Mabanja Amene Zinthu Zikuwayendera Bwino—Chigawo Choyamba
Mabanja Amene Zinthu Zikuwayendera Bwino—Chigawo Choyamba
Monga mmene Galamukani! yapaderayi yasonyezera, ngakhale mabanja amene zinthu zikuwayendera bwino amakhala ndi mavuto. Ndipo zimenezi si zachilendo chifukwa Baibulo limati tikukhala ‘m’nthawi yovuta.’ (2 Timoteyo 3:1) Choncho, pafupifupi banja lililonse masiku ano limakumana ndi mavuto.
Kodi zingatheke bwanji kuti banja limene likukumana ndi mavuto liziyenda bwino? Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Mabanja amene amazindikira zosowa zawo zauzimu amatsatira mfundo za m’Baibulo ndipo zinthu zimawayendera bwino, ngakhale kuti nthawi zina amakumana ndi mavuto. Onani zitsanzo zotsatirazi:
Kusamalira mwana wolumala. Baibulo limasonyeza kuti kusamalira anthu a m’banja mwathu, kuphatikizapo amene akufunika thandizo lapadera, n’kofunika kwambiri. Limati: “Ngati munthu sasamalira ake a iye mwini, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.”—1 Timoteyo 5:8.
Patsamba 15, pali nkhani ya bambo wina wa ku South Africa, dzina lake Victor. Iye ndi mkazi wake akhala akusamalira mwana wolumala kwa zaka zoposa 40.
Kuleredwa ndi makolo ena. Mfundo za m’Baibulo zingathandize munthu kudziona kuti ndi wofunikabe, ngakhale makolo ake omubereka atamusiya. Baibulo limati Yehova Mulungu ndi “mthandizi” wa ana amasiye.—Salmo 10:14.
Patsamba 16, pali nkhani ya mtsikana wina wa ku United States, dzina lake Kenyatta. Iye sanaonanepo ndi makolo ake omubereka.
Kupirira imfa ya mayi kapena bambo. Kumwalira kwa mayi kapena bambo n’kopweteka kwambiri ndipo n’zovuta kuiwala. Koma Baibulo lingatithandize kupirira, chifukwa Mlembi wake ndi Yehova, yemwe ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse.”—2 Akorinto 1:3.
Patsamba 17, pali nkhani ya mtsikana wina wa ku Australia, dzina lake Angela. Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kwamuthandiza kuti aiwaleko imfa ya bambo ake.
Nkhani zotsatirazi zikusonyeza kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumathandiza kuti mabanja aziyenda bwino ngakhale akukumana ndi mavuto.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 15]
Kusamalira Mwana Wolumala
Yosimbidwa ndi Victor Maynes, wa ku South Africa
“Kuyambira ali mwana, Andrew wakhala akudalira ifeyo kuti timuveke, timusambitse ndiponso nthawi zina kuti timudyetse. Panopa ali ndi zaka 44.”
TITAONA kuti Andrew wapitirira chaka chimodzi koma sakuyenda, tinayamba kuganiza kuti ali ndi vuto. Tsiku lina, iye anakomoka ndipo tinathamangira naye kuchipatala. Madokotala atamuyeza anatiuza kuti mwanayo ali ndi matenda a khunyu. Koma anali ndi mavuto enanso. Iwo anapezanso kuti ubongo wake sukugwira ntchito bwino.
Titayesa mitundu yosiyanasiyana ya mankhwala, Andrew anayamba kupezako bwino. Iye ankamwa mankhwala amitundu inayi, katatu patsiku. Koma palibe mankhwala amene angathetseretu vuto lake. Ngakhale kuti panopa ali ndi zaka 44, amachita zinthu ngati mwana wazaka 5 kapena 6.
Madokotala anatilangiza kuti tikamusiye kumalo osamalira ana amene ali ndi matenda osiyanasiyana. Koma ifeyo tinaona kuti ndi bwino kuti tizimusamalira tokha, ngakhale kuti kuchita zimenezi kuli ndi mavuto ake.
Choncho, tonse m’banja mwathu timathandizana kusamalira Andrew. Timathokoza ana athu awiri aakazi ndi mwana wathu wina wamwamuna amene anatithandiza kwambiri kusamalira Andrew. Komanso a Mboni za Yehova anzathu akhala akutithandiza kwambiri. Nthawi zina amatipatsa chakudya kapena kusamalira Andrew ifeyo tikapita kolalikira kapena kukachita zinthu zina.
