Salimo 110:1-7
Salimo ndi Nyimbo ya Davide.
110 Yehova anauza Ambuye wanga kuti:
“Khala kudzanja langa lamanja+Mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”+
2 Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu kuti ulamulirenso madera ena osati mu Ziyoni mokha. Iye adzanena kuti:
“Pita pakati pa adani ako ndipo ukawagonjetse.”+
3 Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.*
Gulu la achinyamata amene ali ngati mame amʼbandakucha likukuthandiza.Iwo ndi apadera kwa ine komanso ndi okongola.
4 Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo. Iye wati:
“Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+Mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki!”+
5 Yehova adzakhala kudzanja lako lamanja.+Iye adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+
6 Adzapereka chiweruzo ku* mitundu ya anthu.+Adzachititsa kuti mʼdziko mudzaze mitembo ya anthu.+
Adzaphwanya mtsogoleri* wa dziko lalikulu.*
7 Ali mʼnjira, iye* adzamwa madzi amumtsinje.
Choncho adzatukula kwambiri mutu wake.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “pa tsiku limene asilikali ako adzakonzekere kumenya nkhondo.”
^ Kapena kuti, “pakati pa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu.”
^ Kapena kuti, “wa dziko lonse lapansi.”
^ Kutanthauza, “Ambuye wanga” amene atchulidwa mu vesi 1.