Kalata ya Yuda 1:1-25
1 Ndine Yuda, kapolo wa Yesu Khristu komanso mʼbale wake wa Yakobo.+ Ndikulembera oitanidwa+ amene Mulungu, yemwe ndi Atate wathu, amawakonda komanso kuwateteza kuti akhale ogwirizana ndi Yesu Khristu.+
2 Mulungu awonjezere chifundo, mtendere ndi chikondi chake kwa inu.
3 Okondedwa, ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso chimene tonsefe tili nacho.+ Komabe, ndaona kuti ndi bwino ndilembe zokulimbikitsani kumenya mwamphamvu nkhondo ya chikhulupiriro+ chomwe chinaperekedwa kamodzi kokha* kwa oyerawo.
4 Ndatero chifukwa chakuti anthu ena alowa mozemba pakati panu. Malemba anasonyezeratu kalekale kuti anthu amenewa adzaweruzidwa. Anthuwa ndi osaopa Mulungu ndipo atenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lopanda manyazi.*+ Komanso asonyeza kuti ndi osakhulupirika kwa Ambuye wathu mmodzi yekha amene anatigula, Yesu Khristu.+
5 Ngakhale kuti mukudziwa kale zonsezi, ndikufuna kukukumbutsani kuti Yehova* atapulumutsa anthu ake powatulutsa mʼdziko la Iguputo,+ pambuyo pake anawononga amene analibe chikhulupiriro.+
6 Ndiponso angelo amene anasiya utumiki umene Mulungu anawapatsa kumwamba komanso malo amene ankayenera kukhala,+ Mulungu anawamanga ndi maunyolo omwe sangaduke* nʼkuwasunga mumdima wandiweyani kuti adzaweruzidwe pa tsiku lalikulu.+
7 Mofanana ndi zimenezi, anthu amʼmizinda ya Sodomu ndi Gomora komanso mizinda yozungulira ankachita chiwerewere* chonyansa kwambiri ndiponso kugonana mʼnjira imene si yachibadwa.+ Anthu amenewa anapatsidwa chilango cha chiwonongeko chosatha*+ ndipo ndi chitsanzo chotichenjeza.
8 Ngakhale zili choncho, anthu amene alowa mozembawa nawonso amakonda zongolota, amaipitsa matupi awo komanso a ena,* amanyoza ulamuliro ndiponso amanenera zamwano anthu amene Mulungu wawapatsa ulemerero.+
9 Koma pamene Mikayeli,+ mkulu wa angelo,+ anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose,+ sanayese nʼkomwe kumuweruza komanso kumunyoza,+ mʼmalomwake anati: “Yehova* akudzudzule.”+
10 Koma anthu amenewa amalankhula monyoza zinthu zonse zimene sakuzimvetsa nʼkomwe.+ Ndipo zimene amazimvetsa mwachibadwa, mofanana ndi nyama zomwe siziganiza,+ amapitiriza kudziipitsa nazo.
11 Ali ndi tsoka chifukwa atsatira njira ya Kaini,+ asankha njira yolakwika ya Balamu+ kuti alandire mphoto ndipo awonongeka polankhula moukira+ ngati Kora.+
12 Anthuwa akamadya nanu pamaphwando amene mumachita kuti musonyezane chikondi,+ amakhala ngati miyala ikuluikulu yobisika mʼmadzi. Alinso ngati abusa amene amadzidyetsa okha mopanda mantha,+ mitambo yopanda madzi yotengekatengeka ndi mphepo,+ komanso ngati mitengo yopanda zipatso koma nyengo yake yobereka itatsala pangʼono kutha, yoferatu* ndiponso yoti yazulidwa.
13 Ali ngatinso mafunde oopsa apanyanja otulutsa thovu la zinthu zowachititsa manyazi,+ ndiponso nyenyezi zoyenda mopanda dongosolo, ndipo Mulungu wawaika mumdima wandiweyani mmene adzakhalemo mpaka kalekale.+
14 Ngakhalenso Inoki,+ wa mʼbadwo wa 7 kuchokera kwa Adamu, analosera za iwowa pamene anati: “Taonani! Yehova* anabwera ndi angelo ake masauzandemasauzande+
15 kudzaweruza anthu onse,+ ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha zinthu zonyoza Mulungu zimene anachita, komanso chifukwa cha zinthu zonse zoipa kwambiri zimene ochimwa osaopa Mulunguwa anamunenera.”+
16 Anthu amenewa amakonda kungʼungʼudza,+ kudandaula za moyo wawo, amangochita zimene amalakalaka+ komanso amalankhula modzitama. Amatamandanso anthu nʼcholinga choti apezepo phindu.+
17 Koma inu okondedwa, kumbukirani mawu amene atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu ananeneratu kalero.
18 Paja ankakuuzani kuti: “Mʼmasiku otsiriza kudzakhala onyoza, omwe azidzangochita zinthu zoipa zimene amalakalaka.”+
19 Anthu amenewa amachititsa kuti anthu asamagwirizane,+ amachita zinthu ngati zinyama ndipo satsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu.
20 Koma inu okondedwa, muzilimbitsa chikhulupiriro chanu choyera kwambiri komanso muzipemphera mogwirizana ndi mzimu woyera,+
21 kuti mupitirize kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Mulungu azikukondani,+ pamene mukuyembekezera chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chomwe chidzachititse kuti mupeze moyo wosatha.+
22 Ndiponso pitirizani kuchitira chifundo+ anthu amene amakayikira zimene timakhulupirira.+
23 Apulumutseni+ powachotsa mofulumira pamoto. Pitirizaninso kuchitira chifundo anthu ena, koma muzisamala. Powachitira chifundocho, muzidana ndi zovala zawo zomwe azidetsa ndi makhalidwe oipa.*+
24 Mulungu wathu waulemerero angathe kukutetezani kuti musagwe ndiponso kukuthandizani kuti muime pamaso pake opanda cholakwa+ mukusangalala kwambiri.
25 Iye yekha ndi Mulungu komanso Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, ndipo ndi woyenera ulemerero, ufumu, mphamvu ndi ulamuliro kuchokera kalekale kufika panopa komanso mpaka muyaya. Ame.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “kamodzi mpaka kalekale.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “maunyolo amuyaya.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “moto wosatha.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kutanthauza kuti amawaipitsa pochita chiwerewere.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “yakufa kawiri.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “azidetsa ndi ntchito zathupi.”