Kodi Amwenye a ku Brazil Adzatha Onse?
Kodi Amwenye a ku Brazil Adzatha Onse?
YOLEMBEDWA KU BRAZIL
KU BRAZIL kuli dera linalake lotetezerako zachilengedwe (lotchedwa Xingu National Park) lomwe limapezeka m’boma la Mato Grosso. Derali n’lalikulu makilomita 27,000, moti lingalowe kanayi m’dziko la Malawi. Kumeneku kumakhala amwenye pafupifupi 3,600 a m’mafuko 14. Malowa ndi owirira kwambiri ndipo amaoneka okongola kwambiri pa zithunzi zimene anthu amajambula ali m’mlengalenga. Nkhalango zina zozungulira derali anaziyatsa kuti asavutike podula mitengo yogulitsa kapena pokonza malo odyetsera ng’ombe zambirimbiri zimene amaweta.
M’ma 1960 boma la Brazil linayamba kukhazikitsa midzi yoti kuzikhala amwenye. Midzi imeneyi imapezeka makamaka m’dera la Amazon, ndipo panopa yatenga gawo lalikulu ndithu moti titagawa dziko la Brazil m’zigawo 10, derali lingakhale lalikulu kuposa gawo limodzi lotere. Kuika amwenyewa m’midzi kwachititsa kuti ayambe kuchulukana. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri chifukwa choti aka n’koyamba kuti amwenyewa ayambe kuchulukana, kuchokera pa zaka 500 zapitazo. Akuti panopo mwina amwenyewa alipo 300,000. Komatu ichi ndi chiwerengero chochepa kwambiri kuyerekezera ndi chiwerengero cha m’chaka cha 1500 chifukwa akuti panthawiyi amwenyewa anali pafupifupi 2 miliyoni kapena mwinanso 6 miliyoni.
M’zaka 500 zapitazi, pachitika zinthu zimene wolemba wina ananena kuti “n’zoopsa kwambiri chifukwa zinapulula amwenyewa.” Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti amwenyewa apululuke chonchi? Kodi tsopano n’zotsimikizika kuti amwenyewa satha onse chifukwa choti chiwerengero chawo chayamba kukwera?
Kufika kwa Atsamunda
M’zaka 30 kuchokera mu 1500, pamene dziko la Portugal linalengeza kuti chigawo cha Brazil chili m’manja mwake, atsamunda Achipwitikiziwa ankalimbana kwambiri ndi zodula mitengo inayake ya kumeneku yomwe amapangira utoto wofiira. Dzina loti Brazil, linachokera ku dzina la mitengo imeneyi. Mitengoyi inali yamtengo wapatali kwambiri ku Ulaya, ndipo azungu ankaigula posinthanitsa ndi tizinthu tawo tachabechabe.
Komabe, posakhalitsa anatulukira kuti ku Brazil ulimi wa nzimbe umayenda bwino kwambiri chifukwa cha nyengo yake. Koma vuto linali loti kulima nzimbe ndi ntchito yofunika anthu ambiri. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kufuna akapolo ochuluka. Atsamundawo sanachite kuvutika n’kukatenga akapolo kutali chifukwa amwenye anali mbwee m’chigawo chonsecho.
Kodi Kugwira Amwenye Ukapolo Kunayamba Bwanji?
Pachikhalidwe chawo, amwenyewa ankalima mbewu zoti azidya basi. Ntchito ya amuna inali yosaka nyama ndi kuwedza nsomba ndipo ankagwiranso ntchito yakalavulagaga yoswa mphanje. Akazi ndiwo ankadzala, kukolola, ndi kukonza chakudya. Azungu ophunzira kwambiri ankatama amwenyewa chifukwa cha moyo wawo wosakonda ndalama ndiponso wosalira zambiri. Koma atsamunda ambiri ankaona amwenyewa ngati anthu aulesi basi.
Amwenye amene sankadana ndi atsamundawo ankawanyengerera kuti asamukire m’madera a kufupi ndi malo amene Apwitikizi anakhazikikako kuti azikawagwirira ntchito ndi kuwateteza. Akatolika a chipani cha Ajezuwiti ndi zipani zina zotere ndiwo anathandiza kwambiri ponyengerera amwenyewa. Komatu iwowa sanadziwe kuti zimenezi zidzalowetsa amwenyewa m’mavuto aakulu kwambiri. Atsamundawo ankakakamiza amwenyewo kugwira ntchito ngati akapolo ngakhale kuti malamulo a boma ankati amwenyewo anali ndi ufulu ndiponso anali ndi mphamvu pa malo awo onse. Nthawi zambiri sankalipidwa ngakhalenso kuloledwa kukhala ndi minda yawoyawo.
