MUTU 16
Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena
1-3. (a) Kodi Esitere ankamva bwanji pamene ankayandikira mpando wachifumu wa mwamuna wake? (b) Kodi mfumu inachita chiyani Esitere atafika pafupi ndi mpando wake?
MTIMA wa Esitere unkagunda kwambiri pamene ankayandikira pomwe mfumu inakhala. Yerekezerani kuti mukumuona akulowa m’nyumba yachifumu, yomwe inali ku Susani ku Perisiya ndipo anthu onse akukhala chete moti Esitere akutha kumva kaphokoso ka mapazi ake komanso ka zovala zake zachifumu. Nyumba yachifumuyi inali yaikulu kwambiri ndipo makoma ake anali omangidwa mochititsa chidwi. Komanso inali yokongoletsedwa ndi matabwa a mkungudza ochokera ku Lebanoni. Koma Esitere sanachite chidwi kwambiri ndi zimenezi. Maso ake onse anali pa mfumu chifukwa ankadziwa kuti zimene mfumuyo ingachite zingachititse kuti aphedwe kapena ayi.
2 Mfumuyo inkangomuyang’anitsitsa pamene ankayandikira ndipo kenako inamuloza ndi ndodo yake yachifumu yagolide. Zimene mfumu inachitazi zingaoneke ngati nkhani yaing’ono koma zinali zofunika kwambiri popeza zinachititsa kuti Esitere asaphedwe chifukwa cha mlandu umene wapalamula. Mlandu wake unali woti iye wakaonekera pamaso pa mfumuyo asanaitanidwe. Atafika pamene panali mfumuyo, Esitere anagwira pamwamba pa ndodoyo posonyeza kuyamikira.—Esitere 5:1, 2.
3 Ahasiwero ankachita kuonekeratu kuti anali wolemera kwambiri komanso mfumu yamphamvu. Akatswiri amaphunziro amanena kuti zovala za mafumu a ku Perisiya a nthawi imeneyo zinali zapamwamba kwambiri moti panopa mtengo wake ukhoza kukhala madola mamiliyoni ambiri. Koma ngakhale zinali choncho, Esitere anaona kuti Ahasiwero ankamukondabe. Ahasiwero anati: “Chavuta n’chiyani Mfumukazi Esitere, ndipo ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu, ipatsidwa kwa iwe.”—Esitere 5:3.
4. Kodi Esitere ankafunika kuchita zinthu zovuta ziti?
4 Zimene Esitere anachitazi, pokaonekera kwa mfumu ndi cholinga choti akateteze anthu a mtundu wake ku chiwembu chofuna kuwapha onse, zinasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro komanso anali wolimba mtima. Koma ngakhale kuti zinatheka kuonana ndi mfumuyi, panali
padakali zinthu zina zovuta kwambiri zoti achite. Iye anafunika kufotokoza momveka bwino kwa mfumu yomva zake zokhayi kuti izindikire kuti mlangizi wake Hamani, amene inkamudalira kwambiri, anali atainamiza n’cholinga choti ilamule zoti anthu a mtundu wa Esitere aphedwe. Kodi Esitere akanafotokoza bwanji zimenezi momveka bwino, ndipo tingaphunzirepo chiyani pa chikhulupiriro chake?Anasankha Mwanzeru “Nthawi Yolankhula”
5, 6. (a) Kodi Esitere anatsatira bwanji mfundo yopezeka pa Mlaliki 3:1, 7? (b) Pamene Esitere ankalankhula ndi mwamuna wake, kodi anasonyeza bwanji kuti anali munthu wanzeru?
5 Kodi Esitere akanangofikira kufotokozera mfumuyo nkhani imene wabwerera pamaso pa anthu onse ogwira ntchito m’nyumba ya mfumuyo? Kuchita zimenezi kukanachititsa manyazi mfumuyo komanso kukanachititsa Hamani kuyamba kudziikira kumbuyo. Ndiyeno kodi Esitere anatani? Zaka zambiri izi zisanachitike, mfumu yanzeru Solomo inauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:1, 7) Tikukhulupirira kuti Moredekai, munthu wokhulupirika yemwe analera Esitere ngati mwana wake weniweni, ankamuphunzitsa mtsikanayu mfundo ngati zimenezi. Choncho Esitere ankadziwa kufunika kosankha bwino “nthawi yolankhula.”
