Oweruza 16:1-31

  • Samisoni ku Gaza (1-3)

  • Samisoni ndi Delila (4-22)

  • Samisoni anabwezera nʼkufa (23-31)

16  Nthawi ina, Samisoni anapita ku Gaza nʼkuona hule kumeneko ndipo analowa mʼnyumba ya huleyo. 2  Anthu a ku Gaza anauzidwa kuti: “Samisoni wabwera kuno.” Choncho anazungulira malowo nʼkumubisalira usiku wonse pageti la mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse nʼkumaganiza kuti: “Kukangocha timupha.” 3  Koma Samisoni anagonabe mpaka pakati pa usiku. Kenako anadzuka pakati pa usikupo nʼkugwira zitseko za geti la mzindawo pamodzi ndi nsanamira zake ziwiri nʼkuzizula pamodzi ndi chokhomera cha getilo. Atatero anazinyamula pamapewa nʼkupita nazo pamwamba pa phiri limene linayangʼanana ndi Heburoni. 4  Kenako Samisoni anayamba kukonda mkazi wina wakuchigwa cha Soreki, dzina lake Delila.+ 5  Zitatero olamulira a Afilisiti anapita kwa mkaziyo nʼkumuuza kuti: “Umunyengerere+ kuti udziwe chimene chimamuchititsa kuti akhale ndi mphamvu zambiri komanso zimene tingachite kuti timufoole, timʼmange ndiponso timugonjetse. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva zokwana 1,100.” 6  Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Tandiuza, kodi chimene chimakuchititsa kuti ukhale ndi mphamvu zambiri nʼchiyani, nanga angakumange ndi chiyani kuti akugonjetse?” 7  Samisoni anamuyankha kuti: “Atandimanga ndi zingwe 7 zatsopano zaziwisi,* ndingafooke nʼkukhala ngati munthu wamba.” 8  Choncho olamulira a Afilisiti anamʼbweretsera zingwe 7 zatsopano zaziwisi. Kenako Delila anamanga Samisoni ndi zingwezo. 9  Apa nʼkuti anthu atabisalira Samisoni mʼchipinda china. Mkaziyo anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Atamva zimenezo, Samisoni anadula zingwe zija ngati mmene ulusi* umadukira ukagwira moto.+ Chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike. 10  Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Iwe wandipusitsa pondiuza bodza. Chonde ndiuze zimene angakumange nazo.” 11  Samisoni anamuyankha kuti: “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritsepo ntchito, ndingafooke nʼkukhala ngati munthu wamba.” 12  Ndiyeno Delila anatenga zingwe zatsopano nʼkumumanga nazo manja ndipo anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” (Pa nthawiyi nʼkuti anthu atamʼbisalira mʼchipinda china.) Samisoni atamva zimenezi anadula zingwe zimene anamʼmanga nazozo ngati akudula ulusi.+ 13  Kenako Delila anauza Samisoni kuti: “Wakhala ukundipusitsa pondiuza zabodza.+ Ndiuze zimene angakumange nazo.” Samisoni anayankha kuti: “Umange zingongo 7 zamʼmutu mwanga ndi ulusi wowombera mulitali mwa nsalu.” 14  Iye anamangadi zingongozo nʼkuzipina. Kenako anamuuza kuti: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Samisoni atamva zimenezi anadzuka ndipo anachotsa chopinira chija komanso ulusi uja. 15  Ndiyeno Delila anauza Samisoni kuti: “Nʼchifukwa chiyani umanena kuti, ‘Ndimakukonda,’+ chonsecho mtima wako suli pa ine? Wakhala ukundipusitsa katatu konse ndipo sunandiuze chimene chimakuchititsa kuti ukhale ndi mphamvu zambiri.”+ 16  Chifukwa chakuti Delila ankapanikiza Samisoni tsiku lililonse komanso kumuumiriza kuti amuuze, Samisoni anafika potopa nazo kwambiri moti sakanathanso kupirira.