Nehemiya 9:1-38

  • Anthu analapa machimo awo (1-38)

    • Yehova ndi Mulungu wokhululuka (17)

9  Pa tsiku la 24 la mwezi umenewu Aisiraeli anasonkhana pamodzi ndipo anasala kudya atavala ziguduli komanso atadzithira dothi kumutu.+ 2  Aisiraeli anadzipatula kwa anthu onse omwe sanali Aisiraeli+ ndipo anaimirira nʼkuyamba kuulula machimo awo komanso zolakwa za makolo awo.+ 3  Iwo anaimirirabe ndipo anawerenga mokweza buku la Chilamulo+ cha Yehova Mulungu wawo kwa maola atatu. Kwa maola enanso atatu anaulula machimo awo ndiponso kugwadira Yehova Mulungu wawo. 4  Ndiyeno Yesuwa, Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya,+ Bani ndi Kenani anakwera pansanja+ ya Alevi nʼkuyamba kufuula kwa Yehova Mulungu wawo. 5  Ndipo Yesuwa, Kadimiyeli, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya, omwe anali Alevi, anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu mpaka kalekale.*+ Inu Mulungu wathu, anthuwa atamande dzina lanu laulemerero, lomwe ndi lalikulu kuposa dalitso ndiponso chitamando chilichonse. 6  Inu nokha ndinu Yehova.+ Munapanga kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba ndi magulu ake onse. Munapanganso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo komanso nyanja ndi zonse zomwe zili mmenemo. Mumasunga zinthu zamoyo ndipo magulu akumwamba amakugwadirani. 7  Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu+ nʼkumutulutsa mumzinda wa Uri+ wa Akasidi ndipo munamupatsa dzina lakuti Abulahamu.+ 8  Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika,+ choncho munachita naye pangano kuti mudzamʼpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Munalonjeza kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbadwa*+ zake ndipo munakwaniritsadi zimene munalonjeza chifukwa ndinu wolungama. 9  Choncho munaona mavuto amene makolo athu ankakumana nawo ku Iguputo+ ndipo munamva kulira kwawo pa Nyanja Yofiira. 10  Ndiyeno munakhaulitsa Farao, atumiki ake onse ndiponso anthu onse amʼdziko lake powaonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa.+ Munachita zimenezi chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepa munadzipangira dzina lomwe lilipobe mpaka lero.+ 11  Munagawa nyanja pamaso pawo ndipo anadutsa panthaka youma.+ Anthu amene ankawathamangitsa munawaponya pansi pa nyanja ngati mwala woponyedwa mʼmafunde amphamvu.+ 12  Masana munkawatsogolera ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawatsogolera ndi chipilala cha moto kuti uziwaunikira njira imene ankayenera kudutsa.+ 13  Ndiyeno munatsikira paphiri la Sinai+ nʼkulankhula nawo muli kumwamba+ ndipo munawapatsa ziweruzo zolungama, malamulo a choonadi* ndiponso mfundo ndi malangizo abwino.+ 14  Munawauza za Sabata+ lanu lopatulika ndipo munawapatsa malangizo, mfundo ndi malamulo kudzera mwa Mose mtumiki wanu. 15  Pamene anali ndi njala munawapatsa chakudya chochokera kumwamba+ ndipo pamene anali ndi ludzu munatulutsa madzi pathanthwe.+ Munawauza kuti alowe nʼkutenga dziko limene munalumbira* kuti mudzawapatsa. 16  Koma makolo athuwo anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi+ ndipo sankatsatira malamulo anu. 17  Iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire zinthu zodabwitsa zimene munawachitira. Mʼmalomwake anaumitsa khosi ndipo anasankha munthu woti awatsogolere pobwereranso ku ukapolo ku Iguputo.+ Koma inu ndinu Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika*+ chochuluka, choncho simunawasiye.+ 18  Ngakhale pamene anapanga chifaniziro chachitsulo cha mwana wa ngʼombe nʼkuyamba kunena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutulutsani ku Iguputo,’+ ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani, 19  inu simunawasiye mʼchipululu, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Chipilala cha mtambo sichinawachokere masana ndipo chinkawatsogolera, komanso chipilala cha moto sichinawachokere usiku ndipo chinkawaunikira njira yoyenera kudutsa.+ 20  Munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti akhale anzeru.+ Simunawamane mana+ ndipo pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi.