Wolembedwa ndi Luka 3:1-38

  • Chiyambi cha ntchito ya Yohane (1, 2)

  • Yohane ankalimbikitsa anthu kuti abatizidwe (3-20)

  • Kubatizidwa kwa Yesu (21, 22)

  • Mzere wa makolo a Yesu Khristu (23-38)

3  Mʼchaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode*+ anali wolamulira chigawo cha Galileya.* Filipo mʼbale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene. 2  Mʼmasiku amenewo Anasi anali wansembe wamkulu ndipo Kayafa+ anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo mawu a Mulungu anafika kwa Yohane+ mwana wa Zekariya mʼchipululu.+ 3  Choncho iye anapita mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 4  Ankachita zimenezi mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mawu a Mneneri Yesaya kuti: “Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.+ 5  Chigwa chilichonse chikwiriridwe, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zisalazidwe. Njira zokhotakhota zikhale zowongoka ndipo malo okumbikakumbika akhale osalaza bwino. 6  Anthu onse adzaona njira ya Mulungu yopulumutsira anthu.’”+ 7  Choncho anayamba kuuza gulu la anthu amene ankabwera kwa iye kudzabatizidwa kuti: “Ana a njoka inu, ndi ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8  Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kuti mwalapa. Ndipo musamadzinamize kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Chifukwa ndikukuuzani kuti Mulungu akhoza kupangira Abulahamu ana kuchokera kumiyala iyi. 9  Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pamizu ya mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabereka zipatso zabwino udulidwa nʼkuponyedwa pamoto.”+ 10  Ndiyeno gulu la anthu linkamufunsa kuti: “Nanga tichite chiyani?” 11  Iye anawayankha kuti: “Munthu amene ali ndi zovala ziwiri agawireko munthu amene alibiretu ndipo amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”+ 12  Okhometsa msonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa+ ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tichite chiyani?” 13  Iye anawauza kuti: “Musamalipiritse anthu* zambiri kuposa mtengo weniweni wa msonkho.”+ 14  Asilikali nawonso ankamufunsa kuti: “Kodi tichite chiyani?” Ndipo iye ankawauza kuti: “Musamavutitse anthu* kapena kuimba aliyense mlandu wabodza,+ koma muzikhutira ndi zimene mumalandira.”* 15  Tsopano anthu ankayembekezera Khristu ndipo onse ankaganiza mʼmitima yawo za Yohane kuti, “Kodi Khristu uja si ameneyu?”+ 16  Yohane anayankha onsewo kuti: “Ine ndikukubatizani ndi madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso moto.+ 17  Fosholo yake youluzira mankhusu* ili mʼmanja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira munkhokwe, koma mankhusu adzawawotcha ndi moto umene sungazimitsidwe.” 18  Iye anaperekanso malangizo ena ambiri ndipo anapitiriza kulengeza uthenga wabwino kwa anthu. 19  Ndiyeno popeza kuti Yohane anadzudzula Herode wolamulira chigawo pa nkhani yokhudza Herodiya, mkazi wa mʼbale wake, komanso chifukwa cha zoipa zonse zimene Herode anachita, 20  Herode anawonjezera choipa china pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.+ 21  Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa.+ Ndiye pamene ankapemphera, kumwamba kunatseguka,+ 22  ndipo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”+ 23  Pamene Yesu+ anayamba ntchito yake anali ndi zaka pafupifupi 30.+ Anthu ankadziwa kuti Yesu anali mwanawa Yosefe,+mwana wa Heli, 24  mwana wa Matati,mwana wa Levi,mwana wa Meliki,mwana wa Yananai,mwana wa Yosefe, 25  mwana wa Matatiyo,mwana wa Amosi,mwana wa Nahumu,mwana wa Esili,mwana wa Nagai, 26  mwana wa Maati,mwana wa Matatiyo,mwana wa Semeini,mwana wa Yoseki,mwana wa Yoda, 27  mwana wa Yoanani,mwana wa Resa,mwana wa Zerubabele,+mwana wa Salatiyeli,+mwana wa Neri, 28  mwana wa Meliki,mwana wa Adi,mwana wa Kosamu,mwana wa Elimadama,mwana wa Ere, 29  mwana wa Yesu,mwana wa Eliezere,mwana wa Yorimu,mwana wa Matati,mwana wa Levi, 30  mwana wa Sumiyoni,mwana wa Yudasi,mwana wa Yosefe,mwana wa Yonamu,mwana wa Eliyakimu, 31  mwana wa Meleya,mwana wa Mena,mwana wa Matata,mwana wa Natani,+mwana wa Davide,+ 32  mwana wa Jese,+mwana wa Obedi,+mwana wa Boazi,+mwana wa Salimoni,+mwana wa Naasoni,+ 33  mwana wa Aminadabu,mwana wa Arini,mwana wa Hezironi,mwana wa Perezi,+mwana wa Yuda,+ 34  mwana wa Yakobo,+mwana wa Isaki,+mwana wa Abulahamu,+mwana wa Tera,+mwana wa Nahori,+ 35  mwana wa Serugi,+mwana wa Reu,+mwana wa Pelegi,+mwana wa Ebere,+mwana wa Shela,+ 36  mwana wa Kainani,mwana wa Aripakisadi,+mwana wa Semu,+mwana wa Nowa,+mwana wa Lameki,+ 37  mwana wa Metusela,+mwana wa Inoki,mwana wa Yaredi,+mwana wa Mahalaliyeli,+mwana wa Kainani,+ 38  mwana wa Enosi,+mwana wa Seti,+mwana wa Adamu,+mwana wa Mulungu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anali bwanamkubwa wa chigawo cha 4 cha dera.”
Ameneyu anali Herode Antipa. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Musamakakamize anthu kulipira.”
Kapena kuti, “ndi malipiro anu.”
Kapena kuti, “Musamalande anthu zinthu zawo.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.