Zoti Banja Likambirane
Zoti Banja Likambirane
KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA . . . Adamu ndi Hava?
KODI NTHAWI INA MUNAFUNAPO KUTENGA CHINTHU CHIMENE SICHINALI CHANU?
• Kongoletsani zithunzizi ndi chekeni. • Werengani mavesiwa ndipo muwafotokoze pomalizitsa mawu amene akusoweka. • Pezani zinthu zimene zikusoweka—(1) kamba ndi (2) chule.
GENESIS 3:4 ․․․․․
KENAKO, MULUNGU ANAWAFUNSA NGATI ANALI ATADYA CHIPATSO CHOLETSEDWA.—GENESIS 3:11
GENESIS 3:12 ․․․․․
GENESIS 3:13 ․․․․․
CHIFUKWA CHAKUTI ADAMU NDI HAVA ANABERA MULUNGU, IYE ANAWATHAMANGITSA M’MUNDA WA EDENI NDIPO PAMAPETO PAKE ANAFA.—GENESIS 3:14-24
N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava ankayenera kumvera Mulungu?
ZOKUTHANDIZANI: Chivumbulutso 4:11.
Kodi zotsatira za zimene iwo anachita n’zotani?
ZOKUTHANDIZANI: Aroma 5:12.
Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikazi?
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Ndani amene anachititsa kuti njoka ija ilankhule?
ZOKUTHANDIZANI: Chivumbulutso 12:9.
Sungani Kuti Muzikumbukira
Dulani, pindani pakati n’kusunga
KHADI LA BAIBULO 18 YOSIYA
MAFUNSO
A. Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka ․․․․․ ndipo analamulira kwa zaka ․․․․․ .
B. Kodi ndi aneneri awiri ati amene anathandiza Yosiya kuti akhale ndi makhalidwe abwino?
C. Kodi wansembe anapeza chiyani m’kachisi pamene Yosiya analamula kuti ‘nyumba ya Yehova’ ikonzedwenso?
[Tchati]
4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu
Anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 650 B.C.E.
1 C.E.
98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa
[Mapu]
Anaphwanya zifaniziro zogoba m’mizinda imene munkakhala anthu a mitundu imeneyi.—2 Mbiri 34:6, 7.
Nafitali
Manase
Efuraimu
Simiyoni
YOSIYA
ANALI NDANI?
Yosiya “anachita zoyenera pamaso pa Yehova” ngakhale kuti bambo ake, a Amoni anachita zoipa. (2 Mbiri 34:2) Iye anasankha kumvera anthu amene ankakonda Mulungu. Mulungu ankakonda kwambiri Yosiya chifukwa chakuti anali wodzichepetsa komanso ankalambira Mulungu woona.—2 Mafumu 22:19; 23:24, 25.
MAYANKHO
A. 8, 31.—2 Mbiri 34:1.
B. Yeremiya ndi Zefaniya.—Yeremiya 1:1, 2; Zefaniya 1:1.
C. Anapeza “buku la chilamulo cha Yehova,” limene Mose analemba.—2 Mbiri 34:14-18.
Anthu ndi Mayiko
3. Mayina athu ndi Sash ndi Rosette ndipo tili ndi zaka 9 ndi 8. Timakhala ku Rwanda. Kodi mukudziwa kuti ku Rwanda kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 19,000; 47,500, kapena 77,500?
4. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Rwanda.
A
B
C
D
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.mr1310.com.
● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 10
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31
1. Kamba amene ali pachithunzi chomalizira.
2. Chule amene ali pachithunzi choyamba.
3. 19,000.
4. B.