Nthawi zonse timakumbukira lonjezo la Mulungu limene limapezeka pa Yesaya 33:24, lakuti m’tsogolomu anthu “sadzanena, Ine ndidwala.” Sitikayikira ngakhale pang’ono kuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chobweretsa dziko latsopano ndiponso chothetsa matenda onse. (2 Petulo 3:13) Choncho, timayembekezera nthawi imene Andrew adzakhale bwino. Panopo timalimba mtima tikaganizira mawu a Yesu akuti ngati tiika zinthu za Ufumu wa Mulungu patsogolo, tidzapatsidwa zinthu zimene timafunikira pamoyo. (Mateyo 6:33) Mulungu wakhala akutithandiza nthawi yonseyi ndipo sitisowa chilichonse.
N’zoona kuti mabanja onse sangakwanitse kusamalira okha munthu wa pabanja pawo amene akudwala. Koma inu amene mukukwanitsa kuchita zimenezi, ndikukulimbikitsani kuti muzipemphera nthawi zonse. (1 Petulo 5:6, 7) Chachiwiri, muzikonda kwambiri mwana wanuyo, ndipo musamaone ngati iye sangathe kuphunzira za Yehova Mulungu. (Aefeso 6:4) Chachitatu, munthu aliyense pabanja panu ayenera kuyesetsa kusamalira wodwalayo. Chachinayi, muyenera kukumbukira kuti panyumba panu m’pamene mwana wanuyo angasamalidwe mwachikondi kwambiri. Tikudziwa kuti mabanja ndi osiyanasiyana. Koma ifeyo tikuona kuti tinachita bwino kusankha kuti tizisamalira Andrew panyumba pathu. Ndipo Andrew ndi mwana amene ndimamukonda kwambiri.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 16]
Kuleredwa ndi Makolo Ena
Yosimbidwa ndi Kenyatta Young, wa ku United States
“Ukaleredwa m’banja loti kholo limodzi ndi lokupeza zimakhalako bwino chifukwa umaonabe kuti pali chibale. Koma ineyo ndimakhala ndi makolo amene anangonditenga kuti ndizikhala nawo. Ndipo sindikudziwa m’bale wanga aliyense.”
BAMBO anga wondibereka sindikuwadziwa ndipo mayi anga sindinawaonepo. Ndinamva kuti mayi anga ankamwa kwambiri mowa komanso ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ali ndi pakati. Nditabadwa, anakandisiya kumalo osamalira ana amasiye, ndipo ndinakhala m’malo osiyanasiyana oterewa. Kenako, ndisanakwanitse zaka ziwiri, banja lina linanditenga n’kumakhala nane.
Bambo anga wondilera anandiuza kuti mayi wogwira ntchito kumalo osamalira ana amasiye atawaonetsa chithunzi changa, nthawi yomweyo anaganiza zonditenga. Pasanapite nthawi ndinayamba kukondana ndi mayi anga atsopanowa. Ndinawauza kuti iwo ndi mayi anga ndipo ndikufuna kupita nawo kunyumba kwawo.
Komabe ndikukumbukira kuti ndili mwana ndinkaopa kuti ndikalakwitsa chinachake, andibwezera kumalo osamalira ana amasiye. Ndinkaona kuti sindinali woyenera kumapsa mtima kapena kudwala ngati mmene ana ena amachitira. Ndipo ndinkayesetsa kwambiri kuti ndisatenge chimfine. Nthawi zambiri makolo angawo ankanditsimikizira kuti amandikonda ndipo sanganditaye.
Ngakhale kuti tsopano ndakula, nthawi zambiri ndimadzionabe kuti ndine wosafunika. Ndipo ndikayamba kuchotsa maganizo amenewa, anthu ena amandikumbutsa pondiuza kuti, “Uzithokoza kwambiri kuti uli ndi makolo achikondi amene analolera kukutenga kuti uzikhala nawo.” Ndimathokozadi kuti makolowa ananditenga, koma mawu ngati amenewa amandikhumudwitsa chifukwa zimakhala ngati kuti ndine munthu wosayenera kukondedwa.
Zimandipweteka kwambiri ndikaganizira kuti mwina sindidzawaona bambo anga wondibereka. Nthawi zambiri zimandipwetekanso kuti mayi anga wondibereka sanasiye kuledzera kuti andilere. Nthawi zina ndimawamvera chisoni. Ndimaganiza kuti ndikanakumana nawo, ndikanawauza kuti zinthu zikundiyendera ndipo asadandaule kuti sanandisamalire.
