Wolembedwa ndi Mateyu 13:1-58

  • MAFANIZO OKHUDZA UFUMU (1-52)

    • Wofesa mbewu (1-9)

    • Chifukwa chake Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo (10-17)

    • Tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (18-23)

    • Tirigu ndi namsongole (24-30)

    • Kanjere kampiru komanso zofufumitsa (31-33)

    • Kugwiritsa ntchito mafanizo kunakwaniritsa ulosi (34, 35)

    • Tanthauzo la fanizo la tirigu ndi namsongole (36-43)

    • Chuma chobisika ndi ngale yamtengo wapatali (44-46)

    • Khoka (47-50)

    • Chuma chatsopano ndi chakale (51, 52)

  • Yesu anakanidwa mʼdera lakwawo (53-58)

13  Tsiku limenelo, Yesu anachoka kunyumba nʼkukakhala pansi mʼmphepete mwa nyanja. 2  Gulu lalikulu la anthu linasonkhana pamene iye anali, moti iye anakwera mʼngalawa nʼkukhala pansi, ndipo gulu lonse la anthulo linaimirira mʼmphepete mwa nyanjayo.+ 3  Kenako anawauza zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mafanizo+ kuti: “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4  Pamene ankafesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa msewu ndipo kunabwera mbalame nʼkuzidya.+ 5  Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6  Koma dzuwa litawala kwambiri zinawauka ndipo zinafota chifukwa zinalibe mizu. 7  Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinakula nʼkulepheretsa mbewuzo kukula.+ 8  Koma zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinayamba kubereka zipatso. Mbewu ina inabereka zipatso 100, ina 60 ndipo ina 30.+ 9  Amene ali ndi makutu amve.”+ 10  Ndiyeno ophunzira ake anabwera nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo?”+ 11  Koma iye anawayankha kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika+ za Ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo. 12  Chifukwa amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale zimene akuganiza kuti ali nazo.+ 13  Nʼchifukwa chake ndikulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo. Chifukwa ngakhale kuti akuyangʼana, sakuona chilichonse. Ngakhale kuti akumva, sakumvetsa zimene zikunenedwa ndipo sakuzindikira tanthauzo lake.+ 14  Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa. Ulosiwo umanena kuti: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira tanthauzo lake. Kuyangʼana mudzangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 15  Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkuzindikira tanthauzo lake mʼmitima yawo kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.’+ 16  Koma inu ndinu osangalala chifukwa maso anu amaona komanso makutu anu amamva.+ 17  Chifukwa ndithu ndikukuuzani, aneneri ambiri komanso anthu olungama ankalakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ komanso kuti amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve. 18  Tsopano mvetserani fanizo la munthu wofesa mbewu.+ 19  Munthu aliyense akamva mawu a Ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo+ amabwera nʼkuchotsa zimene zafesedwa mumtima wa munthuyo. Iyi ndi mbewu imene inafesedwa mʼmbali mwa msewu ija.+ 20  Koma imene inafesedwa pamiyala, ndi munthu amene wamva mawu nʼkuwavomereza mwamsanga ndiponso mosangalala.+ 21  Komabe chifukwa chakuti amakhala alibe mizu amapitiriza kukula kwa nthawi yochepa. Koma akakumana ndi masautso kapena kuyamba kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga. 22  Imene inafesedwa paminga, ndi munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za moyo wa mʼnthawi* ino+ ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula ndipo sabereka zipatso.+ 23  Koma mbewu imene inafesedwa panthaka yabwino, ndi munthu amene wamva mawu nʼkuzindikira tanthauzo lake, amene amaberekadi zipatso, wina amabereka zipatso 100, wina 60 ndipo wina 30.”+ 24  Anawafotokozera fanizo linanso kuti: “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi munthu amene anafesa mbewu yabwino mʼmunda mwake. 25  Koma anthu ali mʼtulo, kunabwera mdani wake kudzafesa namsongole mʼmunda wa tiriguwo nʼkuchoka. 26  Tiriguyo atakula nʼkutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekera. 27  Ndiyeno akapolo a mwinimunda uja anabwera nʼkudzamuuza kuti, ‘Ambuye, kodi mʼmesa munafesa mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokeranso kuti?’ 28  Iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane anachita zimenezi.’+ Akapolowo anati, ‘Ndiye kodi mukufuna kuti tipite tikamuzule?’ 