Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nkhawa

Nkhawa

Nkhawa zina zimakhala zothandiza koma zina zimangotibweretsera mavuto. Baibulo limatithandiza kudziwa nkhawa zoyenera ndi zosayenera.

Kodi pali amene sakhala ndi nkhawa?

ZIMENE ZIMACHITIKA

Munthu akakhala ndi nkhawa amapanikizika, amachita mantha komanso amangodandaula. Popeza tikukhala m’dziko limene zinthu zimangosintha nthawi iliyonse, munthu aliyense akhoza kukhala ndi nkhawa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mfumu Davide ananena kuti: “Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti? Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?” (Salimo 13:2) Koma kodi n’chiyani chinkamuthandiza Davide? Ankapemphera kwa Yehova n’kumuuza zomwe zinkamudetsa nkhawa ndipo ankakhulupirira kuti amuthandiza. (Salimo 13:5; 62:8) Ndipotu Mulungu amatilimbikitsa kuti tizimuuza zamumtima mwathu. Lemba la 1 Petulo 5:7 limati: “Chitani zimenezi pamene mukumutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”

Tikamathandiza anthu ena zimatithandiza kuchepetsako nkhawa

Koma pali zinthu zinanso zomwe tingachite pofuna kulimbana ndi nkhawa zathu. Mwachitsanzo, nthawi ina mtumwi Paulo anadera nkhawa “mipingo yonse,” ndipo anayesetsa kukalimbikitsa Akhristu akumipingo imeneyo. (2 Akorinto 11:28) Apa tingati nkhawa za Paulo zinachepa chifukwa chakuti anayesetsa kukathandiza anthu akumipingoyo. Choncho nkhawa zake zinali zothandiza chifukwa zinamuchititsa kuti akathandize anthu ena. Ifenso tikhoza kuthandiza anthu ena ngati timawadera nkhawa. Koma ngati sitidera nkhawa abale athu, tingasonyeze kuti tilibe chikondi.—Miyambo 17:17.

“Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”Afilipi 2:4.

Kodi mungatani kuti musamade nkhawa kwambiri?

ZIMENE ZIMACHITIKA

Anthu amakhala ndi nkhawa chifukwa choganizira zinthu zolakwika zomwe anachita m’mbuyo, kuganizira zam’tsogolo kapenanso chifukwa cha nkhani za ndalama. *

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuganizira zinthu zolakwika zomwe tinachita m’mbuyo: M’nthawi ya atumwi, anthu ena asanakhale Akhristu anali zidakwa, olanda, adama komanso akuba. (1 Akorinto 6:9-11) Koma m’malo momangoganizira zinthu zomwe ankachita m’mbuyozo, anasintha ndipo ankakhulupirira kuti Mulungu anawasonyeza chifundo chachikulu. Lemba la Salimo 130:4 limati: “Inu [Mulungu] mumakhululukiradi, kuti anthu akuopeni.”

Kudera nkhawa zam’tsogolo: Yesu Khristu ananena kuti “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.” (Mateyu 6:25, 34) Kodi iye ankatanthauza chiyani pamenepa? Ankatanthauza kuti tizithana ndi mavuto omwe takumana nawo pa nthawiyo. Tisamapanikizike kwambiri ndi nkhawa chifukwa choganizira zinthu zomwe zingadzatichitikire m’tsogolo. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tisamachite zinthu mosaganiza bwino. Tizikumbukiranso kuti zinthu zambiri zomwe zimatidetsa nkhawa, sizingachitike n’komwe.

Kudera nkhawa za ndalama: Solomo amene anali munthu wanzeru, anapemphera kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma.” (Miyambo 30:8) M’malomwake iye ankakhutira ndi zomwe anali nazo ndipo zinachititsa kuti Mulungu azimukonda. Lemba la Aheberi 13:5, limati: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’” Ndalama sizingatithandize pa zinthu zonse. Koma nthawi zonse Mulungu amathandiza anthu amene amam’khulupirira komanso kukhala ndi moyo wosafuna zambiri.

“Sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.”Salimo 37:25.

Kodi zidzatheka kukhaliratu opanda nkhawa?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Mtolankhani wa nyuzipepala ina analemba kuti “Tikulowa m’nthawi imene palibe amene angapewe kukhala ndi nkhawa.” (The Guardian) Mtolankhani winanso analemba kuti, “Anthu ambiri a ku America akuvutika kwambiri ndi nkhawa.”–The Wall Street Journal

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miyambo 12:25) Ndipo “mawu abwino” amapezeka mu ‘uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ (Mateyu 24:14) Ufumu umenewu ndi boma la Mulungu ndipo udzachita zinthu zomwe patokha sitingakwanitse. Udzathetsa nkhawa zathu zonse potichotsera zinthu zomwe zimayambitsa mavuto kuphatikizapo matenda komanso imfa. “[Mulungu ] adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.

“Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu.”Aroma 15:13.

^ ndime 10 Anthu amene amavutika kwambiri ndi nkhawa ayenera kukaonana ndi adokotala. Galamukani! sisankhira anthu mankhwala kapena njira inayake yochizira matenda.