Boma lachifumu la Portugal linayesa kuika malamulo oletsa ukapolo umenewu koma silinaphule kanthu. Atsamunda ambiri ankapeza njira zina zozembera malamulowa. Panthawiyi, atsamunda ambiri sankaona kuti kunali kulakwa ngati agonjetsa amwenye enaake pankhondo, n’kuwagwira ukapolo kapena kuwagulitsa. Nkhondo zoterezi ankazitcha kuti nkhondo zovomerezeka. Atsamundawo ankagula amwenye amene agwidwa ukapolo ndi mitundu ina ya amwenye ndipo nthawi zina ankalungamitsa khalidweli ponena kuti kwenikweni anali kuwawombola akapolowo m’manja mwa adani awo.
Motero, tingati chifukwa chachikulu chimene chinathandiza kuti utsamunda upite patsogolo kumeneku chinali ulimi wa nzimbe, zomwe ankapangira shuga. Ndipo panthawiyi ntchito imeneyi siikanayenda popanda akapolo. Choncho nthawi zambiri boma lachifumu la Portugal linkalephera kuchitira mwina koma kungovomereza ukapolo pofuna kupeza ndalama.
Nkhondo Zapakati pa Atsamunda Achipwitikizi ndi Atsamunda Achifalansa ndi Achidatchi
Amwenye ndiwo ankavutika kwambiri chifukwa cha nkhondo za pakati pa atsamunda okhaokha. Afalansa ndi Adatchi ankafuna kulanda dziko la Brazil m’manja mwa Apwitikizi. Motero ankalimbana ndi Apwitikizi poyesa kukopa amwenye kuti akhale kumbali yawo. Amwenyewo sanatulukire kuti cholinga chenicheni cha atsamundawo chinali cholanda dziko lawo. M’malomwake, iwo anaona kuti uwu ndi mwayi wawo woti abwezere zachipongwe zosiyanasiyana zimene anachitidwa ndi mitundu ina ya amwenye anzawo, omwe anali adani awo akalekale. Choncho amwenyewo analowerera mwamtima wonse nkhondo zapakati pa atsamundazo.
Mwachitsanzo, pa November 10, m’chaka cha 1555, Mfalansa wina wolemekezeka dzina lake Nicholas de Villegaignon, anafika ku Guanabara Bay (komwe pano ndi ku Rio de Janeiro) n’kukhazikitsa likulu la asilikali kuti aziteteza derali. Iyeyo anagwirizana ndi amwenye a mtundu wotchedwa Tamoio. Apwitikizi anatenga amwenye a mtundu wotchedwa Tupinamba kuchokera ku Bahia, ndipo mu March 1560, anagonjetsa likulu la asilikali lomwe linkaoneka ngati losagonjetsekalo. Afalansawo anathawa koma anapitirizabe kuchita zamalonda ndiponso kulimbikitsa amwenye amtundu wotchedwa Tamoio aja kumenyana ndi Apwitikizi. Atamenyana nawo kangapo konse amwenyewo anagonja. Akuti pa kumenyana kwina kotereku, amwenye 10,000 anaphedwa ndipo enanso 20,000 anagwidwa ukapolo.
Anabweretsa Nthenda Zoopsa za ku Ulaya
Amwenye analibe matenda ambiri panthawi yoyamba imene anakumana ndi Apwitikizi. Azungu oyamba odzaona malo m’derali ankakhulupirira kuti azigogo ambiri pakati pa amwenyewa anali atakwanitsa zaka 100. Koma matupi a amwenyewa anali asanazolowere matenda a ku Ulaya ndi ku Africa. N’kutheka kuti ichi n’chifukwa chachikulu kwambiri chimene chinachititsa kuti amwenyewa atsale pang’ono kutha onse.
Apwitikizi analemba malipoti osonyeza kuti kunkabuka miliri yosiyanasiyana imene inachepetseratu chiwerengero cha amwenye. Mu 1561, mliri wa nthomba unapulula anthu ku Portugal ndipo unafika mpaka ku Brazil. Kumeneku unapulula anthu mosaneneka. Mkatolika wina wa chipani cha Ajezuwiti, dzina lake Leonardo do Vale, analemba kalata pa May 12, 1563, yomwe inafotokoza mmene mliri umenewu unasakazira anthu ku Brazil. M’kalatamo analemba kuti: “Mliri wa nthomba umenewu unali woipa kwambiri moti palibe munthu amene ankatha kupirira fungo lochokera pathupi la munthu wogwidwa ndi nthendayi. Motero odwala ambiri ankafa ali okhaokha, ndipo ankadyedwa ndi mphutsi zazikulu zedi zomwe zinkangoti nyakanyaka pathupi lawo lonse, moti sanali oti mungawayang’ane kawiri.”
