Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Moyo

Kulemekeza Moyo

N’CHIFUKWA CHIYANI KULEMEKEZA MOYO N’KOFUNIKA?

Zochita komanso makhalidwe amene amasonyeza kuti sitikulemekeza moyo zikhoza kuwononga thanzi lathu komanso kuvulaza anthu ena.

  • Kusuta fodya sikuti kumangoyambitsa khansa basi, koma kumachititsanso thupi kuti lizilephera kulimbana ndi tizilombo toyambitsa matendawa. Pa anthu 100 alionse amene anamwalira ndi matenda a khansa ya m’mapapo, anthu 90 anayamba kudwala matendawa chifukwa choti ankasuta, kapena chifukwa choti ankapuma utsi wa fodya umene ena ankasuta.

  • Chaka chilichonse anthu ambiri amasokonezeka maganizo chifukwa cha mantha omwe amabwera chifukwa cha zachiwawa zowombera ndi mfuti. Kafukufuku wina akusonyeza kuti “ngakhale anthu amene sanavulazidwe [pamene achiwembu anawombera pasukulu yawo], amakhala akuvutikabe maganizo kwa nthawi yaitali.”—Stanford University.

  • Anthu amene amayendetsa galimoto atamwa mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, amaika pachiopsezo moyo wa anthu ena. Anthu amene amachita zinthu zosonyeza kuti sakulemekeza moyo, nthawi zambiri amachititsa kuti anthu osalakwa avulale.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZILEMEKEZA MOYO

Muziteteza thanzi lanu. N’zotheka kusiyiratu zizolowezi zoipa monga kusuta, kugwiritsa ntchito shisha kapena kuti kuvepa, kumwa mowa kwambiri kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Zizolowezi zimenezi zimawononga moyo wanu komanso zimasonyeza kuti simukulemekeza moyo wa anthu ena kuphatikizapo anthu a m’banja lanu.

“Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”—2 Akorinto 7:1.

Muzipewa ngozi. Kuti mupewe ngozi muzionetsetsa kuti nyumba yanu ndi yokonzedwa bwino nthawi zonse. Muziyendetsa galimoto mosamala ndipo muzionetsetsa kuti ndi yokonzedwa bwino. Musamalole kuti anthu ena akukakamizeni kuchita zinthu zimene zingachititse ngozi kapena imfa.

“Mukamanga nyumba yatsopano muzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti nyumba yanu ingakhale ndi mlandu wa magazi ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.”—Deuteronomo 22:8. a

Muzikhala okoma mtima. Kulemekeza moyo kumaphatikizapo mmene timaonera anthu amitundu komanso mayiko onse, kaya ndi olemera kapena osauka, ophunzira kapena osaphunzira. Ndipotu tsankho komanso chidani ndi zomwe zimachititsa kuti padzikoli pazichitika zachiwawa komanso nkhondo.

“Chidani chachikulu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata, mawu achipongwe komanso zinthu zonse zoipa zichotsedwe mwa inu. Koma muzikomerana mtima.”—Aefeso 4:31, 32.

ZIMENE TIKUCHITA POLEMEKEZA MOYO

A Mboni za Yehova amaphunzitsa ena zimene angachite kuti akhale ndi moyo wathanzi. Timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asiye zizolowezi komanso makhalidwe amene angawononge moyo wawo.

Timatsatira kwambiri malangizo okhudza kupewa ngozi tikamagwira ntchito zomangamanga. Anthu amene amadzipereka kuti akagwire nawo ntchito yomanga malo amene timasonkhana komanso amene timagwiritsa ntchito kuti tipititse patsogolo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo, amaphunzitsidwa mmene angapewere ngozi. Nyumba zathu zimayenderedwa nthawi ndi nthawi kuti titsimikizire ngati zili bwino pofuna kutsatira malangizo okhudza kupewa ngozi a m’dera limene nyumbazi zili.

Timathandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi. M’miyezi ina 12 ya posachedwapa, tinathandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi zoposa 200 padziko lonse, ndipo tinagwiritsa ntchito ndalama pafupifupi madola 12 miliyoni zimene anthu anapereka mwa kufuna kwawo pothandiza anthu omwe anakhudzidwawo.

Pamene mliri wa Ebola unavuta kwambiri ku West Africa (mu 2014) komanso ku Democratic Republic of Congo (mu 2018), tinaphunzitsa anthu mmene angapewere kufala kwa matenda oopsa kwambiriwa. Tinatumiza anthu kuti akalankhule kwa anthu omwe anaikidwa m’magulu osiyanasiyana pa nkhani ya mutu wakuti “Kumvera Kumateteza.” Tinaika zipangizo zosambira m’manja pamakomo a malo athu onse olambirira komanso tinalimbikitsa anthu kufunika kosamba m’manja komanso kuchita zinthu zimene zingateteze moyo wawo.

Ku Sierra Leone, pa wailesi anapereka chilengezo choyamikira a Mboni za Yehova chifukwa chothandiza a Mboni anzawo komanso anthu omwe sanali a Mboni a m’dera lawo za mmene angapewere kachilombo ka Ebola.

Bigili losambira m’manja pa Nyumba ya Ufumu pa nthawi imene ku Liberia kunali mliri wa Ebola mu 2014

a Kalekale ku Middle East, anthu ankafunika kutsatira lamulo limeneli. Kuchita zimenezi kunkasonyeza kuti akusamala moyo wa anthu a m’banja lawo komanso wa anthu ena.