Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kuthana Ndi Nsikidzi

N’zotheka Kuthana Ndi Nsikidzi

M’ZAKA za m’ma 1950, zinkaoneka kuti anthu athana ndi vuto la nsikidzi. Koma pofika m’zaka za m’ma 1970, vutoli linali lidakalipo chifukwa mayiko ambiri anali ataletsa kugwiritsa ntchito mankhwala a DDT, omwe ankathandiza kwambiri pophera nsikidzi. Mankhwalawa analetsedwa chifukwa chakuti anali oopsa komanso ankawononga zachilengedwe.

Zimenezi zinachititsa kuti vuto la nsikidzi liwonjezereke chifukwa chakuti mankhwala ena anali ochepa mphamvu. Komanso nsikidzi zinawonjezereka chifukwa anthu ankakonda kuyenda m’madera osiyanasiyana zomwe zinkachititsa kuti nsikidzizo zifalikire m’madera ena. Lipoti lina lonena za kuthana ndi nsikidzi, lomwe linatuluka mu 2012, linanena kuti: “M’zaka 12 zapitazi, nsikidzi zaswana kwambiri m’mayiko a ku United States, Canada, ku Middle East, Australia, m’mayiko ena a ku Ulaya ndi Africa.”

Akuti mumzinda wa Moscow, ku Russia, vuto la nsikidzi lakula kwambiri. Ndipo ku Australia, vuto la nsikidzi lawonjerezereka ndi 5,000 peresenti kuyambira mu 1999.

Anthu ena mosadziwa amatenga nsikidzi m’malo ngati m’masitolo, malo oonera mafilimu kapena m’mahotela. Bwana wa pa hotela ina ku United States, ananena kuti: “Masiku ano sizachilendo kupeza nsikidzi m’mahotela.” N’chifukwa chiyani nsikidzi zimavuta kupha? Kodi mungatani kuti mupewe vuto la nsikidzi? Ngati m’nyumba mwanu muli nsikidzi, kodi mungatani kuti muthane nazo?

Sizifa Chisawawa

Chifukwa chakuti nsikidzi ndi zazing’ono kwambiri zimabisala paliponse. Mwachitsanzo zimapezeka m’mphasa, m’matilesi, m’mipando, m’masiwitchi a magetsi komanso mu wailesi. Nsikidzi zimakonda kukhala pafupi ndi pamene anthu amagona kapena kukhala n’cholinga choti ziziwayamwa magazi. *

Nthawi zambiri nsikidzi zimakonda kuluma anthu akagona. Koma anthu ambiri samadziwa kuti nsikidzi ikuwaluma chifukwa ikamaluma imalavulira madzi enaake omwe amachititsa kuti munthu asamve kena kalikonse, mwina kwa mphindi 10. Ndipo chodabwitsa n’chakuti nsikidzi zimatha kukhala osadya kwa miyezi yambiri.

Koma mosiyana ndi tizilombo tina ngati udzudzu, nsikidzi sizifalitsa matenda. Komabe zimati zikaluma, munthu amamva kuyabwa ndipo nthawi zina pamene walumidwapo pamatupa. Anthu ambiri amakhalanso ndi nkhawa chifukwa cha nsikidzi. Anthu amene m’nyumba mwawo muli nsikidzi amasowa tulo, amakhala mwamanyazi ndipo nthawi zina ngakhale nsikidzizo zitatha iwo amamva ngati zikuwalumabe. Lipoti lina la ku Sierra Leone, linanena kuti: “Nsikidzi zimasowetsa tulo komanso mtendere ndipo ngati zapezeka m’nyumba mwako umachita manyazi.”

Kodi Mungathane Nazo Bwanji?

Nsikidzi zikhoza kupezeka m’nyumba mwa aliyense, koma mukhoza kuthana nazo ngati mutazitulukira mwansanga. Choncho mukakhala panyumba kapena paulendo muzikhala tcheru kuti muone ngati pamene mulipo pali nsikidzi. Muzifufuza m’katundu wanu wam’nyumba ngati m’mipando kuti mudziwe ngati muli timazira ta nsikidzi tomwe timaoneka ngati tinjere kapena ngati muli timadontho tamagazi. Mungagwiritse ntchito tochi kuti muone bwinobwino.

Musalole kuti m’nyumba mwanu muzipezeka nsikidzi. Muzionetsetsa kuti mwamata ming’alu yapakhoma ndi m’mafelemu. Ngakhale kuti nsikidzi sizimabwera chifukwa cha uve, mungathe kuzipewa ngati mutamasesa kawirikawiri komanso kupewa kuunjika katundu. Ngati mwapita ku hotela, mungachite bwino kupewa kuika chikwama chanu pabedi kapena pansi kuti musatenge nsikidzi.

Zimene Mungachite Ngati M’nyumba Mwanu Muli Nsikidzi

Nthawi zambiri m’nyumba kapena muhotela mukapezeka nsikidzi, mungade nkhawa mwinanso kuchita manyazi. Mwachitsanzo, Dave ndi mkazi wake atapita ku holide anakalumidwa ndi nsikidzi. Dave anati: “Tinachita manyazi kwambiri moti tinkada nkhawa kuti tikapita kunyumba tizikati chiyani. Tinkada nkhawa kuti anzathu akangomva kuyabwa azingoti ndi nsikidzi zimene tinawapatsira.” Ngakhale kuti mungakhale ndi nkhawa komanso manyazi mukapezeka ndi nsikidzi, musamachite manyazi kupempha ena kuti akuthandizeni. Dipatimenti ya ku New York City, yoona za umoyo inanena kuti: “N’zoona kuti nsikidzi zimavuta kupha, koma n’zotheka kuthana nazo.”

Muzifufuza kuti muone ngati m’nyumba mwanu muli nsikidzi ndipo pezani njira zoti nsikidzizo zisamapeze pobisala

Koma kupha nsikidzi ndi ntchito yaikulu. Ngati mwaona kuti m’nyumba mwanu muli nsikidzi, pezani munthu wopha tizilombo wovomerezedwa ndi boma. Ngakhale kuti mankhwala amene tawatchula aja sakugwiritsidwanso ntchito masiku ano, anthu opha tizilombo amagwiritsa ntchito mankhwala osiyanasiyana pophera nsikidzi. Katswiri wina wofufuza tizilombo ting’onoting’ono, dzina lake Dini M. Miller, anati: “Kuti muthane ndi nsikidzi, pamafunika kuti amene akukhala m’nyumbamo, eni ake a nyumbayo komanso opha tizilombo achite zinthu mogwirizana.” Ngati mutatsatira malangizo a anthu opha tizilombo komanso kuyesetsa kusamalira m’nyumba mwanu, mukhoza kuthana ndi vuto la nsikidzi.

^ ndime 7 Akatswiri ofufuza tizilombo ting’onoting’ono amanena kuti nsikidzi zimayamwa magazi a anthu ndi nyama zina monga amphaka ndi agalu.