Ajezuwiti Anakhumudwa ndi Maukwati a Pakati pa Amwenye ndi Azungu
Maukwati a pakati pa amwenye ndi azungu anachititsanso kuti mitundu yambiri ya amwenye izimiririke. Buku lina linati: “Apwitikizi ndiponso amwenye a ku Brazil, onse analibe vuto ndi zokwatirana pakati pawo.” (Red Gold—The Conquest of the Brazilian Indians) Amwenye ankaona kuti kupereka akazi amtundu wawo, makamaka ana awo, kuti akwatiwe ndi anthu achilendo kunali kusonyeza kuti alendowo awalandira bwino. Pamene anafika ku Brazil, m’chaka cha 1549, Akatolika a chipani cha Ajezuwiti anakhumudwa kwambiri ndi zimene anaona. Mjezuwiti wina, dzina lake Manoel Nóbrega, anadandaula motere: “[Abusa] amauza amuna poyera kuti palibe
cholakwika kungolowana ndi akazi achimwenyewa. Atsamundawa amatenga akapolo awo onse aakazi ngati azikazi awo.” Munthu wina anauza mfumu ya ku Portugal kuti pali mtsamunda wina wachipwitikizi yemwe ‘ali ndi ana, zidzukulu, zidzukulu tudzi komanso mbumba yaikulu zedi moti ndikuchita mantha kukuuzani chiwerengero chawo.’Pofika cha m’kati mwa m’ma 1600, magulu ambiri a amwenye amene kale ankapezeka ponseponse m’madera a m’mphepete mwanyanja ku Brazil, anali ataphedwa, kapena kugwidwa ukapolo, kapenanso kusakanikirana ndi azungu chifukwa cha maukwati. Posakhalitsa, zoterezi n’zimenenso inaona mitundu ya amwenye a m’chigawo cha Amazon.
Apwitikizi atafika m’chigawo cha Amazon, tingati inali nthawi yawo yoti akhetse magazi mmene angafunire m’dera lonse la kumunsi kwa mtsinje wa Amazon. Malinga ndi zimene ananena Mkatolika wina wa udindo woyang’anira boma la Maranhão, dzina lake Manoel Teixeira, m’zaka makumi angapo chabe Apwitikizi anapha pafupifupi amwenye 2 miliyoni m’boma la Maranhão ndi Pará. N’kutheka kuti chiwerengerochi n’chongokokomeza komabe chikusonyeza mavuto aakulu amene amwenyewa anakumana nawo. Patsogolo pake, madera a kumtunda kwa mtsinje wa Amazon anakumananso ndi zoopsa zoterezi. Pofika cham’kati mwa zaka za m’ma 1700, pafupifupi amwenye onse anali atatha m’chigawo cha Amazon, kupatulapo m’madera akutali kwambiri.
Chakumapeto kwa m’ma 1800 ndi m’ma 1900, chitukuko chinafika m’madera ambiri akutali a m’chigawo cha Amazon ndipo zimenezi zinachititsa kuti amwenye amene anatsala m’madera amenewa ayambe kukumana ndi azungu. Charles Goodyear atatulukira njira yopangira mphira mu 1844, zomwe zinachititsa kuti ayambe kupanga matayala a labala, malonda a mitengo yopangira labala anayamba kuyenda bwino kwambiri. Anthu azamalonda anayamba kukhamukira ku chigawo cha Amazon, chomwe chinali chigawo chokhachi chimene kunkapezeka zipangizo zofunika popanga labala. Nthawi imeneyi n’njotchuka kwambiri chifukwa cha zinthu zimene azamalondawa ankachita podyera masuku pamutu amwenyewa, zomwe zinachepetsanso kwambiri chiwerengero chawo.
Kodi Moyo wa Amwenyewa Unasintha Motani M’ma 1900?
Mu 1970, boma la Brazil linaganiza zogwirizanitsa amwenyewa ndi anthu ena onse m’dzikolo. Linatero pokonza misewu ikuluikulu yofika m’madera akutali kwambiri m’chigawo cha Amazon. Misewu yambiri yotereyi inadutsa m’kati mwa madera okhala amwenye. Motero zinakhala zosavuta kuti kuzifika anthu obwera kudzafufuza zinthu zimene makampani osiyanasiyana angapindule nazo. Zimenezi zinabweretsanso nthenda zoopsa zosiyanasiyana.
