Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Chionetsero chokhudza kusudzulana ku Italy. Pachionetserochi panali mabungwe othandiza anthu kupeza mwamuna kapena mkazi woti amange naye banja. Panalinso mabungwe amene amakonza za maulendo a anthu osakwatira akafuna kupita kutchuthi, mabungwe othandiza anthu amene akukonzekera kusudzulana kuti apeze loya wabwino, anthu owerengetsera zachuma, akatswiri a maganizo, ndi amkhalapakati a anthu osudzulana.—CORRIERE DELLA SERA, ITALY.

Anthu asiya kukhulupirira tchalitchi cha Katolika chifukwa cha “mmene tchalitchichi chakhala chikuchitira ndi nkhani zokhudza ansembe amene amapezeka ndi milandu yachiwerewere.” Zimenezi zachititsa kuti “kuyendetsa tchalitchichi kukhale kovuta kwambiri kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomo.”—NATIONAL CATHOLIC REPORTER, U.S.A.

Asayansi amene anafufuza DNA ya tsitsi la munthu wina amene anamupeza ku Greenland, yemwe anafa zaka 4,000 zapitazo, anati “zikuoneka kuti munthuyo anali wa ku Siberia.”—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.

Anthu Ambiri Sakukhulupiriranso Matchalitchi

Nyuzipepala ya The Irish Times inanena kuti: “Anthu ambiri sakukhulupiriranso tchalitchi [cha Katolika].” Nyuzipepalayo inati anthu ambiri ku Ireland sakukhulupiriranso tchalitchi cha Katolika mofanana ndi mmene sakukhulupiriranso boma komanso mabanki. N’zodabwitsa kuti ku Ireland, komwe anthu akhala akukhulupirira kwambiri tchalitchi cha Katolika, kunapezeka kuti anthu 32 pa anthu 100 alionse amene anafunsidwa mafunso pa kafukufuku winawake waposachedwapa ananena kuti sakhulupirira n’komwe tchalitchichi, ndipo anthu 21 pa anthu 100 alionse anati sakhulupirira kwenikweni tchalitchichi. Milandu imene atsogoleri a tchalitchichi akhala akupezeka nayo posachedwapa ndi imene yachititsa kuti anthu ambiri asamakhulupirirenso tchalitchichi.

Anthu Omaliza Maphunziro a Kukoleji Akusowa Ntchito

Kodi munthu akamaliza maphunziro a kukoleji ndiye kuti apeza ntchito? Osati nthawi zonse, malinga ndi zimene inanena nyuzipepala ya Manila Bulletin. Nyuzipepalayi inagwira mawu Herbert Bautista, yemwe ndi meya wa mzinda wa Quezon. Iye anati: “Anthu mamiliyoni ambiri akumamaliza maphunziro a kukoleji komanso yunivesite chaka chilichonse, ndipo ambiri a iwo sakupeza ntchito chifukwa zimene anaphunzira n’zosagwirizana ndi ntchito zimene zilipo.” Chifukwa chosowa ntchito, ambiri amangoyamba ntchito ya ukalaliki kapena yoperekera zakudya m’malesitilanti. Panopa boma likulimbikitsa anthu kuti akamaliza sukulu ya sekondale, azichita maphunziro osatenga nthawi yaitali a ntchito yamanja kuti azipeza ntchito mosavuta.

Zitsulo za Mlatho Zikudyekadyeka ndi Malovu a Anthu

Ku Calcutta, m’dziko la India, mlatho wotchedwa Howrah womwe ndi wautali mamita 457 ukudyekadyeka chifukwa cha malovu a anthu. Koma kodi malovu angachititse kuti zitsulo za mlatho zidyekedyeke? Anthu ambiri amene amadutsa pamlathowo amadya zinazake zokhala ngati chingamu zomwe zimapangidwa ndi masamba a mtedza wa beteli, mtedza wa areca ndiponso laimu. Iwo akatha kutafuna zimenezi amalavulira pazitsulo za mlathowu, ndipo malovuwo akuchititsa kuti zitsulozo zizidyekadyeka. Nyuzipepala ya The Telegraph ya mumzinda wa Calcutta inati: “Kuyambira m’chaka cha 2007, malovu a anthu odutsa pamlathowu achititsa kuti zitsulo zimene zimalimbitsa zipilala zake zidyeke. Zitsulozi zinali zokhuthala mamilimita 6 koma panopa zafika pa mamilimita atatu.” Pamlathowu pamadutsa anthu okwana 500,000 ndi magalimoto okwana 100,000 tsiku lililonse.