Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Panama

Panama

KU PANAMA n’kotchuka kwambiri chifukwa cha ngalande yaikulu yomwe imalumikizitsa nyanja ya Atlantic ndi ya Pacific. Komanso anthu a ku North ndi South America amadutsa ku Panama akafuna kuyenderana. M’dzikoli muli anthu a mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Ambiri mwa anthu akumeneku makolo awo anachokera ku Ulaya.

KODI MUKUDZIWA? Ku Panama kuli achule amtundu winawake (Atelopus zeteki) omwe amabayibitsa akafuna kukopana kapena kuchenjezana

Mu 1501, anthu ofufuza malo ochokera ku Spain anayamba kufika ku Panama ndipo anapeza mitundu yosiyanasiyana ya anthu, yomwe ina imapezekabe mpaka pano. Umodzi mwa mitundu imeneyi ndi mtundu wa anthu otchedwa Guna (womwe poyamba unkadziwika kuti Kuna). Anthu ambiri a mtundu umenewu amapezeka pa zilumba za San Blas zomwe zili  m’mphepete mwa nyanja ya Pacific kumalire a dziko la Panama ndi Colombia. Iwo amasaka nyama, kuwedza nsomba komanso kulima.

Anthu a mtundu wa Guna amati mwamuna akakwatira amakakhala kuchikamwini. Koma akabereka mwana wamkazi amasamuka kuchikamwiniko n’kukayamba kukhala kwaokha.

Ku Panama kuli mipingo ya Mboni za Yehova pafupifupi 300. Mipingo yambiri ndi ya Chisipanishi koma ina ndi ya Chitchainizi, Chingelezi, Chigujarati, Chiguna, Chikiliyo cha ku Haiti, Chingabere ndi Chinenero chamanja cha ku Panama.