Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Kutukwana N’kulakwadi? (March 2008) Ndinakulira m’banja lachikhristu, koma ndinali ndi chizolowezi chotukwana. Ndinkayesetsa kuthetsa chizolowezi chimenechi, koma zinkandivuta. Nkhaniyi yandithandiza kwambiri. Monga mmene munanenera m’nkhaniyi, ndikuona kuti kutukwana ndi kusayamikira mphatso ya kulankhula imene Mulungu anatipatsa. Masiku ano ndimayamba ndaganiza kaye ndisanalankhule. Zikomo kwambiri.

C. P., Brazil

Panopa ndili ndi zaka 12. Kusukulu kwathu anzanga amakonda kutukwana, ndipo ndikuopa kuti nanenso ndingatengere khalidwe limeneli. Pamene nkhani imeneyi inatuluka mu Galamukani!, n’kuti ndikuganiza zokupemphani kuti mulembe zimenezi m’nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa.” Nkhaniyi yandikumbutsa kuti kutukwana ndi kulakwa, ndipo yandilimbikitsa kuti ndisamatukwane. Pitirizani kulemba nkhani ngati zimenezi.

A. P., United States

Ineyo ndi mwamuna wanga timagwira ntchito yoyeretsa nyumba za anthu. Munthu wina amene timamuyeretsera nyumba yake, anatiuza “mfundo yomwe akufuna kutsatira m’chaka chatsopano.” Iye ananena kuti tsiku lililonse akumapempha Mulungu kuti amuthandize kuthetsa khalidwe lake loipa. Ndipo anandipempha kuti ndim’patse magazini aliwonse amene ndinali nawo okhudza nkhaniyi. Ndinapempherera nkhani imeneyi, ndipo ndinakopera magazini atsopano a pa MP3 kuchokera pa adiresi ya pa Intaneti ya www.mr1310.com. Pomvetsera tsiku lotsatira, ndinasangalala kwambiri kumva mitu imene inali m’magaziniyo. Ngakhale kuti nkhaniyi munalembera achinyamata, ndinaonabe kuti imuthandiza. Choncho, ndinapita kukamupatsa magaziniyo.

S. C. United States

Oona za Ndege Amakutetezani Bwanji? (April 2008) Nditawerenga nkhaniyi ndinasangalala kwambiri chifukwa ndinadziwa kuti anthu aona za ndege amayesetsa kuti pasachitike ngozi ndege ikamanyamuka. Galamukani! imeneyi inafotokoza bwino kwambiri nkhaniyi. Zikomo kwambiri.

T. S., Brazil

Kodi Mungayankhe Bwanji? Panopa ndili ndi zaka 12 ndipo ndimakhala kum’mwera kwa dziko la Ireland. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha nkhani zimene zimakhala kumapeto kwa magazini a Galamukani! zomwe zimakhala ndi mafunso oti achinyamata ayankhe. Zimenezi n’zothandiza kwambiri. Zimathandiza kuti ana awerenge magaziniwa. Ndikupempha kuti musaleke kulemba zimenezi. Zikomo.

A.C., Ireland