Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Msika wa ku Africa

Msika wa ku Africa

Msika wa ku Africa

NJIRA yabwino kwambiri yodziwira chikhalidwe, miyambo komanso chakudya cha anthu a dziko lina lililonse ndi kupita kumsika wa m’dzikolo. Kumeneko mungacheze ndi anthu a kumaloko, kulawa chakudya chawo komanso kugula katundu. Mungapezekonso ogulitsa malonda ansangala amene angayesetse kwambiri kuti alankhule chinenero chanu ngakhale kuti sakuchidziwa bwino.

Ku Africa kuno n’kumene kumapezeka misika yochititsa chidwi kwambiri. M’misika imeneyi mumakhala anthu ankhaninkhani komanso malonda a mitundu yonse. Munthu ukangoona zimene zimachitika m’misika imeneyi, umadziwadi kuti uli ku Africa. Tsopano tiyeni tikaone umodzi wa misika yotereyi, ku Douala, m’dziko la Cameroon.

Ulendo wa Kumsika

M’mizinda yambiri ya ku Africa, anthu popita kumsika amakonda kukwera njinga zamoto chifukwa zimayenda mwachangu komanso ndi zotchipa. Nthawi zambiri njingazi zimakhala zikudikirira anthu okwera. Nanunso ngati mutalimba mtima mungakwere nawo njingazi. Ku Cameroon, ulendo wa panjinga umakhala wofulumira komanso wotchipa kwambiri kuyerekeza ndi kukwera galimoto.

Ena amene sakufuna kukwera njinga zimenezi, amakwera matakisi, omwe amapezekanso ambirimbiri. Anthu angapo amadzazana mu takisi imodzi kuti aliyense alipire ndalama zochepa.

Kumakhala Mabenchi Ambirimbiri

Munthu amene sanayambe waonapo misika yotereyi, amachita chidwi ndi kuchuluka kwa anthu komanso mabenchi ogulitsirapo malonda. Anthu ambirimbiri, kuphatikizapo ana, amanyamula malonda awo pamutu. Nthawi zambiri malonda ake amakhala nkhuku, malalanje osendasenda, mankhwala osiyanasiyana ndi zinthu zina.

Pamwamba pa mabenchiwo pamadzaza ndi zinthu zakudimba monga kabichi, karoti, nkhaka, mabilinganya, maungu, zitheba, mbatata, tomato, zilazi ndi mitundu yosiyanasiyana ya letesi. Anthu ena ochokera ku mayiko akunja sangadziwe zakudya zina chifukwa zambiri zimakhala za ku Africa konkuno. Mabenchi amene amaoneka okongola kwambiri ndi ogulitsirapo tsabola wofiira ndi wachikasu, chifukwa m’mamawa dzuwa likamawala tsabolayo amanyezimira. Pamabenchi ena amagulitsirapo zipatso monga mapeyala, nthochi, manyumwa, mavwende, zinanazi, malalanje ndi mandimu. Zipatsozi zimaoneka kuti n’zokoma kwambiri komanso zimakhala zotsika mtengo. Kumakhalanso chakudya chofala monga chinangwa, zilazi ndi mpunga ndiponso zinthu zochokera kunja monga anyezi ndi adyo.

Anthu ambiri amene amagulitsa malonda mu msika wa Douala ndi a mitundu ya Hausa komanso Fula. Anthu amenewa sasowa chifukwa amavala mikanjo yaitali yotchedwa gandouras kapena boubous, yomwe nthawi zambiri imakhala ya buluu, yoyera, kapena yachikasu. Komanso amakonda kupereka moni wansangala mu chinenero cha Fulfulde. Mumsikamu anthu amachita zinthu mofatsa. Tili mumsikamu, munthu wina wogulitsa malonda, dzina lake Ibrahim, anandisankhira anyezi mutatu mkulumkulu n’kundipatsa waulere. Iye anandiuza kuti: “Ukauze mkazi wako kuti akaphikire limodzi ndi mpunga ndipo moto wake usakachuluke.”

Chapatali pang’ono tinaona nyama zongophedwa kumene zikugulitsidwa. Panali nyama ya ng’ombe ndiponso ya mbuzi. Tinaona anthu amphamvu zedi atanyamula nyama paphewa ndipo kenako anaiponya pabenchi. Anthu ogulitsa nyamawo akamaitanira malonda amanola mipeni yawo mwaluso kwambiri. Kwa anthu amene angafune kukapha okha nyama, pamagulitsidwanso mbuzi, nkhuku, ndiponso nkhumba zamoyo.

Kumakhalanso Zakudya Zophikaphika

M’misika yambiri ya ku Africa simungalephere kupeza malo kumene mungadyeko chakudya chophikaphika. M’malo ena otere mumakhala nyimbo zomwe zimaimbidwa mokweza kwambiri n’cholinga chokopa anthu ogula, koma pamakhala malo ena aphee kumene mungadyeko chakudya cha ku Africa komanso kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Nthawi zina amalemba pabolodi chakudya chimene ali nacho ndipo ngati mlendo sakuzidziwa bwino zakudyazi, angafunikire kupempha munthu wina kuti amuthandize kusankha chakudya chabwino.

Chakudya chimene chimapezeka kawirikawiri ndi mpunga ndiponso fufu, chomwe ndi chakudya chopangidwa kuchokera ku chinangwa, nthochi kapena zilazi zogaya. Kumakhalanso nsomba yowotcha, nyama ya ng’ombe, ndi nkhuku zomwe amaikamo msuzi wopangidwa ndi therere, chiponde kapena tomato. Chakudyachi chimatenga nthawi kuti chibwere ndipo ukamadikirira umakhala ndi nthawi yambiri yocheza.

Panabwera atsikana awiri ogwira ntchito pamalowa kudzatipatsira chakudya. Mmodzi anatibweretsera mpunga, nyemba ndi fufu m’mbale zachitsulo ndipo zonsezi anazinyamulira pa thileyi yayikulu. Zakudya monga mpunga ndi fufu, amadyera msuzi wa therere, ndiponso nyama ndi nsomba. Kwa amene amakonda zothirathira m’zakudya, pamakhalanso botolo la tsabola. Mtsikana wachiwiriyo anabweretsa beseni la madzi komanso nsalu yopukutira m’manja. Kusamba m’manja n’kofunika kwambiri chifukwa amadyera manja. Si zachilendo kuona munthu akupemphera asanayambe kudya ndipo anthu a tebulo loyandikana naye nawonso amavomereza kuti “Amen.”

Kulalikira Mumsika

Misika ndi yofunika kwambiri pa chikhalidwe cha anthu. Imathandiza kuti anthu akaguleko ndi kugulitsako malonda komanso n’kumene anthu amakonda kuuzanako nkhani, kucheza ndi anzawo komanso kufufuzako ntchito. Baibulo limanena kuti Yesu ankapita m’misika kukaphunzitsa anthu za Mulungu komanso kuchiritsa anthu odwala. Mtumwi Paulo nayenso ankakambirana ndi anthu ‘amene anakomana nawo m’bwalo la malonda [mumsika].’ (Machitidwe 17:16, 17; Maliko 6:56) Ngakhalenso masiku ano, Mboni za Yehova ku Cameroon zimaona kuti mumsika ndi malo abwino olalikiriramo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa.

[Chithunzi patsamba 24]

Tsabola wooneka bwino