CHIGAWO 7
Kodi Yesu Anali Ndani?
Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi. 1 Yohane 4:9
Ngati tikufuna kukondweretsa Yehova, tiyenera kumvera munthu winanso wofunika kwambiri. Kale kwambiri Yehova asanalenge Adamu, analenga mngelo wamphamvu kwambiri kumwamba.
Patapita nthawi, Yehova anatumiza mngelo ameneyu kudzabadwa ngati mwana ku Betelehemu kwa namwali wina dzina lake Mariya. Mwana ameneyo anam’patsa dzina lakuti Yesu.—Yohane 6:38.
Ali padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Mulungu. Iye anali wachifundo, wachikondi ndiponso anthu ankafika kwa iye momasuka. Ankaphunzitsa anthu choonadi chonena za Yehova mopanda mantha.
1 Petulo 2:21-24
Yesu ankachita zinthu zabwino koma anthu ankadana naye.Yesu anachiritsanso odwala ndi kuukitsa anthu ena amene anafa.
Atsogoleri a chipembedzo ankadana ndi Yesu chifukwa iye ankaulula zochita zawo zoipa ndipo ankaululanso kuti iwo ankaphunzitsa zinthu zabodza.
Atsogoleri a chipembedzo anachititsa Aroma kuti amenye ndi kupha Yesu.