Machitidwe a Atumwi 19:1-41

  • Paulo ku Efeso; anthu ena anabatizidwanso (1-7)

  • Ntchito yolalikira ya Paulo (8-10)

  • Utumiki unkayenda bwino ngakhale kuti ena ankakhulupirira zamizimu (11-20)

  • Chisokonezo ku Efeso (21-41)

19  Nthawi inayake, Apolo+ ali ku Korinto, Paulo anadzera kumadera akumtunda mpaka anafika ku Efeso.+ Kumeneko anapezako ophunzira ena, 2  ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandira mzimu woyera mutakhala okhulupirira?”+ Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu sitinamvepo kuti kuli mzimu woyera.” 3  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga munabatizidwa ubatizo wamtundu wanji?” Iwo anayankha kuti: “Tinabatizidwa ubatizo wa Yohane.”+ 4  Kenako Paulo anati: “Ubatizo umene Yohane ankabatiza anthu unali chizindikiro chakuti munthu walapa.+ Ankauza anthu kuti akhulupirire amene akubwera mʼmbuyo mwake,+ kutanthauza Yesu.” 5  Atamva zimenezi, anthuwo anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 6  Ndiyeno Paulo atawagwira pamutu,* iwo analandira mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula malilime* komanso kunenera.+ 7  Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12. 8  Kwa miyezi itatu, Paulo ankapita kusunagoge+ kumene ankalankhula molimba mtima. Kumeneko ankakamba nkhani ndiponso kuwafotokozera mfundo zogwira mtima zokhudza Ufumu wa Mulungu.+ 9  Koma ena anapitiriza kuchita makani komanso sankakhulupirira, ndipo ankanena zonyoza Njirayo+ pamaso pa anthu ambiri. Choncho iye anawachokera+ nʼkuchotsanso ophunzirawo pakati pawo. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakamba nkhani muholo pasukulu ya Turano. 10  Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, moti anthu onse okhala mʼchigawo cha Asia, Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye. 11  Mulungu anapitiriza kuchita zinthu zamphamvu komanso zodabwitsa kudzera mwa Paulo.+ 12  Moti anthu ankatenga ngakhale tinsalu ndi zovala* zimene zakhudza thupi la Paulo nʼkupita nazo kwa odwala,+ ndipo matenda awo ankatheratu. Nayonso mizimu yoipa inkatuluka.+ 13  Koma Ayuda ena amene ankayendayenda nʼkumatulutsa ziwanda, anayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pofuna kuchiritsa anthu amene anali ndi mizimu yoipa. Ankanena kuti: “Ndikukulamula mʼdzina la Yesu amene Paulo akumulalikira.”+ 14  Panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu wa Chiyuda, amene ankachita zimenezi. 15  Koma mzimu woipa unawayankha kuti: “Ine Yesu ndikumudziwa+ ndipo Paulo ndikumudziwanso bwino.+ Nanga inuyo ndinu ndani?” 16  Kenako, munthu amene anali ndi mzimu woipa uja anawalumphira. Analimbana nawo mmodzimmodzi mpaka kuwagonjetsa onsewo, moti anatuluka mʼnyumbamo nʼkuthawa ali maliseche komanso atavulala. 17  Anthu onse anadziwa zimenezi, Ayuda ndi Agiriki amene ankakhala ku Efeso. Choncho onse anagwidwa ndi mantha ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitiriza kulemekezedwa. 18  Anthu ambiri amene anakhala okhulupirira ankabwera kudzaulula machimo awo ndiponso kufotokoza poyera zoipa zimene ankachita. 19  Anthu ambiri amene ankachita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo nʼkuwatentha pamaso pa anthu onse.+ Ndipo atawerengera mtengo wake anapeza kuti anali okwana ndalama zasiliva zokwana 50,000. 20  Choncho mawu a Yehova* anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.+ 21  Zitachitika zimenezi, Paulo anatsimikiza mumtima mwake kupita ku Yerusalemu,+ kudzera ku Makedoniya+ ndi ku Akaya. Iye anati: “Ndikakafika kumeneko, ndikapitanso ku Roma.”