3
Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?
KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?
Taganizirani izi: Ndi Lachitatu madzulo ndipo mnyamata wina wazaka 17, dzina lake Geoffrey wamaliza kugwira ntchito zapakhomo. Iye akuona kuti tsopano ndi nthawi yoti apume n’kumaonera TV.
Choncho akuyatsa TV n’kukhala pampando. Koma nthawi yomweyo bambo ake akutulukira ndipo akuoneka kuti akudabwa ndiponso sakusangalala.
Bambowo akunena kuti: “Geoff! Ukutani apa m’malo moti uzikamuthandiza mng’ono wako kulemba homuweki? Iwe koma umamva?”
Geoffrey akunena chapansipansi kuti : “Ehe zayambika.”
Bambowo akunena kuti: “Geoff wati chani?”
Geoffrey akuyankha kuti: “Palibe.”
Bambo ake akwiya koopsa ndipo akunena kuti: “Usadzandilankhulenso choncho wamva?”
Kodi mukanakhala Geoffrey mukanatani kuti zoterezi zisachitike?
MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA
Kulankhulana ndi makolo anu tingakuyerekezere ndi kuyendetsa galimoto. Ngati mutapeza kuti msewu watsekedwa, mukhoza kungodzera msewu wina. Msewu ukatsekedwa mukhoza kupeza njira ina imene mungadutse. Choncho n’zothekanso kupeza njira ina yolankhulirana ndi makolo anu
CHITSANZO:
Mtsikana wina dzina lake Leah anati: “Bambo anga ndi ovuta. Nthawi zina ndikamawafotokozera zinazake ndimangowamva akuti: ‘Ee? Ukuti chiyani?’”
PALI NJIRA ZITATU ZIMENE LEAH ANGATSATIRE.
-
YOYAMBA. Kuwalusira bambo akewo.
Leah akunena mopsa mtima kuti, “Kodi simukumvetsera bwanji? Mukuona ngati ndi nkhani yaing’ono?”
-
YACHIWIRI. Kusiya kulankhula nawo.
Leah wangosiya kuwafotokozera nkhaniyo.
-
YACHITATU. Kudikira kaye n’kudzakambirana nawo nthawi ina.
Leah akupeza nthawi ina yabwino n’kulankhula nawo kapena akungowalembera kalata yowafotokozera zimene amafuna kuwauza.
Kodi inuyo mukuganiza kuti njira yabwino imene Leah angatsatire ndi iti?
TAGANIZIRANI IZI: Bambo a Leah atanganidwa ndi zinazake ndiye sakudziwa mmene Leah akumvera mumtima mwake. Leah atasankha Njira Yoyambayi, bambo akewo sangadziwe chifukwa chimene walusira ndipo sangamve zimene amafuna kuwauza. Komanso zingasonyeze kuti salemekeza bambo akewo. (Aefeso 6:2) Choncho, njira imeneyi singathandize ngakhale pang’ono.
Njira Yachiwiriyi ikhoza kukhala yosavuta koma si yanzeru. Tikutero chifukwa chakuti popanda kuwafotokozera vuto lakelo, iwo sangadziwe zimene zikumuchitikira ndipo sangamuthandize. Choncho, kusiya kulankhula nawo n’kosathandiza.
Koma potsatira Njira Yachitatu, Leah sakulola kuti kusamvetsera kwa bambo ake kumupangitse kuti asalankhule nawonso. M’malomwake iye wasankha kulankhula nawo pa nthawi ina. Ndipo kulembera kalata bambo akewo kungathandize kuti iyeyo ayambe kumva bwino.
Kulemba kalata kungathandizenso kuti afotokoze bwinobwino vuto lake. Bambo ake akawerenga kalatayo akhoza kumvetsa maganizo ake komanso mmene akumvera mumtima mwake. Choncho Njira Yachitatu ndi yothandiza kwa Leah komanso kwa bambo akewo. Kaya alankhula nawo pamasom’pamaso kapena alemba kalata, ndiye kuti watsatira malangizo a m’Baibulo akuti “titsatire zinthu zobweretsa mtendere.”—Aroma 14:19.
Kodi pali njira zinanso zimene Leah angatsatire?
Ganizirani njira imodzi. Kenako ganizirani zimene zingachitike atatsatira.
MUZISAMALA POLANKHULA NDI MAKOLO ANU
Dziwani kuti mukhoza kunena zinthu zina, makolo anu n’kumva zina.
MWACHITSANZO:
Makolo anu akufunsani kuti ‘Wakhumudwa ndi chiyani?’ Ndiyeno inu n’kuyankha kuti, “Palibe.”
Makolo anuwo angaganize kuti mukutanthauza zoti “Sindingakuuzeni chifukwa sindimakukhulupirirani. Ndikauza anzanga chifukwa ndi amene angandithandize.”
Ndiye tiyerekeze kuti muli ndi vuto linalake ndipo makolo anu akufuna kukuthandizani. Koma inuyo mukuti: “Musadandaule. Ndithana nazo ndekha.”
-
Kodi makolo anu angaganize chiyani?
-
Kodi yankho labwino lingakhale loti chiyani?