Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekezana M’banja

Kulemekezana M’banja

N’CHIFUKWA CHIYANI KULEMEKEZANA M’BANJA N’KOFUNIKA?

Kulemekezana m’banja kumachititsa kuti m’banjamo muzikhala mtendere ndipo mwamuna, mkazi komanso ana amamva kuti ndi otetezeka.

  • Buku lina linanena kuti anthu okwatirana akamalemekezana, amasonyeza kuti amakondana kwambiri “osati pochitirana zinthu zikuluzikulu zokha koma ngakhalenso zing’onozing’ono tsiku lililonse.”—The Seven Principles for Making Marriage Work.

  • Kafukufuku akusonyeza kuti ana amene amaphunzira kulemekeza ena amakhala osangalala, amagwirizana kwambiri ndi makolo awo komanso savutika kwambiri maganizo.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZILEMEKEZANA M’BANJA LANU

Muzikhala ndi pulani, limodzi ndi banja lanu. Choyamba, onetsetsani kuti mukudziwa kuti mukati “ulemu” mumatanthauza chiyani. Chachiwiri, lembani makhalidwe amene mukufuna kuti aliyense m’banja lanu aziwasonyeza komanso amene mukufuna kuti aziwapewa. Chachitatu, kambiranani pulaniyo monga banja n’cholinga choti inuyo komanso ana anu mudziwe bwino zomwe mungachite kuti muzisonyeza ulemu.

“Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino.”—Miyambo 21:5.

Muzikhala chitsanzo. Kodi mumaimba mlandu anthu a m’banja lanu chifukwa cha zimene alakwitsa, kuwanyoza akapereka maganizo awo kapena kusawalabadira komanso kuwadula mawu akamalankhula?

Zimene Zingakuthandizeni: Muziyesetsa kuona ulemu ngati ngongole yoti mubweze kwa mwamuna kapena mkazi wanu komanso ana anu, osati ngati malipiro a zinazake zimene achita.

“Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.”—Aroma 12:10.

Muzikhalabe aulemu ngakhale pamene mukusiyana maganizo. Muzipewa kunena mawu ngati akuti, “mumakonda kuchita zakuti” kapena “simuchita zakuti.” Mawu amenewa amakhala opweteka komanso onyoza ndipo angachititse kuti nkhani yaing’ono ikule kwambiri n’kufika pa mkangano.

“Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

ZIMENE TIKUCHITA POLIMBIKITSA KUTI ANTHU AZILEMEKEZANA M’BANJA

A Mboni za Yehova amalimbikitsa anthu onse m’banja kuti azilemekezana ndipo nthawi zambiri nkhani zimenezi zimapezeka m’mabuku, timabuku komanso mavidiyo zomwe amafalitsa kwaulere.

KWA ANTHU OKWATIRANA: Nkhani za mutu wakuti Mfundo Zothandiza Mabanja zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti . . .

  • azimvetsera bwino mnzawo akamalankhula

  • asamasiye kulankhulana akasemphana maganizo

  • asiye kukangana

(Fufuzani mawu akuti “Mfundo Zothandiza Mabanja” pa jw.org)

KWA MAKOLO: Nkhani za mutu wakuti Mfundo Zothandiza Mabanja zingathandize makolo kuphunzitsa ana awo kuti . . .

  • akhale omvera

  • azigwira ntchito zapakhomo

  • azipempha zinthu mwaulemu komanso azithokoza

(Fufuzani mawu akuti “Kulera Ana” komanso “Kulera Ana Achinyamata” pa jw.org)

Onaninso zakumapeto zakuti “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa” m’buku lakuti, “Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa”—Buku Loyamba. (Fufuzani mawu akuti “Mafunso Amene Makolo Amadzifunsa” pa jw.org)

KWA ACHINYAMATA: Gawo lakuti Achinyamata pa jw.org lili ndi nkhani, mavidiyo komanso zoti achinyamata achite zomwe zingawathandize kuti . . .

  • azigwirizana ndi makolo komanso achibale awo

  • azilankhulana mwaulemu ndi makolo awo pa malamulo amene makolowo anakhazikitsa

  • makolo awo aziwakhulupirira

(Fufuzani mawu akuti “Achinyamata” pa jw.org)

Kugwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org ndi kwaulere. Simufunika kulipira ndalama iliyonse kapena kulembetsa komanso simuuzidwa kuti mulembe zokhudza inuyo.