Miyambo 8:1-36
8 Nzerutu ikuitana,
Ndipo kuzindikira kukufuula.+
2 Imaima pamalo okwera+ mʼmbali mwa msewu.Imaima pamphambano za misewu.
3 Pambali pa mageti, olowera mumzinda,Pakhomo lolowera mumzindawo,Ikungokhalira kufuula mokweza kuti:+
4 “Ndikuitana anthu inu.Ndikulankhula ndi nonsenu* mokweza.
5 Inu osadziwa zinthu, phunzirani kukhala ochenjera.+Opusa inu, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.*
6 Mvetserani, chifukwa zimene ndikulankhula ndi zofunika.Pakamwa panga pamalankhula zinthu zabwino.
7 Chifukwa pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,Ndipo milomo yanga imanyansidwa ndi zoipa.
8 Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.
Pa mawu onsewo palibe abodza kapena achinyengo.
9 Ndi osavuta kumva kwa munthu wozindikiraKomanso ndi olondola kwa anthu odziwa zinthu.
10 Landirani malangizo* anga osati siliva,Komanso kudziwa zinthu mʼmalo mwa golide woyenga bwino kwambiri,+
11 Chifukwa nzeru ndi zabwino kwambiri kuposa miyala ya korali.*Zinthu zina zonse zamtengo wapatali sizingafanane nazo.
12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.Ndimadziwa zinthu ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+
13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+
Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso mawu achinyengo.+
14 Ine ndili ndi malangizo abwino komanso nzeru zothandiza.+Kumvetsa zinthu+ ndiponso mphamvu+ ndi zanga.
15 Chifukwa cha ine, mafumu amalamulira,Ndipo akuluakulu a boma amakhazikitsa malamulo olungama.+
16 Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,Ndipo anthu olemekezeka amaweruza mwachilungamo.
17 Ndimakonda amene amandikonda,Ndipo amene akundifunafuna adzandipeza.+
18 Chuma ndi ulemerero zili ndi ine,Ndili ndi chuma* chosatha komanso chilungamo.
19 Zimene munthu amapeza kwa ine nʼzabwino kuposa golide, ngakhale golide woyengedwa bwino kwambiri,Ndipo mphatso zimene ndimapereka nʼzabwino kuposa siliva wabwino kwambiri.+
20 Ndimayenda mʼnjira yachilungamo,Komanso pakati pa misewu yachilungamo.
21 Anthu amene amandikonda, ndimawapatsa cholowa chamtengo wapatali,Ndipo ndimadzazitsa nyumba zawo zosungiramo zinthu.
22 Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova,+Ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.+
23 Ndinakhazikitsidwa kale kwambiri,*+Kuyambira pachiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe.+
24 Ndinabadwa kulibe madzi akuya,*+Kulibe akasupe osefukira madzi.
25 Mapiri asanaikidwe mʼmalo ake,Komanso mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinabadwa,
26 Iye asanapange dziko lapansi ndi nthaka yake,Kapena zibuma zoyamba za dothi lapadziko lapansi.
27 Pamene ankakonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+Pamene ankaika malire pakati pa mlengalenga ndi nyanja,+
28 Pamene ankakhazikitsa* mitambo kumwamba,Pamene ankakhazikitsa akasupe a madzi akuya,
29 Pamene ankaikira nyanja lamuloKuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+Pamene ankakhazikitsa maziko a dziko lapansi,
30 Pa nthawi imeneyo, ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+
Iye ankasangalala kwambiri ndi ine+ tsiku ndi tsiku.Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+
31 Ndinkasangalala ndi dziko lapansi limene anakonza kuti anthu azikhalamo,Ndipo ana a anthu ndi amene ankandisangalatsa kwambiri.*
32 Tsopano ana anga, ndimvereni.Ndithu, osangalala ndi amene amayenda mʼnjira zanga.
33 Mverani malangizo+ kuti mukhale anzeru,Ndipo musamawanyalanyaze.
34 Wosangalala ndi munthu amene amandimvetseraPobwera mʼmamawa kwambiri pakhomo la nyumba yanga tsiku lililonse,*Podikirira pafupi ndi khomo lolowera mʼnyumba mwanga.
35 Chifukwa wondipeza ine adzapeza moyo,+Ndipo Yehova amasangalala naye.
36 Koma amene amandinyalanyaza amadzipweteka yekha,Ndipo amene amadana ndi ine amakonda imfa.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi ana a anthu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “muumvetse mtima.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “cholowa chamtengo wapatali.”
^ Kapena kuti, “kuyambira nthawi yosakumbukirika.”
^ Kapena kuti, “Ndinabadwa ndi ululu wapobereka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ankalimbitsa.”
^ Kapena kuti, “mtundu wa anthu ndi umene unkandisangalatsa kwambiri.”
^ Kapena kuti, “Pokhala maso pakhomo.”