Chilungamo
Ndi ndani yekha amene ali ndi ulamuliro wonena zimene zili zoyenera kapena zolungama?
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ge 18:23-33—Yehova anaonetsa Abulahamu kuti Iye ndi woweruza wachilungamo
-
Sl 72:1-4, 12-14—Wamasalimo anauziridwa kulemba zotamanda Mesiya kuti idzakhala Mfumu yachilungamo ngati Yehova
-
Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo zolungama za Yehova?
Sl 37:25, 29; Yak 5:16; 1Pe 3:12
Onaninso Sl 35:24; Yes 26:9; Aro 1:17
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Yob 37:22-24—Elihu anatamanda chilungamo cha Yehova, yemwe amachititsa kuti atumiki ake azimulemekeza chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa
-
Sl 89:13-17—Wamasalimo anatamanda Yehova chifukwa cha ulamuliro wake wachilungamo
-
Kodi kufunafuna chilungamo cha Mulungu kutanthauza chiyani?
Eze 18:25-31; Mt 6:33; Aro 12:1, 2; Aef 4:23, 24
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Ge 6:9, 22; 7:1—Nowa anasonyeza kuti anali wolungama potsatira mosamala zonse zimene Yehova anamupempha kuti achite
-
Aro 4:1-3, 9—Yehova anaona Abulahamu kukhala wolungama chifukwa anasonyeza kuti amamukhulupirira kwambiri
-
N’chifukwa chiyani chilungamo chathu chiyenera kusonyeza kuti timakonda Yehova m’malo mongofuna kudzionetsera kuti ndife olungama pamaso pa anthu?
Mt 6:1; 23:27, 28; Lu 16:14, 15; Aro 10:10
-
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
-
Mt 5:20; 15:7-9—Yesu anauza anthu kuti asamasonyeze chilungamo chawo potengera mfundo zimene alembi ndi Afarisi ankatsatira chifukwa anali achinyengo
-
Lu 18:9-14—Yesu ananena fanizo pofuna kudzudzula anthu amene ankafuna kudzionetsera kuti ndi olungama kwambiri kuposa anzawo
-
N’chifukwa chiyani kukhala wabwino kumaposa kukhala wolungama?
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kudziona ngati ndife olungama komanso kupewa kuchita zinthu modzionetsera kuti ndife olungama kwambiri kuposa ena?