Numeri 14:1-45

  • Anthu ankafuna kubwerera ku Iguputo (1-10)

    • Lipoti labwino la Yoswa ndi Kalebe (6-9)

  • Yehova anakwiya; Mose anapepesa (11-19)

  • Chilango: zaka 40 mʼchipululu (20-38)

  • Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Aamaleki (39-45)

14  Kenako gulu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anapitiriza kulira usiku wonse.+ 2  Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni,+ ndipo gulu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera mʼchipululu muno. 3  Nʼchifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+ 4  Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+ 5  Mose ndi Aroni atamva zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi pamaso pa gulu lonse la Aisiraeli. 6  Ndipo Yoswa+ mwana wa Nuni ndi Kalebe+ mwana wa Yefune, amene anakazonda nawo dzikolo, anangʼamba zovala zawo. 7  Iwo anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Dziko limene tinakalowamo nʼkulizonda ndi dziko labwino kwambiri.+ 8  Ngati Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsadi mʼdzikolo nʼkulipereka kwa ife, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 9  Koma chofunika nʼchakuti musapandukire Yehova, ndipo anthu amʼdzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo, koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope.” 10  Koma gulu lonselo linayamba kunena zoti liwaponye miyala.+ Kenako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisiraeli onse+ pamwamba pa chihema chokumanako. 11  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza mpaka liti?+ Kodi adzayamba liti kundikhulupirira pambuyo pa zizindikiro zonse zimene ndachita pakati pawo?+ 12  Ndiwagwetsera mliri ndi kuwawononga, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwowa.”+ 13  Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene anthuwa munawalanditsa mʼmanja mwawo pogwiritsa ntchito mphamvu zanu, adzamva zimenezi.+ 14  Iwo akamva adzauza anthu amʼdziko lino, amenenso amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ komanso kuti mumaonekera kwa iwo pamasomʼpamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo, pamene usiku mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto.+ 15  Mukapha anthu onsewa kamodzinʼkamodzi,* mitundu imene yamva za inu idzanena kuti: 16  ‘Yehova analephera kufikitsa anthuwo kudziko limene anawalumbirira, choncho anangowaphera mʼchipululu.’+ 17  Chonde Yehova, tsopano sonyezani kuti mphamvu zanu ndi zazikulu mogwirizana ndi mmene munalonjezera kuti: 18  ‘Yehova ndi wosakwiya msanga, ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.*+ Amakhululukira zolakwa ndi machimo, koma sadzalekerera wolakwa osamupatsa chilango. Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.’+ 19  Chonde, khululukani zolakwa za anthuwa mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chachikulu, ngati mmene mwakhala mukuwakhululukira kuchokera ku Iguputo mpaka pano.”+ 20  Ndiyeno Yehova anati: “Chabwino, ndawakhululukira mogwirizana ndi zimene wanena.+ 21  Komanso, pali ine Mulungu wamoyo, dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi ulemerero wa Yehova.+ 22  Komabe anthu onse amene aona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, komanso zimene ndachita mʼchipululu, koma apitiriza kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, ndipo sanamvere mawu anga,+ 23  sadzaliona mʼpangʼono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+ 24  Koma chifukwa choti mtumiki wanga Kalebe+ anali wosiyana ndi ena,* ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse, ndithu ndidzamulowetsa mʼdziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzatenga dzikolo kukhala lawo.+ 25  Popeza Aamaleki ndi Akanani+ akukhala kuchigwa, mawa mubwerere nʼkuyamba ulendo wopita kuchipululu kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.”+ 26  Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 27  “Kodi gulu la anthu oipa amenewa lingʼungʼudza motsutsana nane mpaka liti?+ Ndamva kungʼungʼudza kumene Aisiraeli akuchita motsutsana nane.+ 28  Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzakuchitirani mogwirizana ndi zimene ndamva mukulankhula.+ 29  Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30  Nonsenu simudzalowa mʼdziko limene ndinalumbira* kuti mudzakhalamo,+ kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+ 31  Koma ana anu amene munati adzatengedwa ndi adani,+ amenewo ndi amene ndidzawalowetse mʼdzikolo ndipo adzadziwa dziko limene inu mwalikana.+ 32  Koma inuyo mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno. 33  Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu kwa zaka 40,+ ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu,* mpaka womalizira kufa wa inu atagona mʼmanda mʼchipululu muno.+ 34  Mudzalangidwa mogwirizana ndi kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, kwa masiku 40.+ Mudzalangidwa kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi, kuti mudziwe kuipa kotsutsana ndi ine.* 35  Ine Yehova ndalankhula. Zimene ndidzachitire gulu lonse la anthu oipali, amene asonkhana kuti atsutsane ndi ine ndi izi: Onse adzafera mʼchipululu muno ndipo adzathera momwe muno.+ 36  Komanso amuna amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo, omwe anabweretsa lipoti loipa nʼkupangitsa kuti anthu onse adandaule motsutsana ndi Mose,+ 37  amuna amene anadzanena zoipa zokhazokha zokhudza dzikolo, Yehova adzawapatsa chilango ndipo adzafa.+ 38  Koma Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene anali mʼgulu la anthu amene anakazonda dziko, adzakhalabe ndi moyo ndithu.”’”+ 39  Mose atawauza Aisiraeli onse mawu amenewa, anthu onse anayamba kulira kwambiri. 40  Komanso, iwo anadzuka mʼmawa kwambiri kuti apite kudera lamapiri lija, ndipo anati: “Ife takonzeka kuti tipite kumalo amene Yehova ananena, chifukwa tachimwa.”+ 41  Koma Mose anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya lamulo la Yehova? Zimenezo sizikuthandizani. 42  Musapite kumeneko chifukwa Yehova sali nanu ndipo adani anuwo akakugonjetsani.+ 43  Kumeneko mukakumana ndi Aamaleki komanso Akanani,+ ndipo akakuphani ndi lupanga. Yehova sapita nanu kumeneko chifukwa mwasiya kutsatira Yehova.”+ 44  Komabe anthuwo anadzikuza ndipo ananyamuka nʼkupita kudera lamapiri kuja,+ koma Mose limodzi ndi likasa la pangano la Yehova sanachoke pakati pa msasa.+ 45  Zitatero Aamaleki ndi Akanani omwe ankakhala kudera lamapirilo anatsika nʼkuyamba kuwapha ndi kuwabalalitsa mpaka ku Horima.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ngati munthu mmodzi.”
Kapena kuti, “amasonyeza kukoma mtima kosatha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali ndi mzimu wosiyana ndi ena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinakweza dzanja langa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “uhule wanu.”
Kapena kuti, “kondiona ngati mdani.”