Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?
Mutu 20
Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?
Lembani dzina la aphunzitsi amene amakusangalatsani. ․․․․․
N’chifukwa chiyani amakusangalatsani? ․․․․․
Lembani dzina la aphunzitsi amene simugwirizana nawo. ․․․․․
MUKHOZA kusankha anzanu koma n’zosatheka kusankha aphunzitsi. Koma mwina inuyo aphunzitsi anu onse amakusangalatsani ngati mmene zinalili ndi David wazaka 18. Iye ananena kuti: “Sindinayambanepo ndi mphunzitsi aliyense. Onse ankandikonda chifukwa ndinkawalemekeza.”
Koma mwina aphunzitsi anu amachita zofanana ndi zimene amachita aphunzitsi a Sarah yemwe ali ndi zaka 11. Iye ananena kuti: “Aphunzitsi athu ndi ovuta kwambiri. Akamaphunzitsa palibe chomwe ndimamva. Nthawi zina safotokoza zinthu bwinobwino kapena amafotokoza zinthu zambirimbiri moti amatisokoneza.” Kuti muzigwirizana
ndi aphunzitsi anu, choyamba mukufunika kudziwa vuto lenileni limene muli nalo. Mukazindikira vutolo, n’zotheka kulithetsa. Ikani chizindikiro ichi ✔ m’bokosi loyenerera kapena lembani chifukwa china m’munsimu.□ Sindimamva zimene amaphunzitsa
□ Ndimaona kuti amandibera malikisi
□ Ndimaona kuti amakondera ana ena
□ Amandipatsa chilango chopweteka pa zinthu zazing’ono
□ Ndimaona kuti amadana nane
□ Zina ․․․․․
Kodi mungatani kuti mavuto amenewa athe? Choyamba, tsatirani malangizo amene mtumwi Petulo analemba akuti: “Nonsenu mukhale amaganizo amodzi, omverana chisoni.” (1 Petulo 3:8) Kodi n’chiyani chimene chingakuchititseni kuti muziwamvera chisoni, kapena kuti kuwamvetsa, aphunzitsi anu amene mumaona kuti ndi ovuta? Tiyeni tikambirane mfundo zingapo zokhudza aphunzitsi zomwe zikhoza kukuthandizani.
Aphunzitsi nawonso amalakwitsa. Nawonso ndi anthu moti amalakwitsa zinthu ndiponso ali ndi mavuto awo. Yakobo analemba kuti: “Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro, ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse.” (Yakobo 3:2) Brianna yemwe ali ndi zaka 19 ananena kuti: “Aphunzitsi athu a masamu sankachedwa kupsa mtima ndipo nthawi zambiri ankangotikalipira. Chifukwa cha zimenezi sitinkawalemekeza.” Kodi aphunzitsiwo ankachita zimenezi chifukwa chiyani? Brianna anati: “Anthu a m’kalasi mwathu anali ovuta ndipo ankachitira dala zinthu zosokonekera kwambiri kuti awapweteketse mtima aphunzitsiwo.”
Mukalakwitsa chinachake mwachidziwikire mungasangalale ngati aphunzitsi anu atangokusiyani, makamaka ngati mwalakwitsa chinthucho chifukwa chakuti mwapanikizika kwambiri. Ndi zimene nanunso muyenera kuchita kwa aphunzitsi anu. Lembani zimene zinachitika
posachedwapa kusukulu kwanu ndiponso zimene mukuganiza kuti zinakwiyitsa aphunzitsi anu.․․․․․
Mphunzitsi amakhala ndi ana omwe amawakonda kwambiri. Taganizirani mavuto amene aphunzitsi anu amakumana nawo: Ndi ana angati m’kalasi mwanu amene amakondadi sukulu? Pa ana amene amakonda sukuluwo ndi angati amene amamvetsera mwachidwi zimene aphunzitsi akuphunzitsa kwa mphindi 30 kapena kuposa? Nanga ndi angati amene amati akayambana ndi munthu wina amakaphwetsera mkwiyo wawo pa aphunzitsi? Ndiye tayerekezani kuti inuyo muli ndi ntchito yophunzitsa ana oposa 20 kapena 30 a msinkhu wanu ndipo phunziro limene mukuwaphunzitsalo ambiri salikonda. Kodi simungamakonde ana okhawo amene alidi ndi chidwi chofuna kuphunzira?
N’zoona kuti mukhoza kukhumudwa ngati aphunzitsi anu amachita zinthu mokondera ana ena. Pofotokoza za aphunzitsi ake, Natasha ananena kuti: “Aphunzitsi athu ankati akatipatsa homuweki ankatiikira malire a nthawi imene tiyenera kudzapereka homuwekiyo koma amene ankasewera mpira ankawapatsa nthawi yambiri. Iwo ankachita zimenezi chifukwa anali wachiwiri kwa kochi wa timuyo.” Ngati zofanana ndi zimenezi zitakuchitikirani dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene amachita aphunzitsizi zikusokoneza maphunziro anga?’ Ngati sizikusokoneza maphunziro anu, palibe chifukwa choti muzichitira nsanje kapena kukhumudwa.