6 Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, lero inu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ine ndakukonzerani.” (Esitere 5:4) Mfumuyo inagwirizana nazo ndipo inaitana Hamani kuti abwere kuphwandoko. Pamenepatu Esitere analankhula mwanzeru. Iye anamusungira mwamuna wake ulemu ndipo anakonza nthawi yabwino yoti amufotokozere nkhawa zimene anali nazo.—Werengani Miyambo 10:19.
7, 8. Kodi Esitere anakonza zotani paphwando loyamba, ndipo n’chifukwa chayani sanauze mwamuna wake nthawi yomweyo zimene ankafuna?
7 N’zachidziwikire kuti Esitere anakonza phwandolo mosamala kwambiri ndipo anaonetsetsa kuti chakudya chaphikidwa mogwirizana ndi zimene mwamuna wake amakonda. Anakonza zoti paphwandolo pakhalenso vinyo n’cholinga choti anthuwo asangalale. (Sal. 104:15) Paphwandolo Ahasiwero anasangalala kwambiri ndipo anafunsanso Esitere kuti anene pempho lake. Kodi imeneyi inali nthawi yabwino yoti Esitere alankhule?
8 Esitere anaonabe kuti imeneyi si nthawi yabwino ndipo anaitaniranso mfumuyo ndi Hamani kuphwando lina tsiku lotsatira. (Esitere 5:7, 8) Kodi n’chifukwa chiyani anadikirabe mpaka tsiku lotsatira? Musaiwale kuti, malinga ndi zimene mfumu inalamula, anthu onse a mtundu wa Esitere anayenera kuphedwa. Choncho, pozindikira kuopsa kwa nkhaniyi, Esitere anafunika kuonetsetsa kuti pempho lake walinena nthawi yabwino. Motero anadikirabe ndipo zimenezi zinachititsa kuti mwamuna wake aone kuti amamulemekeza kwambiri.
9. Kodi kuleza mtima n’kofunika bwanji, ndipo tingatsanzire bwanji Esitere pa nkhani imeneyi?
9 Kuleza mtima ndi khalidwe lofunika kwambiri ngakhale kuti ndi anthu ochepa chabe amene ali nalo. Esitere anali ndi nkhawa komanso ankafunitsitsa kulankhulana ndi mfumu, komabe anadikira nthawi yoyenera. Tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chakechi popeza tonsefe nthawi zina timaona zinthu zina zolakwika ndipo timalakalaka zitakonzedwa. Tikafuna kupempha munthu waudindo kuti akonze zinthu zinazake zomwe zalakwika, tiyenera kukhala oleza mtima potengera chitsanzo cha Esitere. Lemba la Miyambo 25:15 limati: “Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.” Tikaleza mtima mpaka nthawi yoyenera ndipo kenako n’kufotokoza maganizo athu modekha, ngati mmene Esitere anachitira, tikhoza kukopa anthu ovuta kwambiri amene tingawayerekezere ndi fupa. Kodi Yehova Mulungu anadalitsa Esitere chifukwa chochita zinthu moleza mtima komanso mwanzeru?
Kuleza Mtima Kunathandiza Kuti Chilungamo Chichitike
10, 11. (a) Kodi n’chiyani chinakhumudwitsa Hamani pamene ankabwerera kwawo kuchokera kuphwando loyamba, nanga mkazi wake ndi anzake anamuuza kuti achite chiyani?
10 Kuleza mtima kwa Esitere, kunapereka mpata woti zinthu zambiri zichitike. Hamani anachoka paphwando loyamba lija “ali wokondwa komanso akusangalala kwambiri mumtima mwake” poona kuti umenewu ndi umboni wakuti mfumu komanso mkazi wake akusangalala naye kwambiri. Koma pamene Hamani ankadutsa pachipata cha mfumu, anaona Moredekai, Myuda yemwe ankakana kumuweramira uja. Monga taonera m’mutu wapitawu, sikuti Moredekai ankalephera kuweramira Hamani chifukwa chopanda ulemu, koma chifukwa cha chikumbumtima chake komanso ankadziwa mmene zimenezi zingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova Mulungu. Komabe Hamani “anamukwiyira kwambiri” Moredekai.—Esitere 5:9.