+ 22  Choncho ku Makedoniya anatumizako awiri mwa anthu amene ankamutumikira, omwe ndi Timoteyo+ ndi Erasito.+ Koma iye anakhalabe mʼchigawo cha Asia kwa kanthawi ndithu. 23  Pa nthawiyo panayambika chisokonezo chachikulu+ chokhudza Njira ya Ambuye.+ 24  Panali munthu wina wosula siliva dzina lake Demetiriyo. Amisiri ankapindula kwambiri chifukwa cha ntchito yake yopanga tiakachisi tasiliva ta Atemi.+ 25  Demetiriyo anasonkhanitsa amisiriwo, limodzi ndi anthu ogwira ntchito yokhudza zinthu zimenezi. Ndiyeno anawauza kuti: “Anthu inu, mukudziwa kuti timapeza chuma kuchokera mu ntchito imeneyi. 26  Tsopano mukuona ndiponso mukumva zoti Paulo wakopa anthu ambiri kuti ayambe kukhulupirira zinthu zina. Wachita zimenezi osati mu Efeso+ mokha muno, koma pafupifupi mʼchigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja si milungu ayi.+ 27  Ndipo chimene chikuopsa kwambiri si kunyozeka kwa ntchito yathu yokhayi, koma kachisi wa mulungu wamkulu wamkazi Atemi azidzaonedwa ngati wopanda pake. Mukudziwa kuti aliyense mʼchigawo chonse cha Asia komanso padziko lonse lapansi amalemekeza Atemi, koma chifukwa cha zimene Paulo akunena ulemerero wake udzatheratu.” 28  Atamva zimenezi anthuwo anakwiya kwambiri nʼkuyamba kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 29  Zitatero mumzindawo munadzaza chisokonezo, ndipo anthu onse anathamangira mʼbwalo lamasewera, atagwira Gayo ndi Arisitako+ nʼkuwakokera mʼbwalomo. Gayo ndi Arisitako ankayenda ndi Paulo ndipo kwawo kunali ku Makedoniya. 30  Paulo ankafuna kulowa mkati mwa gulu la anthulo, koma ophunzira sanamulole. 31  Anthu ena oyangʼanira zikondwerero ndi masewera, amene anali anzake, nawonso anamutumizira uthenga womuchonderera kuti asaike moyo wake pachiswe pokalowa mʼbwalo lamaseweralo. 32  Kunena zoona, gulu lonselo linali litasokonezeka, ena ankafuula zina, ena zina. Moti ambiri sankadziwa nʼkomwe kuti nʼchifukwa chiyani asonkhana kumeneko. 33  Choncho iwo anatulutsa Alekizanda mʼgululo ndipo Ayuda anamukankhira kutsogolo. Kenako Alekizanda anakweza dzanja kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34  Koma iwo atazindikira kuti iye ndi Myuda, onse pamodzi anafuula kwa maola pafupifupi awiri kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!” 35  Pamapeto pake, woyangʼanira mzinda atauza gulu la anthulo kuti likhale chete anati: “Anthu inu a mu Efeso, alipo kodi munthu amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndi umene umayangʼanira kachisi wa Atemi wamkulu ndi chifaniziro chimene chinagwa kuchokera kumwamba? 36  Popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, muyenera kudekha, musachite zinthu mopupuluma. 37  Inu mwabweretsa anthu awa amene si akuba mu akachisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38  Choncho ngati Demetiriyo+ ndi amisiri ali nawowa akuimba mlandu munthu, pamakhala masiku a milandu ndipo abwanamkubwa* alipo. Akasumirane kumeneko. 39  Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, chigamulo chake chiyenera kukaperekedwa pabwalo lovomerezeka. 40  Zimene zachitika lerozi nʼzoopsa chifukwa tingathe kuimbidwa nazo mlandu woukira boma. Palibiretu chifukwa chomveka chimene tingapereke pa chipolowe chimene chachitikachi.” 41  Atanena zimenezi, anauza anthuwo kuti achoke pamalowo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “atawaika manja.”
Kapena kuti, “zilankhulo zosiyanasiyana.”
Kapena kuti, “maepuloni.”
Bwanamkubwa wachigawo cha Roma. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.