Lembani zimene mungachite mukakhala m’kalasi kuti aphunzitsi anu adziwe zoti mumachita chidwi ndi zimene akuphunzitsa.
․․․․․
Kumangokhala kusamvetsetsana. Nthawi zina mumadana ndi aphunzitsi anu chifukwa chosamvetsetsana chabe kapena chifukwa
chosiyana zimene mumakonda. Mwachitsanzo, ngati mumakonda kufunsa mafunso akhoza kuganiza kuti mukutsutsa zimene akuphunzitsa, kapena mukanena nthabwala akhoza kukutengani ngati munthu wopanda ulemu kapena wopusa.Kodi mungatani ngati aphunzitsi anu ataona zinthu molakwika chonchi? Baibulo limanena kuti: “Musabwezere choipa pa choipa. . . . Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:17, 18) Choncho yesetsani kupewa zinthu zimene zingakhumudwitse aphunzitsi anuwo. Komanso musamachitire dala zinthu zimene zingachititse kuti azikudandaulani. Ndipotu muyenera kumacheza nawo komanso kuwakonda. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kuwakonda? Ovutawo?’ Mungasonyeze kuti mumawakonda powapatsa moni mwaulemu mukakumana nawo. Kupitiriza kuchita zinthu mwaulemu komanso kuwamwetulira mukamalankhula nawo kungachititse aphunzitsi anuwo kusintha, n’kuyamba kukukondani.—Aroma 12:20, 21.
Mwachitsanzo, aphunzitsi a Ken nthawi zambiri ankamuona ngati munthu wamwano. Iye anati: “Ndine wamanyazi kwambiri ndipo nthawi zambiri sindinkakonda kulankhula ndi aphunzitsi anga.” Kodi vuto limeneli anathana nalo bwanji? Ken ananena kuti: “Patapita nthawi ndinazindikira kuti aphunzitsiwo ankafuna kundithandiza ndiye ndinayesetsa kuti ndidziwane ndi aphunzitsi onse. Nditangochita zimenezi ndinaona kuti ndinayamba kukhoza bwino m’kalasi.”
Miyambo 25:15) Akakuchitirani zinthu zopanda chilungamo simuyenera kuwapsera mtima kapena kuwalankhula mwamwano. Zimenezi zingachititse aphunzitsi anuwo kusintha maganizo.—Miyambo 15:1.
Koma n’zoona kuti nthawi zina aphunzitsi anuwo sangasinthe ngakhale mutayesetsa kumawachitira ulemu, choncho muyenera kuleza mtima. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali [kapena mphunzitsi], ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.” (Aphunzitsi anu akakuchitirani zinthu zopanda chilungamo, kodi maganizo anu oyamba amakhala oti muwachite chiyani?
․․․․․
Koma kodi choyenera kuchita ndi chiyani?
․․․․․
Mmene Mungathetsere Nkhani Zina
Kuzindikira kuti nawonso aphunzitsi anu amalakwitsa zinthu zina ndi poyambira chabe. Koma kodi mungatani kuti muthetse nkhani zina? Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mumadandaula ndi zinthu zili m’munsizi?
Amandibera malikisi. Katrina ananena kuti: “Ndinkakhoza bwino kwambiri nthawi zonse. Koma chaka china aphunzitsi a sayansi anandilepheretsa. Sindinamvetse kuti zatheka bwanji. Makolo anga anapita kukalankhulana ndi ahedi koma anangondiwonjezera malikisi ochepa moti ndinali wokwiyabe.” Ngati zofanana ndi zimenezi zitakuchitikirani si bwino kuyamba kulankhula zinthu zambirimbiri zowanena aphunzitsi anuwo. M’malomwake mungachite bwino kutengera chitsanzo cha Natani yemwe amatchulidwa m’Baibulo. Iye anapatsidwa ntchito yovuta youlula tchimo lalikulu limene Mfumu Davide inachita. Natani sanalowe m’nyumba ya mfumuyo mwachipongwe kwinaku akufotokoza mokweza zimene mfumuyo yalakwitsa. Iye anapeza njira yabwino yolankhulira ndi Davide.—2 Samueli 12:1-7.
Miyambo 18:13) Mukamvetsera mukhoza kufotokoza bwinobwino zimene mungachite kuti muzikhoza bwino. Ngakhale atapanda kukusinthirani malikisi omwe anaperekawo, kuchita zimenezi kungawathandize kusintha mmene amakuonerani.