11 Hamani anafotokozera mkazi wake komanso anzake zoti Moredekai akukana zoti azimuweramira. Iwo anamuuza kuti akonze mtengo wotalika kuposa mamita 22 ndipo akapemphe chilolezo kwa mfumu kuti apachikepo Moredekai. Hamani anagwirizana ndi maganizo amenewa ndipo nthawi yomweyo anauza munthu kuti akonze mtengowo.—Esitere 5:12-14.
12. (a) N’chifukwa chiyani mfumu inauza anthu kuti aiwerengere mokweza buku limene ankalembamo zochitika za mu ufumuwo? (b) Kodi mfumu inauzidwa zotani zokhudza Moredekai?
12 Baibulo limanena kuti usiku wa tsiku limenelo, “mfumu inasowa tulo.” Zitatero, inauza anthu kuti aiwerengere mokweza buku limene ankalembamo zochitika za mu ufumuwo. Zimene anawerengazo zinaphatikizapo lipoti lokhudza chiwembu chofuna kupha Ahasiweroyo. Mfumu inakumbukira nkhaniyo ndiponso kuti anthu amene anakonza chiwembuwo anagwidwa n’kuphedwa. Koma kodi Moredekai, yemwe anaulula za chiwembucho, anamuchitira chiyani? Mfumuyo itafunsa za nkhaniyi inauzidwa kuti Moredekai sanamuchitire chilichonse.—Werengani Esitere 6:1-3.
13, 14. (a) Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Hamani? (b) Kodi Hamani anauzidwa chiyani ndi mkazi wake komanso anzake?
13 Mokwiya, mfumuyo inafunsa ngati pali nduna iliyonse pafupi yoti aitume kuchita zimene anaiwalazo. Nduna imene inali pafupi inali Hamani. Zikuoneka kuti Hamani ndi amene anayambirira kufika kunyumba ya mfumuyo chifukwa ankafuna kukapempha chilolezo choti aphe Moredekai. Koma iye asanapemphe zimenezi, mfumuyo inamufunsa zomwe angachitire munthu amene mfumu ikukondwera naye. Hamani anaganiza kuti munthu wake ndi iyeyo. Choncho anakonza zoti munthuyo achitiridwe zinthu zapamwamba kwambiri. Iye anauza mfumuyo kuti munthuyo avekedwe zovala zachifumu, akwezedwe pahatchi imene mfumu imakwera ndipo mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu amuyendetse kuzungulira mzinda wonse wa Susani n’kumanena mawu otamanda munthuyo mofuula. Taganizirani mmene nkhope ya Hamani inasinthira atamva kuti munthu woyenera kupatsidwa ulemuyo anali Moredekai. Ndipotu munthu amene mfumuyo inamulamula kuti azikafuula zotamanda Moredekai anali Hamani yemweyo.—Esitere 6:4-10.
14 Mokakamizika, Hamani anachitabe zimene anauzidwazo ndipo atamaliza, anabwerera kunyumba kwake mofulumira komanso atakhumudwa kwambiri. Mkazi wake ndi anzake anamuuza kuti pamenepa zaonekeratu kuti sizimuthera bwino ndipo iye sapambana pa nkhondo yake yolimbana ndi Moredekai.—15. (a) Kodi kuleza mtima kwa Esitere kunali ndi ubwino wotani? (b) N’chifukwa chiyani ndi bwino kuti ifenso ‘tiziyembekezera moleza mtima’?
15 Chifukwa chakuti Esitere anadikiranso tsiku lina asanauze mfumuyo pempho lake, zinachititsa kuti Hamani achite zinthu zomwe zinamubweretsera yekha mavuto. N’kutheka kuti Yehova Mulungu ndi amene anachititsa kuti mfumuyo isowe tulo. (Miy. 21:1) N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuyembekezera moleza mtima.’ (Werengani Mika 7:7.) Tikamayembekezera kuti Mulungu atithandize pa mavuto athu, tidzaona kuti iye amapeza njira yabwino yothetsera mavuto yoposa imene ifeyo tikanatsatira.
