezemo.+ 4  Atathedwa nzeru ndi zimenezi, anangoona amuna awiri ovala zovala zonyezimira ataima pambali pawo. 5  Azimayiwo anagwidwa ndi mantha ndipo anaweramira pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukufunafuna munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?+ 6  Iye kuno kulibe, waukitsidwa. Kumbukirani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya. 7  Paja ananena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa ndi kuphedwa pomupachika pamtengo nʼkuuka tsiku lachitatu.”+ 8  Choncho anakumbukira mawu akewo+ 9  ndipo anachoka kumandako* nʼkubwerera kukanena zonsezi kwa ophunzira 11 aja ndi kwa ena onse.+ 10  Azimayiwa anali Mariya wa ku Magadala, Jowana ndi Mariya amayi ake a Yakobo. Komanso azimayi ena onse amene anali nawo limodzi ankauza atumwi zinthu zimenezi. 11  Koma kwa iwo, zimene ankawauzazo zinkaoneka ngati zopanda pake ndipo sanawakhulupirire azimayiwo. 12  Koma Petulo ananyamuka nʼkuthamangira kumandako,* ndipo atasuzumira mkati, anangoona nsalu zokha. Choncho anachoka ali wodabwa kwambiri ndi zimene zinachitikazo. 13  Koma tsiku lomweli, awiri a iwo anali pa ulendo wopita kumudzi wina wotchedwa Emau, pamtunda wa pafupifupi makilomita 11* kuchokera ku Yerusalemu. 14  Iwo ankakambirana zokhudza zinthu zonse zimene zinachitikazo. 15  Ndiye ali mkati mokambirana zinthu zimenezi, Yesu anafika nʼkuyamba kuyenda nawo limodzi. 16  Koma sanathe kumuzindikira.+ 17  Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zotani zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Iwo anangoima chilili akuoneka achisoni. 18  Poyankha, mmodzi wa iwo dzina lake Keleopa, anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha mʼYerusalemu monga mlendo,* moti sukudziwa zinthu zimene zachitika mmenemo mʼmasiku amenewa?” 19  Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zake ziti?” Iwo anamuuza kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti,+ amene anali mneneri wamphamvu mʼzochita komanso mʼmawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.+ 20  Komanso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulira anamuperekera kwa anthu amene anamuweruza kuti aphedwe ndipo anamukhomerera pamtengo.+ 21  Koma ife tinkayembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.+ Kuwonjezera pamenepo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni zinthu zimenezi. 22  Komanso azimayi ena mʼgulu lathuli atidabwitsa kwambiri. Iwo analawirira mʼmawa kwambiri kumandako,*+ 23  koma ataona kuti mtembo wake sanaupeze, anabwerako nʼkumanena kuti aonanso masomphenya a angelo, amene awauza kuti iye ali ndi moyo. 24  Kenako enanso mʼgulu lathu lomweli anapita kumandako,*+ ndipo anapezadi kuti mʼmandamo mulibe aliyense, mogwirizana ndi zimene azimayiwo ananena, koma iyeyo sanamuone.” 25  Ndiyeno iye anawauza kuti: “Opanda nzeru inu komanso okayikakayika pa zinthu zonse zimene aneneri ananena! 26  Kodi sikunali koyenera kuti Khristu amve zowawa zonsezi+ nʼkulowa mu ulemerero wake?”+ 27  Atatero anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo mʼMalemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneri analemba.+ 28  Kenako anayandikira mudzi umene ankapita, ndipo iye anachita ngati akupitirira ndi ulendo wake. 29  Koma iwo anamuumiriza kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latsala pangʼono kutha.” Atanena zimenezo analowa mʼnyumba ndipo anakhala nawo. 30  Pamene ankadya nawo chakudya,* anatenga mkate nʼkuudalitsa, kenako anaunyemanyema nʼkuyamba kuwagawira.+ 31  Ataona zimenezi, maso awo anatsegukiratu ndipo anamuzindikira, koma iye anazimiririka.+ 32  Iwo anayamba kuuzana kuti: “Kodi si paja tinakhudzidwa kwambiri mumtima pamene amalankhula nafe mumsewu muja ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” 33  Pa ola lomwelo ananyamuka nʼkubwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anakapeza ophunzira 11 aja komanso anthu ena amene anasonkhana nawo pamodzi. 34  Iwo anawauza kuti: “Nʼzoonadi, Ambuye auka kwa akufa ndipo aonekera kwa Simoni!”+ 35  Nawonso anafotokoza zimene zinachitika pamsewu komanso mmene iwo anamuzindikirira pamene ananyemanyema mkate.+ 36  Akulankhula choncho, Yesu anaimirira pakati pawo nʼkuwauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 37  Koma popeza iwo anadzidzimuka kwambiri ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzimu. 38  Choncho iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika maganizo komanso kukayikakayika mʼmitima yanu? 39  Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone, chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa ngati anga amene mukuwaonawa.” 40  Pamene ankanena zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake. 41  Koma popeza iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42  Choncho anamupatsa chidutswa cha nsomba yowotcha, 43  ndipo iye analandira nʼkudya onse akuona. 44  Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi ndinakuuzani mawu akuti,+ zonse zokhudza ine zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose, zimene aneneri analemba komanso zimene zinalembedwa mʼMasalimo ziyenera kukwaniritsidwa.”+ 45  Zitatero anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba+ 46  ndipo anawauza kuti, “Malemba amanena kuti: Khristu adzazunzika ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa,+ 47  ndipo mʼdzina lake, uthenga woti anthu alape machimo awo+ kuti akhululukidwe udzalalikidwa kwa anthu a mitundu yonse,+ kuyambira ku Yerusalemu.+ 48  Inu mudzakhala mboni za zinthu zimenezi.+ 49  Ndipo ine ndidzakutumizirani chimene Atate wanga anakulonjezani. Koma inu mukhalebe mumzindawu mpaka mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.”+ 50  Kenako anawatsogolera mpaka kukafika nawo ku Betaniya ndipo kumeneko anakweza manja ake nʼkuwadalitsa. 51  Pamene ankawadalitsa, analekana nawo ndipo Mulungu anamutenga kupita naye kumwamba.+ 52  Iwo anamugwadira* nʼkubwerera ku Yerusalemu akusangalala kwambiri.+ 53  Nthawi zonse iwo ankakhala mʼkachisi nʼkumatamanda Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “pamanda achikumbutsowo.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya 60.” Sitadiya imodzi inkakwana mamita 185. Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “Kodi ndiwe mlendo yekhayo mu Yerusalemu amene sakudziwa?”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “Atakhala patebulo.”
Kapena kuti, “anamuweramira.”