+ 17  Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse. Anamuuza kuti: “Mʼmutu mwanga simunadutsepo lezala, chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira tsiku limene ndinabadwa.*+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kutha, ndipo ndingafooke nʼkukhala ngati anthu ena onse.” 18  Delila ataona kuti Samisoni wamuululira zonse, nthawi yomweyo anatumiza uthenga kwa olamulira a Afilisiti,+ wakuti: “Tsopano bwerani chifukwa wandiululira zonse.” Choncho olamulira a Afilisitiwo anabwera kwa Delila atatenga ndalama zija. 19  Kenako Delila anachititsa kuti Samisoni agone tulo pamiyendo pake, ndipo anaitana munthu wina kuti amʼmete zingongo 7 za mʼmutu mwake. Zitatero Samisoni analibenso mphamvu kwa Delila chifukwa mphamvu zake zinamʼchokera. 20  Ndiyeno Delila anati: “Afilisiti aja abwera Samisoni!” Samisoni atamva zimenezi anadzuka nʼkunena kuti: “Ndipita ngati mmene ndimachitira muja+ ndipo ndipulumuka.” Koma sanadziwe kuti Yehova anali atamusiya. 21  Choncho Afilisiti anamʼgwira ndipo anamuboola maso. Kenako anapita naye ku Gaza nʼkumumanga ndi matcheni awiri akopa,* ndipo iye ankayendetsa mwala wa mphero mʼndende. 22  Koma tsitsi lake lija linayambanso kukula.+ 23  Olamulira a Afilisiti anasonkhana kuti apereke nsembe kwa Dagoni+ mulungu wawo komanso kuti achite chikondwerero, popeza ankanena kuti: “Mulungu wathu watipatsa mdani wathu Samisoni!” 24  Anthu ataona Samisoni, anayamba kutamanda mulungu wawo. Iwo ankanena kuti: “Mulungu wathu watipatsa mdani wathu, munthu amene wawononga dziko lathu,+ ndiponso kupha anthu ambiri amtundu wathu.”+ 25  Chifukwa choti anasangalala kwambiri, anayamba kunena kuti: “Katengeni Samisoni kuti adzatisangalatse.” Choncho anakamutenga kundende kuti adzawasangalatse ndipo anamuimika pakati pa zipilala. 26  Kenako Samisoni anauza mnyamata amene anamugwira dzanja kuti: “Ndithandize kuti ndigwire zipilala zimene zalimbitsa nyumbayi kuti ndizitsamire.” 27  (Pa nthawiyi nʼkuti mʼnyumbamo mutadzaza amuna ndi akazi. Olamulira onse a Afilisiti analinso momwemo. Padenga la nyumbayo panali amuna ndi akazi pafupifupi 3,000 amene ankaonerera Samisoni akuwasangalatsa.) 28  Ndiyeno Samisoni+ anafuulira Yehova, kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu+ kamodzi kokhaka. Inu Mulungu, ndiloleni ndiwabwezere Afilisitiwa chifukwa cha limodzi mwa maso angawa.”+ 29  Kenako Samisoni anagwira mwamphamvu zipilala ziwiri zapakati zimene zinalimbitsa nyumbayo. Iye anatsamiritsa dzanja lake lamanja kuchipilala chimodzi ndipo lamanzere kuchipilala china. 30  Ndiyeno Samisoni anafuula kuti: “Ndife nawo limodzi Afilisitiwa!” Kenako anakankha zipilalazo ndi mphamvu zake zonse ndipo nyumbayo inagwera olamulira a Afilisiti ndi anthu onse amene anali mmenemo.+ Choncho anthu amene Samisoni anawapha pa nthawi ya imfa yake anali ambiri kuposa amene anawapha pa nthawi imene anali ndi moyo.+ 31  Kenako azichimwene ake ndi anthu onse akubanja la bambo ake, anapita kukatenga mtembo wa Samisoni nʼkudzauika mʼmanda a bambo ake Manowa,+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli. Samisoni anali ataweruza Isiraeli zaka 20.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zingwe zatsopano zaziwisi 7 za mitsempha ya nyama.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ulusi wa fulakisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba mwa mayi anga.”
Kapena kuti, “amkuwa.”