ZITHUNZI ZAKALE
Zheng He
“Tadutsa pamadzi ulendo wa ma li * oposa 100,000 ndipo takumana ndi mafunde aakuluakulu ngati mapiri. Taona madera osiyanasiyana akutali kwambiri . . . Zombo zathu zinkayenda usana ndi usiku komanso zinkathamanga kwambiri ngati nyenyezi. Ndipo pa maulendo athuwa tinkalimbana ndi mafunde.”—Mawu amenewa analembedwa ndi Zheng He m’zaka za m’ma 1400, mumzinda wa Changle, m’chigawo cha Fujian ku China.
DZIKO la China ndi lalikulu komanso lili ndi anthu ambiri. Ku China ndi kumenenso kunamangidwa mpanda waukulu, womwe ndi chimodzi mwa zinthu zakale zotchuka kwambiri. Kunalinso zombo zazikulu komanso zochuluka. Zombo zimenezi zinapangidwa ndi Yongle komanso Xuande, omwe anali olamulira a ku China. Panadutsa zaka 500 kuti anthu apangenso zombo zazikulu komanso zochuluka kuposa zimenezi. Amene ankatsogolera zombozi anali Zheng He yemwe anali Msilamu ndipo ankachokera kum’mwera chakumadzulo kwa China.
CHOLINGA CHA MAULENDOWA
Mawu amene ali kumayambiriro kwa nkhaniyi ndi ena mwa mawu amene Zheng He ananena pofotokoza cholinga cha maulendo akewo. Iye ananena kuti cholinga chake ndi “kudziwitsa anthu a kumadera akutali za ufumu wa kwawo komanso kuwachitira zinthu zabwino.” Chifukwa cha maulendo ake ataliataliwo, Zheng He ananenanso kuti: “Mayiko akutali kwambiri ali pansi pa [dziko la China]. . .Ngakhale alendo ochokera m’mayiko a kutsidya kwa nyanja . . . akhala akubwera ndi mphatso komanso zinthu zamtengo wapatali.”
Anthu amanena zifukwa zosiyanasiyana zomwe olamulirawa ankakonzera maulendo ataliatali amenewa. Ena amanena kuti Zheng He anali chabe nthumwi ya dziko lomwe linali lamphamvu kwambiri koma lamtendere. Pomwe ena amaona kuti maulendo akewo anali ndi cholinga chofuna kuti mayiko ena akhale pansi pa ulamuliro wa China. Iwo amaganiza choncho chifukwa chakuti Zheng He ankapereka mphatso zapamwamba kwambiri komanso ankathandiza mayiko amene ankamulandira bwino. Koma amene ankakana kupereka mphatso kwa mfumu ya ku China kapena amene sankachita zimene iwo akufuna, ankamenyana nawo n’kuwatenga ukapolo. Chifukwa cha maulendo amenewa, mayiko ambiri ozungulira nyanja yamchere ankatumiza nthumwi zawo kuti zikapereke mphatso kwa mfumu ya ku China.
Zombo za Zheng He zinkanyamulanso zokongoletsa, dongo lapadera lopangira zinthu zosiyanasiyana komanso nsalu za ku China kuti azikapanga malonda m’madoko akutali. Iwo ankabwerako ndi miyala ya mtengo wapatali, nyanga, zokometsera zakudya, matabwa komanso zinthu zina zomwe anthu a ku China ankaziona kuti ndi zapamwamba kwambiri. Nthawi ina anabwera ndi nswala, yomwe anthu anachita nayo chidwi kwambiri. Chifukwa cha malonda komanso maulendo amene ankachitika m’zaka za m’ma 1400 amenewa, dziko la China linatukuka kwambiri.
Koma maulendo amenewa sanapite patali chifukwa Zheng He atasiya kuyenda maulendo ake, dziko la China linasiyanso kuchita malonda ndi mayiko ena. Wolamulira watsopano wa ku China ndi mlangizi wake ankaona kuti dziko la China ndi lotukuka kwambiri ndipo anaganiza zosiya kuchita zinthu ndi mayiko ena. Posafuna kuti anthu adziwe zimene dziko la China linkachita mbuyomo, wolamulira watsopanoyo anawononga zombo zonse kuphatikizapo chilichonse chokhudzana ndi maulendo amenewa. Moti anthu a ku China komanso a mayiko ena angodziwa posachedwapa za maulendo apanyanja a Zheng He.
^ ndime 3 Li ndi muyezo umene anthu a ku China ankagwiritsa ntchito kale kwambiri poyezera kutalika kwa zinthu. Muyezowu wakhala ukusinthasintha koma zikuoneka kuti m’nthawi ya Zheng He, ‘li’ imodzi inali muyezo wa mamita pafupifupi 500.