Analankhula Molimba Mtima
16, 17. (a) Kodi Esitere anadziwa bwanji kuti tsopano ndi “nthawi yolankhula”? (b) Kodi Esitere ankasiyana bwanji ndi Vasiti, amene anali mkazi woyamba wa mfumu?
16 Esitere anaona kuti si bwino kuti mfumuyo izingodikirabe kuti aiuza zotani. Choncho, paphwando lotsatira, iye anaona kuti ayenera kufotokoza zonse. Koma kodi akanayambira pati? Mwamwayi, mfumuyo inamufunsanso kuti afotokoze pempho lake. (Esitere 7:2) Esitere anaona kuti tsopano imeneyi ndi “nthawi yolankhula.”
17 N’kutheka kuti Esitere anapemphera chamumtima kwa Mulungu wake asanauze mfumu mawu awa: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomereni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.” (Esitere 7:3) Onani kuti iye anasonyeza kuti ankalemekeza zimene mfumuyo ingalamule malinga ndi zomwe iyoyo yaona kuti n’zoyenera. Zimene Esitere anachitazi zinasonyeza kuti anali wosiyana kwambiri ndi Vasiti, mkazi wakale wa mfumuyi, amene anachititsa manyazi mfumuyi mwadala. (Esitere 1:10-12) Komanso, Esitere sananyoze mfumuyi chifukwa chokhulupirira zinthu zabodza zimene Hamani anaiuza. M’malomwake, anapempha mfumuyo kuti imuteteze kuti asaphedwe.
18. Kodi Esitere anafotokoza bwanji vuto lake kwa mfumu?
18 Pempho limeneli linadabwitsa kwambiri mfumuyo komanso inaona kuti iyeneradi kuchitapo kanthu. Ndipotu palibe mwamuna amene angalekerere kuti mkazi wake aphedwe. Esitere anapitiriza kufotokoza kuti: “Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa. Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna ndi akapolo akazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.” (Esitere 7:4) Onani kuti Esitere anafotokoza zokhudza chiwembucho momveka bwino koma ananenanso kuti zikanakhala kuti iwo anangokhala akapolo chabe, iye sakanadandaula chilichonse. Komano popeza kuti kupha mtundu wonse kukanakhudzanso kwambiri mfumuyo, iye anaona kuti si bwino kungokhala chete.
19. Kodi chitsanzo cha Esitere chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kulankhula mogwira mtima?
19 Chitsanzo cha Esitere chikutiphunzitsa njira yabwino yofotokozera maganizo athu mogwira mtima. Ngati mukufuna kufotokoza vuto linalake kwa munthu amene mumam’konda kapena kwa munthu waudindo, kuchita zinthu moleza mtima, mwaulemu, komanso kutchula vutolo mosapita m’mbali, kungakuthandizeni kwambiri.—Miy. 16:21, 23.
20, 21. (a) Kodi Esitere anaulula bwanji Hamani, ndipo mfumu inatani itamva zimenezi? (b) Kodi Hamani anatani atadziwika kuti ndi woipa?
20 Ndiyeno Ahasiwero anafunsa kuti: “Ndani wachita zimenezi, ndipo ali kuti munthu amene wadzikuza ndi kuchita zinthu zoterezi?” Yerekezerani kuti mukuona Esitere akuloza n’kuyankha kuti: “Munthu wake ndi Esitere 7:5-7.
uyu, Hamani, mdani ndiponso munthu woipa.” Hamani anangoti kukamwa yasaa ndipo anachita mantha kwambiri. N’kutheka kuti nkhope ya mfumuyo inafiira chifukwa cha mkwiyo itazindikira kuti Hamani, mlangizi wake amene inkamukhulupirira, anali ataipusitsa n’kuichititsa kusainira lamulo limene likanachititsa kuti mkazi wake wokondedwa aphedwe. Mfumuyi inachoka paphwandoli n’kupita kumunda wamaluwa kuti mtima wake ukakhale m’malo.—21 Hamani atadziwika kuti anali munthu woipa, anagwada pafupi ndi mapazi a mfumukazi n’kuyamba kuichonderera kwambiri. Ndiyeno pamene mfumu inalowanso m’nyumba muja n’kuona Hamani ali pafupi ndi Esitere, inakwiya kwambiri chifukwa inaona ngati Hamani akufuna kugwiririra Esitereyo m’nyumba mwake momwe. Apa zinaonekeratu kuti Hamani sapulumuka. Hamani anachotsedwa m’nyumbamo atamuphimba nkhope. Kenako nduna ina inauza mfumu za mtengo waukulu uja, umene Hamani ankafuna kupachikapo Moredekai. Ahasiwero atangomva zimenezi, analamula kuti Hamani akapachikidwe pamtengowo.—Esitere 7:8-10.
