Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Belize

Dziko la Belize

DZIKO la Belize ndi laling’ono koma lili ndi zinthu zambiri zachilengedwe. Kuli zinthu monga nkhalango zikuluzikulu, nyanja yokhala ndi madzi okongola komanso zilumba zambiri. Koma si zokhazi. M’dzikoli mulinso zinthu zina zambiri zochititsa chidwi.

Ku Belize kuli mitundu yosiyanasiyana ya mbalame komanso nyama zakutchire. Mwachitsanzo, kuli mbalame yotchedwa toucan yomwe imakhala ndi mitundu yosiyanasiyana yowala. Kulinso nyama inayake yotchedwa Baird tapir yooneka ngati chipembere ndipo imayenda mofulumira kwambiri m’madzi ndi pamtunda pomwe. Komanso kuli nyama zinazake zamphamvu kwambiri zooneka ngati kambuku zomwe zimakonda kukhala zokha. Dziko la Belize ndiye linali loyamba kukhala ndi malo otetezera nyama zooneka ngati akambukuzi.

Dziko la Belize ndiye linali loyamba kukhala ndi malo otetezera nyama zooneka ngati akambuku

Poyamba m’dzikoli munkakhala anthu otchedwa Amaya. M’zaka za m’ma 1500, asilikali a ku Spain anafika m’dzikoli n’cholinga chofuna kugonjetsa Amaya koma sanawagonjetseretu. Kenako asilikali a ku Britain analanda dzikoli ndipo mu 1862 dziko la Belize linakhala m’manja mwa dziko la Britain. Dziko la Belize linalandira ufulu wodzilamulira mu 1981.

 Ku Belize kuli mitundu ya anthu osiyanasiyana monga Akiliyoli, Amwenye, Agarifuna, Amaya ndi Amesitizo. Anthu a m’dzikoli ndi ansangala komanso aulemu. Nthawi zambiri ana akamaitana akuluakulu, amanena kuti “Achemwa” kapena “Achimwene” ndipo akamayankha anthu akuluakulu amanena kuti, “Chabwino mayi” kapena “Ayi bambo.”

Msika wina wa mumzinda wa Belize

M’dzikoli muli mipingo ya Mboni za Yehova ya zinenero zosiyanasiyana monga, Chijeremani, Chikiliyo cha ku Belize, Chimandarini cha ku China, Chimaya, Chingelezi, Chisipanishi ndi chinenero chamanja cha ku America. M’chaka cha 2013, munthu mmodzi pa anthu 40 alionse a m’dzikoli anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umene a Mboni za Yehova anachita.

KODI MUKUDZIWA? M’nyanja ya ku Belize muli zomera zotchedwa coral reef ndipo zinayanga mtunda wa makilomita oposa 290. Padziko lonse, ndi ku Australia kokha kumene kuli zomera za mtunduwu zochuluka kuposa pamenepa.

Padziko lonse, ku Australia n’kumene kuli zomera zotchedwa coral reef zochuluka kwambiri