Nanunso mungachite bwino kulankhula ndi aphunzitsi anuwo modzichepetsa komanso mwaulemu. Koma ngati mutakwiya kwambiri kapena kuyamba kuwanena aphunzitsiwo kuti sadziwa ntchito, ndiye kuti zinthu sizingakuthereni bwino. Choncho ndi bwino kuchita zinthu mwanzeru. Choyamba afunseni zimene mungachite kuti muzikhoza bwino m’kalasi ndipo muzimvetsera pamene akufotokoza. Solomo analemba kuti: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.” (Ndimaona kuti aphunzitsi athu amachita zinthu mokondera. Taonani zimene zinam’chitikira Rachel. Iye nthawi zonse ankakhoza bwino kwambiri koma atafika kalasi ina zinthu zinasintha. Rachel ananena kuti: “Aphunzitsi athu ankayesetsa mmene angathere kuti andilepheretse.” Koma kodi vuto linali chiyani? Zimene mphunzitsiyo ananena pamaso pa Rachel ndi mayi ake zinasonyeza kuti ankadana ndi chipembedzo chawo.
Kodi iwo anatani atamva zimenezi? Rachel anati: “Nthawi iliyonse imene aphunzitsi andilepheretsa chifukwa chodana ndi chipembedzo
changa, amayi anga ankapita kukakambirana nawo. M’kupita kwa nthawi, anasiya kundivutitsa.” Ngati zimenezi zitakuchitikirani muyenera kulimba mtima n’kuwauza makolo anu. Makolo anuwo akhoza kukalankhulana ndi aphunzitsiwo kapena ahedi kuti aone mmene angathetsere vutolo.Muziona Patali
N’zoona kuti mavuto ena sangathe msanga moti nthawi zina mungafunike kungopirira. Tanya ananena kuti: “Aphunzitsi athu ena anali ovuta. Nthawi zambiri ankangotikalipira komanso kutinena kuti ndife zitsiru. Poyamba ndinkalira akatinena zimenezi koma kenako ndinaona kuti ndi bwino ndisamazitengere kwambiri. Ndinkangopiritiriza zomwe andiuza kuti ndichite ndiponso ndinkayesetsa kumvetsera kwambiri akamaphunzitsa. Zimenezi zinachititsa kuti asamandivutitse kwambiri ndiponso ndinakhala m’gulu la ana ochepa omwe ankakhoza bwino phunziro lawo. Patadutsa zaka ziwiri, aphunzitsiwo anachotsedwa ntchito.”
Ngati mutayesetsa kupirira zinthu zoipa zimene aphunzitsi anu amakuchitirani, mukhoza kuphunzira zinthu zimene zingadzakuthandizeni kwambiri mukadzayamba ntchito n’kukhala ndi bwana wovuta. Zingakuthandizeninso kulemekeza kwambiri aphunzitsi abwino, ngati atakhalapo.
Kodi mumaona kuti nthawi imakucheperani? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe mungachite kuti muzikhala ndi nthawi.
LEMBA
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Mateyu 7:12.
MFUNDO YOTHANDIZA
Ngati mukuona kuti zochita za aphunzitsi anu zimakukwanani, muzingoganizira kwambiri zomwe akuphunzitsazo osati iwowo. Muzilemba notsi, kufunsa mwaulemu pamene simunamvetse ndiponso muzimvetsera mwatcheru. Mukamachita zimenezi anzanunso adzayamba kukhala tcheru m’kalasi.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Aphunzitsi anuwo akhala akuphunzitsa zinthu zomwezomwezo kwa nthawi yaitali ndiponso kwa ana osiyanasiyana. Zimenezi zingachititse kuti atope nalo phunzirolo n’kuyamba kuphunzitsa zosagwira mtima kwenikweni ngati mmene ankachitira poyamba.
ZOTI NDICHITE
Kuti zimene aphunzitsi akuphunzitsa ndisamazione ngati zotopetsa, ndizichita izi: ․․․․․
Ngati ndaona kuti aphunzitsi anga andichitira zinthu zopanda chilungamo, ndidzachita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani ndi bwino kumaganizira kwambiri zimene aphunzitsi akuphunzitsa m’malo moganizira kwambiri za iwowo?
● Kodi mmene mumaonera phunziro linalake zingakhudze bwanji mmene mphunzitsi yemwe amaphunzitsa phunzirolo amakuonerani inuyo?
[Mawu Otsindika patsamba 146]
“Ndinayesetsa kwambiri kuti ndizigwirizana ndi aphunzitsi onse. Ndinapeza njira yodziwira mayina awo, ndipo panopa ndikakumana nawo panjira ndimawapatsa moni komanso kucheza nawo pang’ono.”—Anatero Carmen
[Chithunzi patsamba 145]
Aphunzitsi ali ngati miyala yowolokera kuchoka ku umbuli. Mungapindule ndi miyalayi ngati mukuyenda