Kodi Mlembi wa Baibulo Ndani?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mlembi wa Baibulo Ndani?
BAIBULO silibisa za amene analilemba. Mabuku osiyanasiyana a Baibulo amayamba ndi mawu monga akuti, “mawu a Nehemiya,” “masomphenya a Yesaya,” ndi “mawu a Yehova a kwa Yoweli.” (Nehemiya 1:1; Yesaya 1:1; Yoweli 1:1) Mabuku ena a mbiri yakale amatchulidwa kuti analembedwa ndi Gadi, Natani kapena Samueli. (1 Mbiri 29:29) Timawu tapamwamba ta masalmo ambiri timatchula munthu amene analemba.—Salmo 79, 88, 89, 90, 103 ndi 127.
Chifukwa chakuti anthu anagwiritsidwa ntchito kulemba Baibulo, anthu omwe amalikayikira amati Baibulo langokhala buku la nzeru za anthu basi, ngati mmene zilili ndi mabuku ena. Kodi iwo ali ndi zifukwa zomveka zonenera zimenezi?
Analilemba Anthu 40 Koma Mlembi Wake Ndi Mmodzi
Olemba Baibulo ambiri ananena kuti analemba mawu a Yehova, Mulungu woona yekha, ndipo kuti anatsogoleredwa ndi iyeyo kapena mngelo wake. (Zekariya 1:7, 9) Aneneri amene analemba Malemba Achiheberi ananena nthawi zoposa 300 kuti: “Atero Yehova.” (Amosi 1:3; Mika 2:3; Nahumu 1:12) Mabuku awo ambiri amayamba ndi mawu monga akuti: “Mawu a Yehova amene anadza kwa Hoseya.” (Hoseya 1:1; Yona 1:1) Ponena za aneneri a Mulungu, mtumwi Petulo anati: “Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Petulo 1:21.
Choncho, Baibulo lili ndi mabuku ambiri koma nkhani zake zonse n’zogwirizana, ndipo linalembedwa ndi anthu ambiri omwe anati zomwe analemba zinachokera kwa Mulungu. Kunena kwina, Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kulemba nzeru zake. Kodi zinatheka bwanji zimenezi?
‘Linauziridwa ndi Mulungu’
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Mawu achigiriki omasuliridwa kuti ‘kuuziridwa ndi Mulungu’ kwenikweni amatanthauza “kupumiridwa ndi Mulungu.” Choncho, Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu yosaoneka kutsogolera anthu kulemba Baibulo ndi kuwauza zoti alembe. Koma Yehova mwinawake ndiye analemba Malamulo Khumi pamiyala. (Eksodo 31:18) Nthawi zina, Mulungu ankachita kuwauza yekha anthuwo uthenga woti alembe. Pa Eksodo 34:27 timawerenga kuti: “Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mawu awa . . .”
Nthawi zinanso, Mulungu ankawachititsa anthuwo kuona masomphenya a zinthu zoti alembe. N’chifukwa chake Ezekieli ananena kuti: “Ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.” (Ezekieli 1:1) Mofanana ndi zimenezi, “Danieli anaona loto, naona masomphenya a m’mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo.” (Danieli 7:1) Mtumwi Yohane analandira uthenga wa m’buku lomaliza la Baibulo la Chivumbulutso mwanjira ya masomphenya yomweyi. Yohane analemba kuti: “Mwa mzimu, ndinafika m’tsiku la Ambuye, ndipo kumbuyo kwanga ndinamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anati: ‘Zimene uone, lemba mu mpukutu.’”—Chivumbulutso 1:10, 11.
Anagwiritsa Ntchito Luso Lawo
Ngakhale kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu, sizitanthauza kuti anthu amene analilemba sanagwiritse ntchito luso lawo. Iwo anafunikira kugwiritsa ntchito luso lawolo kuti alembe bwino uthenga wa Mulungu. Mwachitsanzo, amene analemba buku la Mlaliki ananena kuti: ‘Anasanthula kuti apeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mawu oona.’ (Mlaliki 12:10) Kuti alembe nkhani yake ya mbiri yakale, Ezara anafufuza m’mabuku osachepera 14, monga “buku la mbiri ya mfumu Davide” ndi “buku la mafumu a Yuda ndi Isiraeli.” (1 Mbiri 27:24; 2 Mbiri 16:11) Luka yemwe analemba Uthenga Wabwino ‘anafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pachiyambi, anafunitsitsa kuti alembe mwatsatanetsatane.’—Luka 1:3.
Mabuku ena a Baibulo amasonyeza bwino amene anawalemba. Mwachitsanzo, Mateyo Levi, yemwe anali wokhometsa msonkho asanakhale wophunzira wa Yesu, ankakonda zinthu za manambala. Iye ndi wolemba Uthenga Wabwino yekhayo amene anatchula kuti Yesu anaperekedwa ndi “ndalama 30 zasiliva.” (Mateyo 27:3; Maliko 2:14) Luka, yemwe anali dotolo, anafotokoza bwino nkhani za matenda. Mwachitsanzo, pofotokoza matenda a anthu ena amene Yesu anawachiritsa, Luka anatchula mawu monga, “malungo aakulu” ndiponso “khate thupi lonse.” (Luka 4:38; 5:12; Akolose 4:14) Choncho, Yehova analola kuti olemba Baibulo afotokoze zinthu mwa luso lawo ndi m’mawu awoawo, komabe iye anawatsogolera kuti alembe uthenga wake molondola.—Miyambo 16:9.
Baibulo Lonse
Kodi si zodabwitsa kuti anthu pafupifupi 40, okhala m’mayiko osiyanasiyana, alembe buku limodzi pazaka zoposa 1,600, koma nkhani zake zonse n’kukhala zogwirizana komanso zofotokoza mfundo yaikulu imodzi yochititsa chidwi? (Onani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?” patsamba 19.) Zimenezi sizikanatheka popanda mlembi mmodzi kuwatsogolera.
Kodi Yehova sakanachitira mwina koma kugwiritsa ntchito anthu kulemba Mawu ake? Ayi. Koma zimene anachitazi zimangosonyeza kuti iye ndi Mulungu wanzeru. Indedi, chinthu chimodzi chomwe chachititsa kuti anthu ambiri padziko lonse azikonda Baibulo n’chakuti olemba ake anafotokoza bwino mmene anthu amamvera mumtima mwawo akakumana ndi zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Mfumu Davide anafotokoza mmene munthu amamvera pamene wachimwa ndipo akuchonderera Mulungu kuti am’chitire chifundo.—Salmo 51:2-4, 13, 17, timawu tapamwamba.
Ngakhale kuti Yehova anagwiritsa ntchito anthu kulemba Mawu ake, ifenso tingakhulupirire Malemba Oyera ngati mmene Akhristu oyambirira anachitira. Iwo anawalandira osati “monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
▪ Kodi mlembi wa “Malemba onse” ndani?—2 Timoteyo 3:16.
▪ Kodi Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito njira zotani pouza anthu zoti alembe m’Baibulo?—Eksodo 31:18; 34:27; Ezekieli 1:1; Danieli 7:1.
▪ Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti anthu anagwiritsa ntchito luso lawo polemba Baibulo?—Mateyo 27:3; Luka 4:38.