Muzilimbikira
Munthu amalimbikira kuchita chinachake ngati waona kuti n’chaphindu.
KODI munthu angapindule bwanji ndi sukulu? Sukulu imathandiza kuti munthu adziwe zinthu kapena kuti akhale ndi nzeru ndipo Baibulo limanena kuti “nzeru zimateteza.” (Mlaliki 7:12) Kodi nzeru zimateteza bwanji? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyerekeze kuti mukudutsa malo enaake oopsa. Kodi mungasankhe kuyenda nokha kapena ndi anzanu amene angakutetezeni ngati mutakumana ndi zoopsa? Zinthu zimene mumaphunzira ku sukulu zili ngati anzanu amene angakuthandizeni pa moyo wanu wonse. Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:
Kuganiza bwino. Sukulu imathandiza munthu kuti azitha kuchita zimene Baibulo limanena kuti ndi “kudziwa zinthu komanso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21, Contemporary English Version) Zinthu zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti muthane nokha ndi mavuto anu m’malo momangodalira anthu ena.
Kukhala bwino ndi anthu. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti aziyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino ngati kuleza mtima ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Popeza munthu akakhala ku sukulu amachita zinthu ndi anthu osiyanasiyana, amakhala ndi mwayi wosonyeza makhalidwe ngati kulolera, kulemekeza ena komanso chifundo. Makhalidwe amenewa angadzamuthandizenso akadzakula.
Kukukonzekeretsani zam’tsogolo. Sukulu imathandiza munthu kuti adziwe kufunika kolimbikira ntchito, zomwe zingadzamuthandize kuti adzapeze ntchito mosavuta komanso kuti adzakhalitse pantchitopo. Kuwonjezera pamenepa, sukulu imathandizanso kuti munthu adzidziwe bwino komanso adziwe mfundo zimene amayendera. (Miyambo 14:15) Kudziwa zimenezi kungamuthandize kuti azilimba mtima kuuza ena mwaulemu zimene amakhulupirira.—1 Petulo 3:15.
Mfundo yofunika kuikumbukira: Monga taonera, sukulu ndiyofunika kwambiri. Koma mukamangoganizira zinthu zomwe sizikusangalatsani pa nkhani ya sukulu mukhoza kuyamba kudana nayo. Choncho, mungachite bwino kuganizira mfundo zimene tazifotokozazi komanso mfundo zina.
Yambani kutsatira malangizo amenewa. Sankhani ndi kuyamba kutsatira mfundo imene ingakuthandizeni kuti muzilimbikira sukulu.