Kodi Mumakhulupirira Nyenyezi?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mumakhulupirira Nyenyezi?
Kodi mnyamata ameneyu amandikondadi?
Kodi ndinyamukedi ulendo umenewu?
Kodi andilembadi ntchito?
ANTHU ambiri amakhulupirira kuti nyenyezi zikhoza kuwathandiza kupeza mayankho a mafunso ngati amene ali pamwambawa. * Koma kodi nyenyezi zingakuthandizenidi pa moyo wanu? Kodi zingakuthandizeni kudziwa zam’tsogolo kapena za khalidwe lanu? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?
Kodi Nyenyezi Zingatithandize Kudziwa Zam’tsogolo?
Anthu ena amakhulupirira kuti zimene zimatichitikira zinalembedwa kale ndipo nyenyezi zikhoza kutithandiza kudziwa zomwe zidzatichitikire m’tsogolo. Koma Baibulo limanena zosiyana ndi zimenezi chifukwa limanena kuti Mulungu amatipatsa mwayi wosankha. Zimenezi zikutanthauza kuti aliyense ali ndi mwayi wosankha zinthu zina zimene zingakhudze tsogolo lake. Mwachitsanzo, Mulungu anauza Aisiraeli kuti: “Ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu. . . . Choncho inuyo ndi mbadwa zanu musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.”—Deuteronomo 30:19.
Ponena mawu amenewa, Yehova Mulungu ankatanthauza kuti anthu ake anali ndi ufulu wosankha zinthu zina zomwe zingakhudze tsogolo lawo. Ngati akanamvera zimene Yehova ananena akanapeza madalitso. Koma akanapanda kumvera, akanakumana ndi mavuto.
Taganizirani izi: Zikanakhala kuti tsogolo la Mwisiraeli aliyense linalembedweratu, kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu aziwauzanso kuti asankhe moyo? Komanso kodi chikanakhala chilungamo kuti Mulungu adzawalange pa zinthu zoti zinalembedweratu kale?
Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti timakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pa moyo wathu mogwirizana ndi zimene tasankha ndipo nyenyezi sizingatithandize kudziwa zimene zidzachitike pa moyo wathu.—Agalatiya 6:7.
Kodi Nyenyezi Zimakhudza Khalidwe Lathu?
Anthu ambiri omwe amakhulupirira nyenyezi amatsutsa mfundo yoti zimene zimatichitikira pa moyo wathu zinalembedwa kalekale. M’modzi mwa anthu amenewa ananena kuti: “Munthu aliyense akhoza kusankha kuti tsogolo lake likhale lotani komabe aliyense amakhala ndi khalidwe lakelake mogwirizana ndi nthawi imene anabadwa.” Anthu ambiri amakhulupiriranso zimenezi. Iwo amaona kuti popeza nyenyezi ndi mapulaneti ena zimatha kusintha zinthu zina padziko lathuli ndiye kutinso zingathe kukhudza khalidwe limene munthu amakhala nalo akamabadwa. Koma Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?
Baibulo si buku la sayansi lofotokoza chilichonse chokhudza thupi la munthu kapena zolengedwa zakuthambo. Komabe limalongosola chifukwa chimene Yehova anapangira zolengedwa zakuthambo. Lemba la Genesis 1:14, 15 limanena kuti: “Mulungu anati: ‘Kukhale zounikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku ndipo zikhale zizindikiro, komanso kuti zisonyeze nyengo . . . zikhale zounikira zakuthambo zowalitsa dziko lapansi.’”
Taganizirani izi: Kodi Mulungu sakanatiuza zikanakhala kuti analenga nyenyezi n’cholinga choti zizitithandiza kudziwa khalidwe lathu?
Choncho nyenyezi ndi zina mwa zinthu zomwe Mulungu anazilenga koma sizitithandiza kudziwa khalidwe lathu.
Kodi Tingadziwe Bwanji Zam’tsogolo?
Sikulakwa kufuna kudziwa zokhudza tsogolo lathu kapena khalidwe lathu. Koma nyenyezi sizingakuthandizeni kudziwa zimenezi.
Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndi amene amanena “za mapeto kuyambira pa chiyambi.” (Yesaya 46:10) Iye ali ndi cholinga ndipo adzachikwaniritsa m’tsogolo. (Yesaya 55:10, 11) Tingadziwe za cholinga chimenechi powerenga Baibulo. Buku lakale limeneli limafotokoza chifukwa chimene anthu akukumana ndi mavuto komanso mmene Mulungu adzathetsere mavutowo. *—2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:1-4.
Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize ngati tikufuna kukhala ndi makhalidwe abwino. Zili choncho chifukwa chakuti tikamawerenga Baibulo tingathe kudzifufuza khalidwe lathu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndi “wachifundo,” “wosakwiya msanga” komanso “wokonzeka kukhululuka.” (Ekisodo 34:6; Salimo 86:5) Kodi inuyo muli ndi makhalidwe amenewa? Baibulo lingatithandize kudziwa ngati tili ndi maganizo olakwika komanso kudziwa zimene tikufunika kusintha.
Choncho sitifunika kukhulupirira nyenyezi n’cholinga choti tidziwe za tsogolo kapena khalidwe lathu. Njira yabwino yodziwira zimenezi ndi kuwerenga Baibulo lomwe ndi ‘louziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, ndi kuwongola zinthu.’—2 Timoteyo 3:16, 17.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Anthu ena amakhulupirira kuti dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi mapulaneti angawathandize kudziwa zam’tsogolo komanso za khalidwe lawo.
^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu, werengani mutu 3, m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● N’chifukwa chiyani Mulungu analenga zolengedwa zakuthambo?—Genesis 1:14, 15.
● Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kusintha makhalidwe anu?—Aheberi 4:12.
● Kodi mungadziwe bwanji zam’tsogolo?—Yesaya 46:10.