Mwachitsanzo taganizirani zimene anaona amwenye otchedwa Panarás. Mtunduwu unachepa kwambiri chifukwa cha nkhondo ndi ukapolo, m’zaka za m’ma 1700 ndi m’ma 1800. Amwenye ochepa chabe a mtunduwu anathawira kumpoto cha kumadzulo, n’kulowerera m’nkhalango yakumpoto ku Mato Grosso. Kenaka boma linakonza msewu waukulu wochoka ku Cuiabá kupita ku Santarém, womwe unadutsa m’kati mwenimweni mwa dera la amwenyewa.
Kukumana ndi azungu kunaphetsa ambiri mwa amwenyewa. Mu 1975, mtundu wa amwenye ambirimbiriwo unangotsala ndi anthu 80 basi. Amwenye a mtundu wotchedwa Panarás anasamutsidwa n’kuwapititsa ku malo otetezerako zachilengedwe otchedwa Xingu National Park. Kumeneko anayesetsa kupeza dera lofanana kwambiri ndi kwawo koma sanalipeze. Kenaka amwenyewa anaganiza zobwerera kwawo. Pa November 1, 1996, nduna ya zachilungamo ya ku Brazil inalamula kuti dera lalikulu mahekitala 495,000 likhale “malo oti amwenyewa azikhalako mpaka kalekale.” Pamenepatu zikuoneka kuti mtundu umenewu wa amwenye wapulumuka.
Kodi Tsogolo Lawo Likhala Labwino Kuposa Kale Lawo?
Kodi kuika amwenyewa m’madera otetezeka kungawathandize kuti asapululuke? Pakali pano zikuoneka kuti n’zosatheka kuti amwenye onse ku Brazil adzathe. Koma vuto lagona poti m’zigawo zambiri zimene amwenyewa akukhala muli madera amene ali ndi miyala yambiri yamtengo wapatali. Akuti m’chigawo chotchedwa Legal Amazonia, muli miyala yamtengo wapatali, monga golide, pulatinamu, dayamondi, aironi, ndi ledi, yokwana pafupifupi madola 1 thililiyoni. Ichi n’chigawo chachikulu chomwe chili ndi maboma 9 opezeka kumpoto ndi pakati chakum’mawa kwa dziko la Brazil. Pafupifupi madera onse amene kumakhala amwenye ku Brazil ali m’chigawo chimenechi. Koma tikunena pano pali anthu ena amene ayamba kale kuswa lamulo popita m’madera amenewa n’kumakafufuza zinthu zimene makampani angapindule nazo m’deralo.
Tikaganizira zimene zakhala zikuchitika m’mbiri yonse ya m’dzikoli timaona kuti amwenyewa amangodyeredwa masuku pamutu akakumana ndi azungu a kumeneku. Azungu ankalima pamsana amwenyewa powapatsa magalasi oonerapo nkhope kuti asinthane ndi golidi. Ndipo ankawapatsa tizinthu tawo tachabechabe kuti asinthane ndi mitengo yamtengo wapatali ya kumeneko. Komanso amwenyewa ankachita kuthawira ku nkhalango za kutali kwambiri poopa kugwidwa ukapolo. Kodi zoterezi n’zimene zingadzachitikenso?
Amwenye ambiri anayamba kukhala moyo wamakono, womakwera ndege, maboti ainjini, ndiponso kugwiritsira ntchito mafoni am’manja. Koma zitenga nthawi kuti titsimikizire zoti amwenyewa angathe kuthana bwinobwino ndi mavuto obwera chifukwa cha chitukuko cha masiku anochi.
[Mapu patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
■ Malo otetezerako zachilengedwe otchedwa Xingu
□ Malo omwe kuli midzi ya amwenye
BRAZIL
BRASÍLIA
Rio de Janeiro
FRENCH GUIANA
SURINAME
GUYANA
VENEZUELA
COLOMBIA
ECUADOR
PERU
BOLIVIA
PARAGUAY
URUGUAY
[Chithunzi patsamba 15]
Anthu a zamalonda ankalima amwenyewa pamsana powagwiritsa ntchito ya thangata m’minda yawo ya mitengo ya labala
[Mawu a Chithunzi]
© Jacques Jangoux/Peter Arnold, Inc.
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Line drawing and design: From the book Brazil and the Brazilians, 1857