ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la New Zealand
PAFUPIFUPI zaka 800 zapitazo, anthu a mtundu wa Maori anasamuka ku Polynesia n’kuyenda mtunda wautali kwambiri panyanja yayikulu n’kukakhazikika ku New Zealand. Ku Polynesia n’kotentha kwambiri kusiyana ndi ku New Zealand. Ku New Zealand kuli mapiri ambiri, madzi oundana, akasupe amadzi otentha komanso kumagwa sinowo kapena kuti chipale chofewa. Patatha zaka 500, anthu enanso ochokera ku Europe komwe ndi kutali kwambiri, anabwera kudzakhazikika m’dzikoli. Chikhalidwe cha anthu a ku New Zealand panopo, n’chosakanikirana ndi cha anthu a ku Britain, Germany komanso Polynesia. Anthu pafupifupi 90 pa 100 aliwonse m’dzikoli, amakhala m’tauni. Mzinda wa Wellington womwe ndi likulu la dzikoli, umadziwika kuti ndi likulu la kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi.
Dziko la New Zealand lili ndi malo ambiri ochititsa chidwi. Choncho ngakhale kuti lili kutali kwambiri, alendo pafupifupi 3 miliyoni amalowa m’dzikoli chaka chilichonse kudzaona malowa.
Ku New Zealand kuli nyama komanso zachilengedwe zambiri. Ndipo ndi dziko lokhali padziko lonse lapansi lomwe lili ndi mitundu yambiri ya mbalame zomwe siziuluka. Kumapezekanso mtundu winawake wa abuluzi otchedwa tuatara, omwe umatha kukhala ndi moyo mpaka zaka 100. Nyama zoyamwitsa za m’dzikoli ndi monga mitundu yochepa ya mileme komanso nsomba zikuluzikulu ngati anangumi ndi ma dolphin.
A Mboni za Yehova akhala akulalikira ku New Zealand kwa zaka pafupifupi 120. Amaphunzitsa anthu Baibulo m’zinenero pafupifupi 19 kuphatikizapo zinenero za ku Polynesia ngati Chinuweya, Chirarotonga, Chisamowa ndi Chitongani.