Yoswa 6:1-27

  • Mpanda wa Yeriko unagwa (1-21)

  • Rahabi ndi banja lake anapulumuka (22-27)

6  Mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha Aisiraeli. Palibe amene ankatuluka kapena kulowa mumzindawo.+ 2  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Mzinda wa Yeriko ndaupereka mʼmanja mwako, pamodzi ndi mfumu yake ndi asilikali ake amphamvu.+ 3  Asilikali nonsenu muziguba kuzungulira mzindawu kamodzi pa tsiku, ndipo muchite zimenezi kwa masiku 6. 4  Ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa atanyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo. Pa tsiku la 7 mudzagube kuzungulira mzindawo maulendo 7, ansembewo akuliza malipenga.+ 5  Ansembewo akadzaliza malipenga a nyanga za nkhosa pa ulendo wa 7, ndipo inu mukadzamva kulira kwa malipengawo, nonse mudzafuule mwamphamvu mfuu yankhondo, ndipo mpanda wonse wa mzindawo udzagwa mpaka pansi.+ Pamenepo, nonsenu mudzathamangire kumeneko.” 6  Choncho Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe nʼkuwauza kuti: “Nyamulani likasa la pangano, ndipo ansembe 7 aziyenda patsogolo pa Likasa la Yehovalo. Ansembewo atenge malipenga 7 a nyanga za nkhosa zamphongo.”+ 7  Anauzanso asilikali kuti: “Nyamukani, mukagube kuzungulira mzindawo. Gulu la asilikali onyamula zida zankhondo+ likhale patsogolo pa Likasa la Yehova.” 8  Monga Yoswa ananenera, ansembe 7 ananyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa pamaso pa Yehova. Iwo anatsogola akuliza malipengawo, ndipo likasa la pangano la Yehova linkabwera pambuyo pawo. 9  Gulu la asilikali onyamula zida linkayenda patsogolo pa ansembe oimba malipenga, pamene gulu lina la asilikali linkabwera pambuyo pa Likasa, uku malipenga aja akuimbidwa mosalekeza. 10  Yoswa analamula asilikaliwo kuti: “Musafuule kapena kulankhula kanthu, ndipo pakamwa panu pasatuluke mawu alionse mpaka tsiku limene ndidzakuuzani kuti, ‘Fuulani!’ Pamenepo mudzafuule.” 11  Choncho iye atalamula, Likasa la Yehova linazungulira mzindawo kamodzi, asilikaliwo akuguba nalo. Kenako iwo anabwerera kumsasa ndipo anakhala kumeneko usiku wonse. 12  Tsiku lotsatira, Yoswa anadzuka mʼmawa kwambiri, ndipo ansembe ananyamula Likasa+ la Yehova. 13  Ansembe 7 onyamula malipenga 7 a nyanga za nkhosa, omwe ankakhala patsogolo pa Likasa la Yehova, ankayenda akuliza malipenga mosalekeza. Patsogolo pawo panali gulu la asilikali onyamula zida, ndipo pambuyo pa Likasa la Yehova pankabwera asilikali ena, uku malipenga akulira mosalekeza. 14  Iwo anagubanso kuzungulira mzindawo kamodzi pa tsiku lachiwirili ndipo atamaliza anabwerera kumsasa. Anachita zimenezi kwa masiku 6.+ 15  Pa tsiku la 7, anadzuka mʼmamawa kwambiri ndipo anaguba kuzungulira mzindawo ngati mmene ankachitira. Pa tsikuli anazungulira mzindawo maulendo 7.+ 16  Pa ulendo wa 7, ansembe aja analiza malipenga awo, ndipo Yoswa anauza asilikaliwo kuti: “Fuulani!+ Chifukwa Yehova wakupatsani mzindawu! 17  Mzindawu komanso zinthu zonse zimene zilimo ziyenera kuwonongedwa,+ zonse ndi za Yehova. Rahabi+ yekha, hule uja, musamuphe. Mumusiye pamodzi ndi onse amene ali nawo mʼnyumba mwake, chifukwa iye anabisa anthu amene tinawatuma.+ 18  Koma zinthu zoyenera kuwonongedwa musamale nazo,+ kuopera kuti mungazisirire nʼkuzitenga+ chifukwa mukatero, mudzabweretsa tsoka pamsasa wa Isiraeli ndipo nawonso udzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa.+ 19  Koma siliva yense, golide yense ndiponso zipangizo zonse zamkuwa ndi zachitsulo, nʼzopatulika kwa Yehova.+ Ziyenera kukaikidwa mosungiramo chuma cha Yehova.”+ 20  Ansembe aja ataliza malipenga, asilikali nʼkumva kulira kwa malipengawo, asilikaliwo anafuula mwamphamvu+ mfuu yankhondo ndipo mpanda wa mzindawo unagwa mpaka pansi.+ Zitatero, iwo analowa mumzindawo. Aliyense anathamangira kumeneko nʼkulanda mzindawo. 21  Aliyense amene anali mumzindawo anamupha ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, anyamata ndi anthu okalamba omwe. Anaphanso ngʼombe, nkhosa ndi abulu.+ 22  Yoswa anauza amuna awiri aja amene anawatuma kukafufuza zokhudza dzikolo, kuti: “Pitani kunyumba kwa hule uja ndipo mukamutulutse limodzi ndi onse amene ali mʼnyumba mwake, mogwirizana ndi zimene munalumbira kwa iye.”+ 23  Choncho, anyamata amene anakafufuza zokhudza dziko aja, anapita kukatulutsa Rahabi limodzi ndi bambo ake, mayi ake, azichimwene ake ndi onse amene anali naye. Anatulutsa achibale ake onse,+ ndipo anayenda nawo bwinobwino kupita nawo kumalo ena kunja kwa msasa wa Isiraeli. 24  Atatero, anatentha mzindawo ndi zonse zimene zinali mmenemo. Koma siliva, golide ndiponso zipangizo zamkuwa ndi zachitsulo, anakaziika mosungiramo chuma cha Yehova.+ 25  Yoswa anangosiya Rahabi hule uja limodzi ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake komanso onse amene anali naye.+ Mayiyo akukhalabe ndi Aisiraeli mpaka lero+ chifukwa anabisa anthu amene Yoswa anawatuma kukafufuza zokhudza Yeriko.+ 26  Pa nthawiyo Yoswa analumbira* kuti: “Munthu amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu adzakhale wotembereredwa pamaso pa Yehova. Akadzangoyala maziko ake, mwana wake woyamba adzafe, ndipo akadzaika zitseko zapageti, mwana wake wotsiriza adzafe.”+ 27  Choncho Yehova anali ndi Yoswa,+ ndipo mbiri yake inamveka padziko lonse.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “analumbiritsa anthu.”