Salimo 135:1-21
135 Tamandani Ya!*
Tamandani dzina la Yehova,Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+
2 Inu amene mwaimirira mʼnyumba ya Yehova,Mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+
3 Tamandani Ya, chifukwa Yehova ndi wabwino.+
Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, chifukwa kuchita zimenezi nʼkosangalatsa.
4 Ya wasankha Yakobo kuti akhale wake,Wasankha Isiraeli kuti akhale chuma chake chapadera.*+
5 Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu.Ambuye wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.+
6 Yehova amachita chilichonse chimene wafuna+Kumwamba, padziko lapansi, mʼnyanja komanso mʼmalo onse ozama.
7 Amachititsa kuti mitambo* ikwere kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima.Amatulutsa mphepo kuchokera mʼnyumba zake zosungira zinthu.+
8 Iye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,Ana a anthu komanso ana a nyama.+
9 Anachita zizindikiro komanso zodabwitsa pakati pako, iwe Iguputo,+Anachita zimenezi kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+
10 Anawononga mitundu yambiri+Ndipo anapha mafumu amphamvu+
11 Anapha Sihoni mfumu ya Aamori,+Ogi mfumu ya Basana+Komanso anawononga maufumu onse a ku Kanani.
12 Dziko lawo analipereka kuti likhale cholowa,Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+
13 Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo kwamuyaya.
Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo* ku mibadwo yonse.+
14 Chifukwa Yehova adzateteza anthu ake pa mlandu,*+Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+
15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,Ntchito ya manja a anthu.+
16 Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+Maso ali nawo koma sangaone.
17 Makutu ali nawo koma sangamve.
Mʼkamwa mwawo mulibe mpweya.+
18 Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+
19 Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova.
Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova.
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+
Inu amene mumaopa Yehova, tamandani Yehova.
21 Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+Atamandidwe mu Ziyoni.+
Tamandani Ya!+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “chamtengo wapatali.”
^ Kapena kuti, “nthunzi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chanu chidzakhalapo.”
^ Kapena kuti, “adzaweruzira anthu ake mlandu.”