Yoweli 3:1-21

  • Yehova adzaweruza mitundu yonse ya anthu (1-17)

    • Chigwa cha Yehosafati (2,12)

    • Chigwa choweruzira (14)

    • Yehova, malo othawirako a Isiraeli (16)

  • Yehova adzadalitsa anthu ake (18-21)

3  “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawiyo,Ndikadzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo,+  2  Ndidzasonkhanitsanso anthu a mitundu yonse,Nʼkuwabweretsa mʼchigwa cha Yehosafati.* Ndipo ndidzawaweruza kumeneko,+Mʼmalo mwa anthu anga ndiponso cholowa changa, Isiraeli.Chifukwa anamwaza Aisiraeli pakati pa anthu a mitundu ina,Ndiponso anagawana dziko langa.+  3  Ankachitira maere anthu anga.+Ankagulitsa mnyamata kuti alipire hule,Ndipo ankagulitsa mtsikana kuti agule vinyo woti amwe.  4  Komanso kodi ndakulakwira chiyaniIwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya? Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita? Ngati mukundibwezera,Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+  5  Chifukwa chakuti mwatenga siliva ndi golide wanga,+Ndipo mwabweretsa zinthu zanga zabwino kwambiri mu akachisi anu,  6  Komanso mwagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agiriki,+Kuti muwapititse kutali ndi dziko lawo,  7  Choncho ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa,+Ndipo ndikubwezerani zimene munachita.  8  Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda.+Iwo adzawagulitsa kwa anthu a ku Sheba, mtundu wa anthu akutali.Ine Yehova ndanena zimenezi.  9  Lengezani kwa anthu a mitundu ina+ kuti: ‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu! Asilikali onse abwere nʼkuukira!+ 10  Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo kuti zikhale mikondo. Munthu wofooka anene kuti: “Ndine wamphamvu.” 11  Inu anthu a mitundu yotizungulira, bwerani mudzathandize ndipo nonse musonkhane.’”+ Inu Yehova, bweretsani asilikali anu kumalo amenewo. 12  “Mitundu ya anthu inyamuke nʼkubwera kuchigwa cha Yehosafati,Chifukwa ndidzakhala kumeneko kuti ndiweruze anthu a mitundu yozungulira.+ 13  Yambani kumweta ndi chikwakwa, chifukwa zokolola zacha. Bwerani nʼkuyamba kuponda chifukwa moponderamo mphesa mwadzaza.+ Malo ogweramo vinyo asefukira, chifukwa zoipa zawo zachuluka kwambiri. 14  Anthu ambirimbiri ali mʼchigwa choweruzira mlandu,Chifukwa tsiku la Yehova layandikira mʼchigwa choweruzira mlandu.+ 15  Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima,Ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala. 16  Yehova adzabangula kuchokera ku Ziyoni,Ndipo adzalankhula mokweza ali ku Yerusalemu. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka.Koma Yehova adzakhala malo othawirako a anthu ake,+Malo achitetezo champhamvu kwa Aisiraeli. 17  Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+ Yerusalemu adzakhala malo opatulika,+Ndipo anthu achilendo* sadzadutsanso mmenemo.+ 18  Nthawi imeneyo mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera.+Mʼmapiri angʼonoangʼono mudzayenda mkaka.Ndipo mʼmitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi. Kasupe adzatuluka mʼnyumba ya Yehova,+Ndipo adzathirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe. 19  Koma Iguputo adzasanduka bwinja,+Ndipo Edomu adzakhala chipululu chopanda kanthu.+Chifukwa cha nkhanza zimene anachitira anthu a ku Yuda,+Ndiponso chifukwa chokhetsa magazi a anthu osalakwa mʼdziko la Yudalo.+ 20  Koma ku Yuda kuzidzakhala anthu nthawi zonse,Ndipo ku Yerusalemu kudzakhala anthu mibadwomibadwo.+ 21  Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+Ndipo ine Yehova ndizidzakhala ku Ziyoni.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Yehova ndi Woweruza.”
Kapena kuti, “ochokera kwina.”