N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kumapita ku Misonkhano ya Mpingo?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kumapita ku Misonkhano ya Mpingo?
KODI MUMASANGALALA MUKAPITA KU MISONKHANO YA MPINGO?
INDE
↓
PITIRIZANI KUCHITA ZIMENEZO
AYI
↓
KODI MUYENERA KUCHITA CHIYANI?
BAIBULO limalimbikitsa Akhristu kuti azisonkhana pamodzi kuti azilambira Mulungu. (Aheberi 10:25) Koma bwanji ngati misonkhano ya mpingo sikusangalatsani? Bwanji ngati mukakhala pa misonkhano ya mpingo maganizo amakhala kwina? Mfundo zimene zili m’masamba otsatirawa zikhoza kukuthandizani.
1. MUZISONKHANA NTHAWI ZONSE
Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira.”—Aheberi 10:25.
N’chifukwa chiyani muyenera kumasonkhana nthawi zonse ngakhale kuti simusangalala ndi misonkhano? Chifukwa kusonkhana nthawi zonse n’kumene kungakuchititseni kuti muyambe kusangalala ndi misonkhanoyo. Taganizirani mfundo iyi: Kodi mukuganiza kuti mungamachite bwino komanso kusangalala ndi masewera enaake ngati mumachita masewerawo mwa apo ndi apo? N’chimodzimodzinso ndi misonkhano ya mpingo. Kupezeka pa misonkhanoyi nthawi zonse kungakuthandizeni kuti muyambe kukonda kwambiri Yehova komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumulambira. Ndipo zimenezi zingakuchititseni kuti musamafune kuphonya misonkhano.—Mateyu 5:3.
Zokuthandizani: Pambuyo pa msonkhano uliwonse, muziyesetsa kuyamikira anthu amene akamba nkhani, ngakhale mmodzi yekha. Muziwauza mfundo zimene zakuthandizani. Muzikhala ndi kope lolembamo zimene mwapindula pa msonkhanowo. Popeza kuti nkhani zambiri pa misonkhanoyi zimakhala zokhudza ntchito yathu yolalikira, mungachite bwino kukhala ndi cholinga choyesetsa kuuza anthu zinthu zimene mumakhulupirira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziona kufunika kwa nkhani zimene zimakambidwa pa misonkhano.
“Kuyambira ndili mwana, makolo anga anandiphunzitsa kufunika kopezeka pa misonkhano nthawi zonse. Choncho, sindinkajomba wamba. Zimenezi zinakhazikika kwambiri m’maganizo mwanga mpaka pano.”—Anatero Kelsey.
Mfundo yofunika kuikumbukira: Anthu amene amafika pa misonkhano nthawi zonse amasangalala ndiponso kupindula nayo kwambiri.
2. MUZIMVETSERA MWATCHERU
Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.”—Luka 8:18.
Akatswiri ena ofufuza anapeza kuti tsiku likamatha, munthu amakhala ataiwala 60 peresenti ya zinthu zimene wamva. Ngati zinthu zimenezi zikanakhala ndalama, kodi simukanayesetsa kuzisunga?
Zokuthandizani: Mukapita ku misonkhano, muzikhala pafupi ndi makolo anu m’mipando yakutsogolo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamasokonezedwe ndi zinthu zina. Komanso muzilemba mfundo za nkhani imene ikukambidwa. Ngakhale kuti anthufe timaphunzira zinthu mosiyanasiyana, kulemba mfundo kungakuthandizeni kuti muzimumvetsera kwambiri wokamba nkhani, komanso mfundozo zingadzakuthandizeni m’tsogolo.
“Kale zinkandivuta kwambiri kumvetsera ndikakhala pa misonkhano, koma panopa ndinasintha. Ndimayesetsa kukumbukira chifukwa chimene ndapitira ku misonkhanoko. Sindimangopitako mwamwambo ngati mmene anthu ena amachitira akamapita kutchalitchi. Ndimapita ku misonkhano ya mpingo kuti ndikalambire Mulungu komanso kuti ndikaphunzire zinthu zimene zingandithandize pa moyo wanga.”—Anatero Kathleen.
Mfundo yofunika kuikumbukira: Kupita ku misonkhano ya mpingo koma osamakamvetsera kuli ngati kupita kuphwando koma osakadyako chilichonse.
