Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisonyeza Chikondi

Muzisonyeza Chikondi

Vuto Limene Limakhalapo

Maganizo atsankho amakhala ovuta kuwachotsa, ngati mmene zimakhaliranso ndi kachirombo koyambitsa matenda ka vairasi. Pamafunika nthawi komanso khama kuti tichotse tsankho mumtima mwathu. Ndiye kodi mungatani kuti mukwanitse kuchita zimenezi?

Mfundo ya M’Baibulo

“Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—AKOLOSE 3:14.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Kuchita zinthu zokomera mtima anthu ena kumathandiza kuti anthu azigwirizana. Ndiye mukamasonyeza kwambiri chikondi kwa ena, maganizo atsankho amakuchokerani. Mukaphunzira kukonda ena kwambiri zidzakuthandizani kuti musamawaganizire zolakwika.

Zimene Mungachite

Ganizirani zimene mungachite kuti musonyeze chikondi anthu amtundu umene mwakhala mukuuona molakwika. Sikuti mufunika kuwachitira chinachake chachikulu. Mungayese kuchita chimodzi kapena zingapo mwa izi:

Chilichonse chimene mungachite posonyeza ena chikondi, chidzakuthandizani kuchepetsa mtima watsankho

  • Mungawasonyeze kuti ndinu munthu wakhalidwe labwino powatsegulira chitseko kapena powauza kuti akhale pampando umene mwakhala m’basi ngati iwo aimirira.

  • Yesani kukamba nawo tinkhani apa ndi apo ngakhale atakhala kuti sadziwa bwinobwino chilankhulo chanu.

  • Muzikhala oleza mtima akachita zinthu mwa njira imene simukuimvetsa.

  • Muziwamvera chisoni akamafotokoza mavuto awo.