‘Chitseko Chimene Yehova Yekha Ndi Amene Angatsegule’
‘Chitseko Chimene Yehova Yekha Ndi Amene Angatsegule’
▪ M’chaka cha 2007 bambo wina anamwalira. Bamboyu anasiya mwana wamkazi wazaka 6, dzina lake Erika, ndi wamwamuna wazaka 4, dzina lake Mattia. Chimene chawathandiza anawa kuti aiwaleko imfa ya bambo awo ndi chiyembekezo chakuti akufa adzauka.—Machitidwe 24:15.
Erika amakonda kuuza ena zinthu za m’Baibulo zimene amakhulupirira, makamaka akapita ku sukulu kwake mumzinda wa Sicily. Mwachitsanzo, mnzake wina, dzina lake Beatrice, atamuuza kuti amakhulupirira kuti bambo ake anapita kumwamba atamwalira, Erika anamufotokozera kuti Baibulo limanena zosiyana ndi zimenezo. Beatrice anafunsa kuti: “Ndiye kuti bambo anga ali kuti?”
Erika anati: “Ali kumanda.” Erika atanena zimenezi, Beatrice anafuna kudziwa zambiri za manda.
Erika anamuuza kuti “manda ali ngati chitseko chimene chimatsegula ndi kutseka. Koma chitsekochi chikatseka, palibe angatsegulenso. Yehova yekha ndi amene adzachitsegule m’dziko latsopano.”
Kenako Erika anafotokozera mnzakeyo kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Anamuuzanso kuti Yehovayo adzakonza dziko lapansi kuti likhale paradaiso, komwe sikudzakhalanso kudwala ndipo akufa adzakhalanso ndi moyo. Ndiyeno Erika anauza Beatrice kuti akafunse mayi ake ngati angalole kuti Erika apatse mwana wawoyo buku lofotokoza mfundo zimene anakambiranazo.
Mayi a Beatrice analola kuti mwana wawo apatsidwe bukulo, ndipo patapita masiku angapo Erika anapatsa mnzakeyo buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Erika amauzabe anzake zinthu zimene iye amaphunzira m’Baibulo ndipo anapatsa aphunzitsi ake buku limodzi lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.
Panopa Erika ndi mchimwene wake Mattia ali ndi chisonibe chifukwa cha imfa ya bambo awo. Koma zimene Baibulo limanena kuti akufa adzauka zimawatonthoza kwambiri. Poyembekezera nthawi imeneyo, anawa, mofanana ndi ana ena ambiri padziko lonse, amalemekeza Yehova, yemwe ndi Mulungu amene amatitonthozadi.—Mateyo 21:16; 2 Akorinto 1:3, 4.
Mukhoza kuitanitsa buku la zithunzi zokongola la masamba 256 limeneli, lomwe masamba ake ndi aakulu mofanana ndi a magazini ino. Lembani adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli. Tchulani chilankhulo chimene mukufuna.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.