+ 21  Kwa zaka 40 munawapatsa chakudya mʼchipululu+ moti sanasowe kanthu. Zovala zawo sizinathe+ ndipo mapazi awo sanatupe. 22  Munawapatsa maufumu ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo mʼzigawozigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ lomwe ndi dziko la mfumu ya Hesiboni+ komanso dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. 23  Ndipo munachulukitsa ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Kenako munawalowetsa mʼdziko limene munalonjeza makolo awo kuti adzalowamo nʼkulitenga kukhala lawo.+ 24  Choncho ana awo analowa nʼkutenga dzikolo.+ Munagonjetsa Akanani,+ anthu amʼdzikolo ndipo munawapereka mʼmanja mwawo. Munaperekanso mafumu a Akananiwo ndi anthu amʼdzikolo kwa Aisiraeli kuti awachitire zimene akufuna. 25  Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndi dziko la nthaka yachonde.+ Ndipo anatenga zitsime zokumba kale, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, minda ya mpesa, minda ya maolivi+ ndiponso mitengo yokhala ndi zipatso zambiri. Choncho ankadya nʼkukhuta moti ananenepa ndipo ankasangalala ndi ubwino wanu waukulu. 26  Koma iwo anali osamvera ndipo anakugalukirani.+ Anasiya kutsatira Chilamulo chanu, anapha aneneri anu amene ankawachenjeza kuti abwerere kwa inu ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+ 27  Chifukwa cha zimenezi, munawapereka mʼmanja mwa adani awo+ amene ankawazunza.+ Koma akakumana ndi mavuto ankakulirirani ndipo inu munkamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, munkawapatsa anthu oti awapulumutse mʼmanja mwa adani awo.+ 28  Koma akangokhala pamtendere ankachitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawapondereza.+ Zikatero, ankabwereranso kwa inu nʼkupempha thandizo+ ndipo inu munkamva muli kumwambako nʼkuwapulumutsa mobwerezabwereza chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 29  Ngakhale kuti munkawachenjeza kuti ayambenso kutsatira Chilamulo chanu, iwo ankadzikuza ndipo ankakana malamulo anu.+ Iwo anachimwa chifukwa sankatsatira ziweruzo zanu zimene munthu akamazitsatira amakhala ndi moyo.+ Anatseka makutu awo ndi kuumitsa makosi awo ndipo anakana kumvera. 30  Munawalezera mtima+ kwa zaka zambiri ndipo munapitiriza kuwachenjeza pogwiritsa ntchito mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, koma anakana kumvera. Kenako munawapereka mʼmanja mwa anthu amʼdzikolo.+ 31  Ndipo chifukwa cha chifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya, popeza ndinu Mulungu wachisomo ndi wachifundo.+ 32  Tsopano inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu, wochititsa mantha, wosunga pangano komanso wachikondi chokhulupirika,+ musachepetse mavuto amene tikukumana nawo ifeyo, mafumu athu, akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu ndi anthu anu onse kuyambira mu nthawi ya mafumu a Asuri+ mpaka pano. 33  Inu mwachita zinthu molungama pa zonse zimene zatichitikira. Mwachita zinthu mokhulupirika koma ife ndi amene tachita zinthu zoipa.+ 34  Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire Chilamulo chanu ndipo sanamvere malamulo anu kapena zikumbutso zanu zowachenjeza. 35  Ngakhale pamene ankalamuliridwa ndi mafumu awo ndipo ankadalitsidwa kwambiri komanso ankakhala mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, iwo sankakutumikirani+ ndipo sanasiye kuchita zoipa. 36  Pano ndife akapolo.+ Ndife akapolo mʼdziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino. 37  Mafumu amene mwalola kuti azitilamulira chifukwa cha machimo athu+ ndi amene akusangalala ndi zokolola zochuluka zamʼdzikoli. Iwo akulamulira matupi athu komanso ziweto zathu mmene akufunira, ndipo tili pamavuto aakulu. 38  Choncho chifukwa cha zimenezi, tikuchita pangano lodalirika+ lochita kulemba ndipo akalonga athu, Alevi athu ndi ansembe athu atsimikizira panganoli ndi chidindo chawo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuyambira kalekale mpaka kalekale.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “malamulo odalirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “munalumbira mutakweza dzanja.”
Kapena kuti, “kukoma mtima kosatha.”