ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Azerbaijan
AZERBAIJAN ndi dziko lalikulu kwambiri pa mayiko atatu amene ali ku chigawo chakum’mwera kwa dera la Caucasus. Zaka masauzande m’mbuyomu, anthu ambiri a mtundu wa Chitheke anayamba kukhala m’dera limeneli. Alendowa anayamba kutengera zikhalidwe za anthu amene anawapeza m’derali ndipo anthuwo anayamba kutengeranso zikhalidwe za alendowo. N’chifukwa chake chilankhulo cha anthu a ku Azerbaijan chimafanana ndi Chitheke.
Anthu a ku Azerbaijan amadziwika kuti ndi ansangala komanso okonda kulandira alendo. Anthu ake amakondana kwambiri ndipo amadalirana akakumana ndi mavuto.
Anthu a ku Azerbaijan amakonda nyimbo komanso ndakatulo. Pali nyimbo zina zotchedwa mugam. Poimba nyimbozi, munthu mmodzi amalakatula ndakatulo za ku Azerbaijan pomwe ena amakhala akuimba zida. Munthu woimba nyimbozi amafunika akhale woti amadziwa bwino kaimbidwe ka nyimbo za mugam komanso woti akhoza kupeka nyimbo nthawi yomwe akuimbayo.
Anthu a ku Azerbaijan amakonda kumwa tiyi. Amamwera tiyiyu m’makapu a galasi ndipo amathiramo shuga ndi zinthu zina zokometsera. Malo ogulitsira tiyi amapezeka m’madera ambiri ndi m’midzi momwe.
Nsomba zotchedwa sturgeon zimapezeka m’nyanja ya Caspian yomwe ili kum’mawa kwa dziko la Azerbaijan. Nsombazi zimatha kukhala ndi moyo zaka 100. Nsomba yaikulu yomwe inagwidwapo inali yaikulu mamita 8.5, ndipo inkalemera makilogalamu 1,297. Anthu amakonda nsombazi chifukwa cha mazira ake omwe ndi chakudya chokwera mtengo kwambiri.
Anthu a ku Azerbaijan amakonda kupemphera komanso kukambirana zokhudza Mulungu. Koma ambiri ndi Asilamu. Kumapezekanso magulu ena a zipembedzo kuphatikizapo a Mboni za Yehova oposa 1,000. Ambiri mwa anthu amenewa ndi nzika zoyambirira kukhala m’dzikoli.
KODI MUKUDZIWA?
A Mboni za Yehova amaphunzitsa Baibulo anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse pogwiritsa ntchito buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli likupezeka m’zinenero zoposa 250 kuphatikizapo Chiazebajani.