Makolo anga ondilera ndi a Mboni za Yehova, ndipo chimodzi mwa zinthu zabwino kwambiri zimene andichitira ndi kundiphunzitsa Baibulo. Nthawi zambiri ndimatonthozedwa ndi mawu a pa Salmo 27:10, akuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” Zimenezi n’zimene zandichitikira ineyo. Ndipo kuleredwa ndi makolo ena kuli ndi zinthu zina zabwino. Mwachitsanzo, ndimasangalala kudziwa mbiri ndiponso moyo wa anthu ena, mwina chifukwa chakuti sindikuwadziwa makolo anga ondibereka. Ndimakonda kwambiri anthu ndipo zimenezi zimandithandiza pogwira ntchito yolalikira. Kukhala wa Mboni za Yehova ndiponso kulankhula za uthenga wa m’Baibulo kumandithandiza kuona kuti ndine wofunika ndiponso moyo wanga uli ndi cholinga. Ndikayamba kudziona kuti ndine wosafunika, ndimapita kolalikira. Kuphunzitsa anthu Baibulo kumandithandiza kuti ndipeze anzanga. Ndadziwa kuti aliyense ali ndi mbiri yosangalatsa ya moyo wake.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 17]
Kupirira Imfa ya Bambo
Yosimbidwa ndi Angela Rutgers, wa ku Australia
“Bambo anga atamwalira zinandikhudza kwambiri. Iwo anali munthu amene ankandithandiza pa chilichonse.”
BAMBO anga anamwalira zaka 10 zapitazo, ndisanakwanitse zaka 20. Miyezi 6 asanamwalire, iwo anapangidwa opaleshoni ndipo dokotala anatiuza kuti n’zokayikitsa kuti achira. Titamva zimenezi, mchimwene wanga anakomoka ndipo ineyo ndinasokonekera kwambiri maganizo. Mayi anga ankangofunsa dokotalayo mafunso ambirimbiri. Monga ndafotokoza kale, patatha miyezi 6 anamwalira.
Bambo atamwalira, ndinayamba kuvutika maganizo kwambiri. Ndinkafuna kuti anzanga azindimvetsa koma sindinkafuna kuti azindimvera chisoni kwambiri. Choncho ndinayesetsa kuti anzanga asadziwe mmene ndinkamvera mumtima. Komabe ndinkaona kuti zinali zovuta kupitiriza kucheza nawo bwinobwino popanda kuwasonyeza kuti chinachake chachitika. Ndikaganizira zimene ndinkachita, ndimaona kuti anzanga ankaleza nane mtima.
Nthawi zina ndimadziimba mlandu chifukwa cha imfa ya bambo anga. Ndikanakonda zikanakhala kuti nthawi zambiri ndinkawauza kuti, “Ndimakukondani bambo.” Ndimalakalaka ndikanati ndiziwakumbatira nthawi zambiri ndi kucheza nawo pamene anali moyo. Ndimayesetsa kudziuza ndekha kuti, ‘Bambo ako sakanafuna kuti uziganiza zimenezi,’ koma maganizo amenewa amandibwererabe.
Ndine wa Mboni za Yehova ndipo zimene Baibulo limanena zakuti akufa adzauka zimanditonthoza kwambiri. (Yohane 5:28, 29) Ndimayesetsa kuyerekezera kuti bambo anga anachoka kupita dera lina lakutali ndipo tsiku lina adzabweranso. Poyamba sindinkasangalala anthu akamandiuza kuti, “Bambo ako udzawaonanso akadzaukitsidwa.” Ine mumtima ndinkati, ‘Ndikufuna kuonana ndi bambo anga panopa.’ Koma kuyerekezera kuti bambo anga apita ku ulendo wautali kunkandithandiza kwambiri. Zimenezi zinkandithandiza kupirira ndiponso kuona kuti m’tsogolomu bambo anga adzauka.
Akhristu anzanga andithandiza kwambiri. Mwachitsanzo, ndikukumbukira munthu wina amene anandiuza kuti samasangalala kunena za imfa ya bambo anga koma nthawi zonse amandiganizira ineyo ndi banja lathu. Mawu amenewa ankandilimbikitsa kwambiri chifukwa ndinazindikira kuti ngakhale anthu sankanena chilichonse, iwo ankaganizira kwambiri ineyo ndi banja lathu. Kudziwa zimenezi kunandithandiza kwambiri.
Patatha miyezi inayi bambo anga atamwalira, mayi anayamba kuthera nthawi yaitali akugwira ntchito yolalikira. Ndipo ndinkaona kuti zimenezi zikuwathandiza kwambiri kuti aiwale imfa ya bambo. Kenako inenso ndinayamba kugwira nawo ntchitoyi. Kuthandiza ena kumachepetsa kwambiri nkhawa. Ntchitoyi yandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Mawu a Yehova ndi malonjezo Ake. Yandithandizanso kuti ndiziganizira anthu ena m’malo momangoganizira za mavuto anga.