ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Kyrgyzstan
DZIKO la Kyrgyzstan lili ku Central Asia ndipo linayandikana ndi mayiko a Kazakhstan, Uzbekistan, Tajikistan, ndi China. Malo aakulu kwambiri m’dzikoli kuli mapiri okhaokha omwe ndi aatali. Pamwamba pa mapiriwa pamazizira kwambiri moti mpaka pamapezeka madzi oundana. Dzikoli linatenga mbali yaikulu ya mapiri a Tian Shan omwe ndi aalitali mamita 7,439. Ku Kyrgyzstan kulinso nkhalango yaikulu kwambiri ya mitengo inayake yobereka zipatso zokhala ndi mtedza mkati mwake. Mitengoyi ili m’gulu la mitengo ikuluikulu padziko lonse.
Anthu a ku Kyrgyzstan ndi okonda kuchereza komanso aulemu. Akamayankhula ndi munthu wamkulu amagwiritsa ntchito mawu aulemu akuti “inu.” Ndipo amasiyira akuluakulu malo abwino oti akhale akakwera basi komanso akamadya chakudya.
Mabanja ambiri m’dzikoli amakhala ndi ana atatu kapena kuposerapo. Nthawi zambiri mwana wamwamuna womaliza amakhalabe ndi makolo ake ngakhale atakwatira. Amachita zimenezi kuti azisamalira makolo ake kwa moyo wawo wonse.
Makolo amaphunzitsa ana awo aakazi maluso osiyanasiyana kuyambira ali aang’ono n’cholinga choti akadzakwatiwa adzakhale akazi abwino. Ndipo mwana wamkazi wazaka zapakati pa 14 ndi 16 amakhala atadziwa bwino ntchito zonse zapakhomo. Nthawi zambiri makolo amakonzeratu mphatso zoti adzapereke kwa mwamuna amene adzakwatire mwana wawo. Amapereka mphatso monga zofunda, zovala komanso kapeti yopanga pamanja. Nayenso mwamuna amapereka ndalama kapena ziweto.
Anthu a m’dzikoli amapha nkhosa kapena hatchi pa zisangalalo kapenanso pa maliro. Ndipo chiwalo chilichonse cha nyamayo chimakhala ndi tanthauzo linalake. Ndiyeno mlendo aliyense yemwe wabwera pamwambowo amapatsidwa chiwalo chinachake potengera msinkhu kapena udindo womwe ali nawo. Anthuwa amachita zimenezi chifukwa chakuti amalemekezana kwambiri. Zikatere amapatsa alendowo chakudya chomwe anthu am’dzikoli amadya chotchedwa beshbarmak. Chakudyachi amachidya ndi manja.