3. MUKAPITA KU MISONKHANO MUSAMANGOKHALA
Lemba logwirizana ndi mfundoyi: “Munthu amaphunzira kwa munthu mnzake, ngati mmene chitsulo chimanolera chitsulo chinzake.”—Miyambo 27:17 Good News Translation.
Dziwani kuti monga wachinyamata, pali zambiri zimene mungachite kuti muthandize pa misonkhano ya pampingo. Choncho muziona kuti kufika kwanu, ndemanga zimene mumapereka komanso kucheza ndi Akhristu anzanu n’zofunika kwambiri.
Zokuthandizani: Muzikhala ndi cholinga chakuti nthawi zonse mukapita ku misonkhano muziperekako ndemanga ngakhale imodzi yokha pa nkhani za mafunso ndi mayankho. Komanso mungadzipereke kugwira ntchito yoyeretsa kapena ntchito zina zimene zingafunike kugwiridwa misonkhano isanayambe, ili mkati kapena itatha. Yesetsani kuti nthawi iliyonse mukafika ku misonkhano muzichezako ndi anthu amene simucheza nawo kawirikawiri.
“Ndili ndi zaka pafupifupi 16, ndinkayesetsa kudzipereka kuti ndizigwira nawo ntchito yoperekera mayikolofoni komanso kuika mipando ndi tebulo ku pulatifomu. Kuchita zimenezi kunkandithandiza kudziona kuti ndine wofunika ndipo zinkandilimbikitsa kuti ndizipita ku misonkhano nthawi zonse mofulumira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizikonda kwambiri zinthu zauzimu.”—Anatero Miles.
Mfundo yofunika kuikumbukira: Mukapita ku misonkhano musamangokhala, muziyesetsa kuchita zinazake. Munthu amapindula akathandizira kuchita zinazake m’malo momangoonerera.
Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mr1310.com.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]
MUKUITANIDWA
Kodi mungakonde
● Kuphunzira zoona zenizeni zokhudza Mulungu?
● Kukhala ndi makhalidwe abwino?
● Kupeza anzanu abwino?
Kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova kungakuthandizeni kwambiri kuchita zimenezi komanso zinthu zina. A Mboni za Yehova amakumana ku Nyumba za Ufumu kawiri pa mlungu kuti alambire Mulungu. Aliyense ndi wolandiridwa ndipo dziwani kuti pa misonkhano imeneyi sipayendetsedwa mbale ya ndalama.
Yesetsani kuti musaphonye. Zimene zimachitika ku Nyumba ya Ufumu n’zosiyana kwambiri ndi zimene zimachitika m’matchalitchi. Zonse zimene amaphunzira pa misonkhano ya Mboni za Yehova zimachokera m’Baibulo. Mukadzafikako mudzaphunzira mmene mawu a Mulungu angakuthandizireni kukhala ndi moyo wabwino kwambiri.—Deuteronomo 31:12; Yesaya 48:17.
Sai—Nthawi yoyamba imene ndinafika ku Nyumba ya Ufumu ndinadabwa kuti kunalibe mafano, kunalibe munthu wovala ngati wansembe ndipo kunalibe amene anandiuza kuti ndipereke ndalama. Aliyense anandilandira mwansangala moti sindinkadziona ngati mlendo. Zimene zinkakambidwa pa msonkhanowu zinali zosavuta kumva komanso zinali zogwira mtima. Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti ndapeza choonadi chimene ndinkachifunafuna.
Deyanira—Ndinapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova koyamba ndili ndi zaka 14. Nditangofika aliyense anandilandira mwansangala. Aliyense anasangalala atandiona ndipo ankafunitsitsa kulankhula nane. Chifukwa cha zimenezi ndinkamasuka kupitako.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 22]
Onani nkhani zimene zikakambidwe kumpingo mlungu wotsatira. Sankhani nkhani imodzi, ndiyeno . . .
DULANI NDI KUCHITA FOTOKOPE
Malizitsani kulemba m’munsimu musanapite ku misonkhano ya mpingo.
Nkhani:
․․․․․
⇩
Zimene ndikufuna kudziwa zokhudza nkhani imeneyi:
․․․․․
Malizitsani kulemba m’munsimu mukabwera ku misonkhano ya mpingo.
Zimene ndaphunzira:
․․․․․
⇩
Mfundo zimene zandithandiza, zomwe ndingatchule poyamikira wokamba nkhaniyo:
․․․․․