Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Analimba Mtima Kufotokoza Zimene Amakhulupirira

Analimba Mtima Kufotokoza Zimene Amakhulupirira

Analimba Mtima Kufotokoza Zimene Amakhulupirira

▪ Atatsala pang’ono kupita kutchuthi, Morgan, yemwe ndi mtsikana wa zaka 7 wa ku pulayimale, pamodzi ndi anzake anauzidwa kuti akawerenge nkhani yokhudza Khirisimasi. Morgan anauza aphunzitsiwo kuti iye amaona kuti Khirisimasi sigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Aphunzitsi akewo anamupatsa mwayi wosankha nkhani ina imene ingagwirizane ndi chikumbumtima chake.

Kenako, pasukuluyi panali mwambo wopereka mphoto zosiyanasiyana kwa ana a sukulu, ndipo makolo a Morgan anaitanidwa ku mwambowu. Morgan anapatsidwa mphoto chifukwa cha kulimba mtima pofotokoza zimene amakhulupirira, ndipo iye sanayembekezere zimenezi. Iye atafunsidwa kuti afotokoze chimene chinamuthandiza kuti akhale wolimba mtima, anafotokoza kuti amawerenga ndi makolo ake buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mfundo za m’bukuli zimakhudza zimene Yesu Khristu ankachita ndi kuphunzitsa.

Buku la masamba 256 limeneli, lomwenso lili ndi zithunzi zokongola, limathandiza makolo kukambirana ndi ana awo momasuka. Bukuli lili ndi mitu monga “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza,” “Kodi ndi Mapwando Onse Amene Amakondweretsa Mulungu?” ndi “Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha.”

Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.