Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukufuna Kukhala Bwenzi la Mulungu?

Kodi Mukufuna Kukhala Bwenzi la Mulungu?

Kodi Mukufuna Kukhala Bwenzi la Mulungu?

● Kodi mungayankhe bwanji funsoli? Mtsikana winawake, yemwe amakhala m’dera la kumudzi, ku Guerrero, m’dziko la Mexico, ananena kuti amakaikira kuti munthu angakhale bwenzi la Mulungu. Atsikana ena awiri omwe ndi a Mboni za Yehova anamuonetsa mtsikanayo kabuku ka mutu wakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! m’chinenero chake. Iye anadabwa kwambiri kuti kabukuka kamapezeka m’chinenero chake cha Tlapanec. Iye ananena kuti sanaonepo buku lina lililonse lolembedwa m’chinenero chake kupatulapo mabuku otulutsidwa ndi boma.

Atsikana awiriwa anafotokoza kuti kabukuko kanali umboni wakuti Mlengi amamukonda mtsikanayo chifukwa ngati atakawerenga atha kumudziwa bwino Mlengi wake. Mwamsanga iye anayamba kuwerenga mutu woyamba wakuti “Mulungu Akukuitanani Kuti Mukhale Bwenzi Lake.” Atamaliza kuwerenga mutuwo, mtsikanayo anati: “Ndikufuna kukhala bwenzi la Mulungu. Kodi mungandipezere Baibulo?” Atsikana a Mboniwo atamubweretsera Baibulo, mayi a mtsikanayo anawapempha kuti asapite msanga kuti awaphunzitse zambiri.

Kabuku kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! kamapezeka m’zinenero zokwana 17 zimene anthu achimwenye amene amakhala ku Mexico amalankhula. Padziko lonse, kabukuka kamapezeka m’zinenero 278 (kuphatikizapo zilembo za akhungu). Mukhoza kuitanitsa kabukuka polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.