22. Kodi chitsanzo cha Esitere chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kufunika kokhalabe ndi chikhulupiriro choti Mulungu atithandiza?
22 Masiku ano kupanda chilungamo kuli ponseponse. Choncho pakakhala nkhani inayake imene sinayende mwachilungamo, n’zosavuta kuyamba kuganiza kuti chilungamo cha nkhaniyo sichidzadziwika. Kodi inunso munayamba mwaganizapo choncho? Koma monga taonera, Esitere sanataye mtima ndipo anakhalabe ndi chikhulupiriro choti Mulungu amuthandiza. Nthawi yoti alankhule itakwana, iye analankhula molimba mtima komanso analankhula chilungamo chokhachokha. Ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza kuti chilungamo chioneke. Nafenso tizichita chimodzimodzi. Yehova sanasinthe ndipo amathabe kuchititsa kuti anthu oipa agwere mumsampha wotchera okha ngati mmene zinachitikira ndi Hamani.—Werengani Salimo 7:11-16.
Anaimira Yehova ndi Anthu Ake
23. (a) Kodi mfumu inapatsa chiyani Esitere ndi Moredekai? (b) Kodi ulosi wonena za Benjamini umene Yakobo anena atatsala pang’ono kumwalira unakwaniritsidwa bwanji? (Onani bokosi lakuti “ Ulosi Unakwaniritsidwa.”)
23 Tsopano mfumu inadziwa kuti Moredekai, yemwe anaipulumutsa kwa anthu amene ankafuna kuipha, analinso bambo a Esitere omulera. Ahasiwero anapatsa Moredekai udindo umene unali wa Hamani, wokhala nduna yaikulu. Komanso anapatsa Esitere nyumba ya Hamani ndi chuma chake Esitere 8:1, 2.
chonse ndipo Esitereyo anauza Moredekai kuti aziyang’anira zinthuzo.—24, 25. (a) N’chifukwa chiyani Esitere ataulula Hamani sanaone kuti nkhani yathera pompo? (b) Kodi Esitere anachita chiyani chomwe chinaikanso moyo wake pa ngozi?
24 Esitere akanakhala kuti sankaganizira anthu ena, akanangosiyira nkhaniyi pomwepo podziwa kuti iyeyo ndi Moredekai zawo zayenda. Koma pa nthawiyi n’kuti lamulo la Hamani lija, lonena kuti Ayuda onse aphedwe, likulengezedwabe m’madera onse a ufumuwo. Hamani anachita Puri, kapena kuti maere, n’cholinga choti adziwe tsiku loyenera kudzachita chiwembu chimenechi. Mwina maere amene anachitawo anali okhudzana ndi zamizimu. (Esitere 9:24-26) Ngakhale kuti kunali kudakali miyezi ingapo kuti tsikulo lifike, Esitere ndi Moredekai anafunika kuchitapo kanthu mwamsanga. Koma kodi iwo akanatani kuti Ayuda asaphedwe?
25 Kachiwirinso, Esitere anaika moyo wake pachiswe n’kukaonekeranso pamaso pa mfumu asanaitanidwe. Iye anachita zimenezi chifukwa choganizira anthu ena. Pa nthawiyi iye analira ndi kuchonderera mwamuna wake kuti asinthe chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda. Koma mu ulamuliro wa Aperisiya, mfumu ikakhazikitsa lamulo silinkasinthidwa. (Dan. 6:12, 15) Choncho, mfumu inapatsa mphamvu Esitere ndi Moredekai yoti akhazikitse lamulo lina latsopano. Iwo anakhazikitsa lamulo lopatsa Ayuda ufulu wodziteteza. Anthu okwera pamahatchi anatumizidwa m’zigawo zonse za ufumuwo kuti akalengeze nkhani yabwinoyi kwa Ayuda. Apa tsopano mitima ya Ayuda inakhala m’malo. (Esitere 8:3-16) Ayuda a m’zigawo zonse za ufumuwo ayenera kuti anayamba kukonzekera nkhondo. Iwo sakanachita zimenezi zikanakhala kuti lamulo latsopanoli silinakhazikitsidwe. Komabe, Ayuda sakanapambana pa nkhondoyi popanda thandizo la Yehova. Koma kodi “Yehova wa makamu” anawathandiza?—1 Sam. 17:45.
