Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 127

Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato

Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato

MATEYU 27:1-11 MALIKO 15:1 LUKA 22:66–23:3 YOHANE 18:28-35

  • YESU ANAIMBIDWANSO MLANDU NDI KHOTI LA SANIHEDIRINI M’MAWA

  • YUDASI ISIKARIYOTI ANADZIMANGIRIRA

  • YESU ANATUMIZIDWA KWA PILATO KUTI AKAIMBIDWE MLANDU

Pamene Petulo ankakana Yesu kachitatu n’kuti kutatsala pang’ono kucha. Oweruza a khoti la Sanihedirini omwe ankaimba Yesu mlandu mosatsatira malamulo anali atamaliza kuweruza mlanduwu komanso anali atabwerera kwawo. Pofika m’mawa, lomwe linali tsiku Lachisanu, oweruza aja anakumananso. Iwo anakumana pofuna kuchititsa anthu kuganiza kuti mlandu wa Yesu waweruzidwa m’mawa wa Lachisanulo potsatira malamulo. Anthuwa anabweranso ndi Yesu pa nthawi imeneyi.

Apanso anthuwa anafunsa Yesu kuti: “Tiuze ngati ndiwe Khristu.” Koma Yesu anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira. Komanso nditakufunsani, simungathe n’komwe kuyankha.” Komabe Yesu anawafotokozera molimba mtima kuti iyeyo ndi ndani mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kale m’buku la Danieli pa Danieli 7:13. Yesu ananena kuti: “Kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.”—Luka 22:67-69; Mateyu 26:63.

Anthuwo anapitirizabe kumufunsa kuti: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Yesu anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha kuti ndine amene.” Zikuoneka kuti Yesu atanena mawu amenewa, anthuwo anapeza chifukwa chomveka chomuimba mlandu wonyoza Mulungu n’cholinga choti amuphe. Anthuwa anafunsa kuti: “Tifuniranjinso umboni wina?” (Luka 22:70, 71; Maliko 14:64) Pamenepo anamanga Yesu n’kupita naye kwa wolamulira wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato.

Mosakayikira Yudasi Isikariyoti anaona anthu amene anabwera kudzagwira Yesu akumutenga n’kupita naye kwa Pilato. Atazindikira kuti Yesu waweruzidwa kuti ayenera kuphedwa, anamva chisoni komanso kudziimba mlandu. Koma m’malo molapa kwa Mulungu, Yudasi anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija. Iye anauza ansembe aakulu kuti: “Ndachimwa popereka munthu wolungama.” Koma anthuwa sanamumvere chisoni moti anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”—Mateyu 27:4.

Kenako Yudasi anaponya ndalama 30 zasiliva zija m’kachisimo ndipo anakonza zongodzipha. Pamene ankadzimangirira, nthambi ya mtengo umene anamangapo chingwe inathyoka ndipo anagwera pamiyala moti anaphulika.—Machitidwe 1:17, 18.

Pamene anthuwo ankapita ndi Yesu kunyumba kwa Pontiyo Pilato n’kuti kudakali m’mawa. Koma Ayuda amene anamutengawo anakana kulowa m’nyumba chifukwa ankaona kuti kulowa m’nyumba ya munthu yemwe sanali Myuda kukanawachititsa kuti akhale odetsedwa. Ndipo ngati akanakhala odetsedwa, sakanayenera kudya nawo chakudya cha pa Nisani 15, lomwe linali tsiku loyamba la Chikondwerero cha Mkate Wopanda Chofufumitsa. Chikondwererochi chinkachitikanso pa nthawi imene ankachita mwambo wa Pasika.

Ndiyeno Pilato anatuluka m’nyumba yake n’kufunsa anthuwo kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?” Anthuwo anayankha kuti: “Munthu uyu akanakhala wosachita zoipa, sitikanabwera naye kwa inu.” N’kutheka kuti Pilato anaona kuti anthuwo akumukakamiza kuchita zimene iyeyo sakufuna, choncho ananena kuti: “M’tengeni eniakenu mukamuweruze mogwirizana ndi chilamulo chanu.” Zimene Ayudawo anayankha zinasonyeza kuti ankafunadi kupha Yesu chifukwa ananena kuti: “N’zosaloleka kwa ife kupha munthu aliyense.”—Yohane 18:29-31.

Ngati Ayuda akanapha Yesu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika anthu akanachita zachipolowe. Koma ngati Ayudawo akanachititsa Aroma kuti aphe Yesu pa mlandu woukira boma, ndiye kuti anthu sakanawaimba mlandu. Pa nthawiyi Aroma ankaloledwa kupha munthu ngati waukira boma.

Atsogoleri achipembedzo sanauze Pilato kuti anali atapeza Yesu ndi mlandu wonyoza Mulungu. Choncho anayamba kupeka zifukwa zina. Iwo ananena kuti: ‘Ife tapeza munthu uyu [1] akupandutsa mtundu wathu, [2] akuletsa anthu kuti asamakhome msonkho kwa Kaisara, komanso [3] akunena kuti ndi Khristu mfumu.’—Luka 23:2.

Pilato, yemwe ankaimira ulamuliro wa Aroma, anada nkhawa kwambiri atamva kuti Yesu ankanena kuti ndi mfumu. Pilato analowanso m’nyumba mwake kenako anaitana Yesu n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Pofunsa funso limeneli, zinali ngati Pilato akufunsa kuti, ‘Kodi ukuphwanya dala lamulo la mu ufumu wa Aroma ponena kuti ndiwe mfumu pomwe mfumu ina ilipo kale, yomwe ndi Kaisara?’ Yesu ankafuna kudziwa kuti Pilato anamva zotani zokhudza iyeyo, choncho anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi mukunena nokha, kapena ena akuuzani za ine?”—Yohane 18:33, 34.

Pilato anayankha ngati kuti sankadziwa kena kalikonse kokhudza Yesu koma anasonyeza ngati ali ndi chidwi choti amudziwe. Iye anayankha Yesu kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati?” Ananenanso kuti: “Anthu a mtundu wako omwe ndi ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine. Kodi unachita chiyani?”—Yohane 18:35.

Yesu sanayese kuthawa nkhani yonena za Ufumu ndipo zimene anayankha zinadabwitsa kwambiri Pilato.