29  Koma iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopera kuti pozula namsongoleyo mungazule limodzi ndi tirigu. 30  Zisiyeni zonse zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola. Mʼnyengo yokolola ndidzauza okolola kuti: Choyamba sonkhanitsani namsongole nʼkumumanga mʼmitolo kuti akawotchedwe. Kenako musonkhanitse tirigu mʼnyumba yanga yosungiramo zinthu.’”+ 31  Anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati kanjere ka mpiru* kamene munthu anakatenga nʼkukadzala mʼmunda mwake.+ 32  Kanjere kameneka ndi kakangʼono kwambiri kuposa njere zonse, koma kakamera kamakula kwambiri kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo umakhala mtengo, moti mbalame zamumlengalenga zimabwera kudzapeza malo okhala munthambi zake.” 33  Anawafotokozeranso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati zofufumitsa zimene mkazi wina anazitenga nʼkuzisakaniza ndi ufa wokwana mabeseni atatu akuluakulu oyezera, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”+ 34  Yesu analankhula zonsezi ndi gulu la anthulo pogwiritsa ntchito mafanizo. Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo,+ 35  kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe. Mneneriyo anati: “Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mafanizo. Ndidzafalitsa zinthu zimene zinabisika kuchokera pachiyambi.”*+ 36  Kenako atauza gulu la anthulo kuti lizipita, analowa mʼnyumba. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Timasulireni fanizo lija la namsongole mʼmunda.” 37  Poyankha iye ananena kuti: “Amene anafesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu. 38  Munda ndi dziko+ ndipo mbewu yabwino ndi ana a Ufumu. Koma namsongole ndi ana a woipayo,+ 39  ndipo mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi. Nthawi yokolola ikuimira mapeto a nthawi* ino ndipo okololawo ndi angelo. 40  Mofanana ndi namsongole amene amamusonkhanitsa nʼkumuwotcha pamoto, zidzakhalanso choncho pamapeto a nthawi* ino.+ 41  Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake ndipo adzachotsa mu Ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa ndiponso anthu osamvera malamulo. 42  Kenako adzawaponya mungʼanjo yamoto.+ Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. 43  Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambiri ngati dzuwa+ mu Ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu amve. 44  Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika mʼmunda, chimene munthu anachipeza nʼkuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo nʼkukagula mundawo.+ 45  Komanso Ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. 46  Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali, anapita ndipo mwamsanga anakagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo nʼkukagula ngaleyo.+ 47  Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati khoka limene laponyedwa mʼnyanja ndipo likusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu. 48  Likadzaza amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi nʼkumasankha zabwino+ ndi kuziika mʼmitanga, koma zosafunika+ amazitaya. 49  Ndi mmenenso zidzakhalire pamapeto a nthawi* ino. Angelo adzapita nʼkukachotsa oipa pakati pa olungama 50  ndipo adzawaponya mungʼanjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. 51  Kodi mukumvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52  Kenako anawauza kuti: “Popeza kuti zili choncho, mphunzitsi aliyense amene waphunzitsidwa za Ufumu wakumwamba ali ngati munthu yemwe ndi mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.” 53  Yesu atamaliza kunena mafanizo amenewa anachoka kumeneko. 54  Atafika mʼdera lakwawo+ anayamba kuwaphunzitsa musunagoge wawo, moti anthu anadabwa ndipo ananena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti?+ 55  Kodi uyu si mwana wa kalipentala uja?+ Kodi mayi ake si Mariya, ndipo azichimwene ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?+ 56  Ndipo azichemwali ake onse sitili nawo konkuno? Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”+ 57  Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena mʼnyumba mwake, koma kwina.”+ 58  Ndipo sanachite ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa chakuti anthuwo analibe chikhulupiriro.

Mawu a M'munsi

“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.
Mabaibulo ena amati, “kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.”