26, 27. (a) Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake kuti agonjetseretu adani awo? (b) Kodi kuphedwa kwa ana a Hamani kunakwaniritsa ulosi uti?
26 Tsiku limene Hamani anakhazikitsa lija litakwana, anthu a Mulungu anali atakonzeka kumenya nkhondo. Akuluakulu ena a boma analinso kumbali ya Ayuda popeza zinali zitamveka kuti Moredekai, yemwe anali Myuda, anali ataikidwa kukhala nduna yaikulu. Yehova anathandiza kwambiri anthu ake kuti apambane. Iye anaonetsetsa kuti adani onse a anthu ake agonjetsedwa kuti asadzachitirenso zoipa anthu akewo. *—Esitere 9:1-6.
27 Komabe, Moredekai sakanakhala wotetezeka kuyang’anira nyumba ya Hamani pamene ana 10 a Hamaniyo adakali moyo. Choncho iwonso anaphedwa. (Esitere 9:7-10) Pamenepatu ulosi wina wa m’Baibulo unakwaniritsidwa. Mulungu anali atalosera kuti Aamaleki onse adzawonongedwa chifukwa iwo anasonyeza kuti anali adani oopsa a anthu ake. (Deut. 25:17-19) Ana a Hamani ayenera kuti anali omalizira enieni kuphedwa pa anthu a mtundu woipa umenewu.
28, 29. (a) N’chifukwa chiyani tingati chinali chifuniro cha Yehova kuti Esitere ndi anthu a mtundu wake amenye nkhondo? (b) N’chifukwa chiyani chitsanzo cha Esitere chili chofunika kwambiri kwa ife?
28 Ngakhale kuti Esitere anali wachitsikana, anachita mbali yake pa nkhani yovuta ngati imeneyi. Iye analemba nawo malamulo okhudza nkhondo komanso kupha anthu oipa. Kuchita zimenezi sinali nkhani yamasewera. Komabe zimenezi zinayenera kuchitika ndithu, chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro cha Yehova choti anthu ake asawonongedwe. Mesiya wolonjezedwa, yemwe ndi njira yokhayo yopulumutsira mtundu wonse wa anthu, anali kudzabadwa kudzera mu mtundu wa Isiraeli. (Gen. 22:18) Atumiki a Mulungu masiku ano amadziwa kuti Yesu, yemwe ndi Mesiya, atabwera padziko lapansi, analamula otsatira ake onse kuti asamamenyenso nkhondo.—Mat. 26:52.
29 Komabe Akhristu amamenya nkhondo yauzimu chifukwa kuposa ndi kale lonse, panopa Satana akufunitsitsa kuti atilepheretse kukhulupirira Yehova Mulungu. (Werengani 2 Akorinto 10:3, 4.) Chitsanzo cha Esitere ndi chofunika kwambiri kwa ife. Nafenso tiyenera kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro mwa kulankhula mwanzeru, kuchita zinthu moleza mtima, kukhala olimba mtima komanso kuyesetsa kuthandiza anthu a Mulungu.
^ ndime 26 Mfumu inalola kuti Ayuda amenyenso nkhondo tsiku lotsatira n’cholinga chakuti amalize kugonjetsa adani awo. (Esitere 9:12-14) Mpaka pano, chaka chilichonse Ayuda amakumbukirabe kupambana kumeneku m’mwezi wa Adara womwe ndi chakumapeto kwa mwezi wa February ndi kumayambiriro kwa March. Mwambowu umatchedwa Purimu ndipo anaupatsa dzina limeneli potengera dzina la maere amene Hamani anachita aja.